Tanthauzo la Nyawu
WODULA MITENGO AKUPITA PAMTENGO WINA MU NKHALANGO YA MU CENTRAL AFRICA, NKHWANGWA ILI M’MANJA. CHOLINGA CHAKE NCHA CHIPEMBEDZO, CHIMENE CHACHITIDWA NTHAŴI ZAMBIRIMBIRI MU AFIRIKA KWA ZAKA ZOCHULUKA.
WODULA mitengoyo anayamba wafikira waula asanapite mu nkhalangomo. Ndiyeno anachita mwambo wa kudziyeretsa ndi kupereka nsembe ku mzimu wa mtengowo.
Akukhapa mtengowo ndi nkhwangwa yake. Akuvumata ndi milomo yake pokhapidwapo, ndiyeno akuyamwa madzi ake kuti ayanjane ndi mtengowo. Atagwetsa mtengowo, akuusiya pansipo kwa masiku angapo kuti apereke nthaŵi yokwanira kwa mzimu wake ya kupeza malo ena kwina. Iye akukhulupirira kuti mtengowo uli ndi mphamvu yakeyake, ngakhale kuti mzimuwo wachoka. Nyonga ya mtengowo njaikulu kwambiri kwakuti awo amene amagwiritsira ntchito mtengowo ayenera kutsatira mosamalitsa mwambo wake, kuti adzitetezere.
Kwa mmisiri wosema ziboliboli, mtengowo ukukhala nyawu (mask). Popanga nyawuyo, amati mtengowo umapeza mphamvu zowonjezereka. Wosemayo alibe ufulu wa kungopanga chinthu chilichonse chimene akufuna; ayenera kutsatira mpangidwe wamwambo wa nyawu ya fukolo. Ngati satero, ndiye kuti fuko lake lingamkane ndipo mzimu wamphamvu wa nyawuyo ungamkwiyire.
Pamene nyawuyo imalizidwa, sing’anga amachita mwambo wopatulikitsa pamene amadzoza nyawuyo ndi mankhwala amatsenga. Tsopano nyawuyo imalingaliridwa kukhala ndi mphamvu zachilendo zazikulu kwambiri ndi kukhala malo a mzimu umene yapatuliridwako. Ndiyeno nyawuyo imakhala yokonzeka kugwiritsiridwa ntchito m’madzoma achipembedzo.
Tanthauzo la Nyawu mu Afirika
Nyawu zimagwiritsiridwa ntchito pa kulambira m’mbali yaikulu ya kontinenti ya Afirika. Buku lakuti Masks—Their Meaning and Function likuti: “Nyawu ingakhale ndi ntchito ziŵiri: ingagwiritsiridwe ntchito monga chithumwa, monga mmene zilili ndi kachinyawu; kapena ingavalidwe, pamene ntchito yake imakhala yopembedzera makolo, mizimu ina.”
Pofotokoza mwatsatanetsatane, katswiri wina Geoffrey Parrinder akuti m’buku lake lakuti Religion in Africa: “[Nyawu za mtengo za mu Afirika] nzachipembedzo, kaya zikhale zopangidwa mwaluso, zachipembedzo, kapena zosaoneka bwino. Zimaimira akufa kapena mizimu yotumikira pamadzoma awo, kapena ‘m’magulu achinsinsi’ ochita ndi akufa kapena ochotsa mfiti m’midzi. Kaya zikhale za nkhope yabwino kapena yowopsa, yopotoka kapena yosaoneka bwino, nyawuzo zimasonyeza mwamphamvu kuwopsa kwa akufa ndiponso za chikhulupiriro chakuti imfa siili mapeto. Zimapangidwa kuti zivalidwe ndi anthu amene amayerekezera akufa, kaŵirikaŵiri matupi awo ataphimbidwa ndi zovala za nyawuzo, ndipo sayenera kutchedwa kuti anthu koma mizimu.”
Kuwonjezera pa kugwiritsiridwa ntchito kwake pamiyambo ya maliro ndi potetezera matsenga, nyawu nzofunika kwambiri pamalangizo a miyambo, pamapwando, pamilandu, pamiyambo ya kubala, ndiponso “kulankhulana ndi akufa.” Nthaŵi zina nyawu zimagwiritsiridwa ntchito m’zikondwerero ndi m’madzoma a Dziko Lachikristu. Mwachitsanzo, ku Sierra Leone, “adyerekezi” ovala nyawu amavina m’bwalo la tchalitchi posonyeza ulemu pa maukwati. M’ntchito zonsezi, nyawu zili ndi tanthuzo lalikulu limodzimodzilo. Izo zili, likutero buku lakuti African Masks, “zotengera za mphamvu zaumulungu, kaya ntchito yake ikhale yaikulu, kapena yochepa ndi yongosangalatsa anthu.”
Pakati pa mafuko oposa 1,000 a mu Afirika, pafupifupi 100 amapanga nyawu. Nyawu zimasiyanasiyana kwambiri mu mpangidwe pakati pa mafuko, ndipo zimasiyana malinga ndi chifuno chake. Komabe, ngakhale kuti pali kusiyanasiyana kumeneku, pali njira zoikidwa zimene mafukowo amadziŵa bwino m’madera aakulu a mu Afirika. Mwachitsanzo, nyawu zosonyeza mizimu ya makolo kwenikweni zili ndi nkhope yabata, pamene kuli kwakuti nyawu zoimira mizimu ina kaŵirikaŵiri zili ndi nkhope yosaoneka bwino. Mphumi yaitali yobulungika imaimira nzeru ndi mkhalidwe wauzimu wakuya. Maso otuzuka kapena nkhope yokhwinyata imasonyeza mkhalidwe wa kugwidwa ndi mzimu. Utoto woyera umaimira mizimu ya akufa ndi mkhalidwe wa ‘dziko la mizimu.’ Nyawu zokhala ndi nyanga za nyama, makamaka njati ya mu Afirika ndi mphoyo, zili za madzoma a kuchotsa ziŵanda, kusamuka kwa mzimu, ndi ufiti.
Nyawu pa Ntchito
Mu Afirika, nyawu sizimangopachikidwa pa khoma; zimagwiritsiridwa ntchito m’madzoma ndi m’magule. Mwina zimaphimba nkhope ya munthu woivalayo kapena mutu wonse. Munthuyo amavala zovala zazitali m’thupi kapena dzibiya za makhwatha akanjedza kapena nkhwende.
Wovalayo amalingaliridwa kuti akuyanjana mwachindunji ndi mzimu wa nyawuyo. The New Encyclopædia Britannica ikufotokoza zimene zimachitika: “Nthaŵi zina wovalayo, atavala nyawu maganizo ake amasintha ndipo monga momwe zimakhalira ndi kugwidwa ndi mzimu amachita mogwirizana ndi mzimu wosonyezedwa ndi nyawuyo. Komabe, kaŵirikaŵiri, wovalayo mwaluso amakhala ‘bwenzi’ la munthu amene akuyerekezerayo . . . Koma kumaoneka ngati kuti wovalayo kaŵirikaŵiri amakhala wogwirizana kotheratu ndi munthu amene akuyesayesa kumsonyeza. Amasintha umunthu wake ndipo amakhala ngati chidole chosadziŵa chimene chikuchita, chimene chili ngati kapolo wa munthu wosonyezedwa ndi nyawuyo.”
Kwa oonerera ololedwa—amene nthaŵi zambiri amakhala amuna chabe—nyawuyo simangoimira munthu wauzimu. Amakhulupirira kuti munthu wina wamoyo wauzimu amakhala m’nyawuyo. Motero, nyawu yeniyeniyo ili yopatulika, ndipo munthu aliyense wakuswa malamulo amalangidwa mwamphamvu ndi anthu, nthaŵi zina amaphedwa. Kuti adzitetezere, wovalayo, mofanana ndi wodula mitengo ndi wosema ziboliboli, ayenera kutsatira mwambo wake.
Tanthauzo la Nyawu kwa Wosunga Zinthu Zakale
Makamaka m’zaka 100 zapitazo, nyawu za mu Afirika zasungidwa ndi anthu achidwi padziko lonse. Kwa wosunga zinthu zakale nyawu zimatanthauza kanthu kena kosiyana kwambiri ndi tanthauzo la aja amene amachita chipembedzo cha mwambo mu Afirika.
M’malo mwa kuiona monga yopatulika, chinthu chopembedzedwa, osunga zinthu zakale amaona nyawu monga ntchito yaumisiri yosonyeza mwambo wa mu Afirika. M’malo mwa kuona nyawu malinga ndi ntchito yake m’chitaganya, iwo amaŵerengera nyawuyo chifukwa cha kukonzedwa bwino kwake, kulimba, ndi mmene imachititsira chidwi. Osunga zinthu zakale amafunsa kuti: Kodi wosema ziboliboliyo amaona motani mtengo wake, nyama yake, masemedwe ake? Kodi wosemayo amagwiritsira ntchito motani luso lake ndi nzeru zake komabe nagwiritsira ntchito njira yoikidwa ndi mwambo wake?
Zoonadi, wosunga zinthu zakale samanyalanyaza malo achipembedzo mu ubwino wa ntchitoyo. Kaŵirikaŵiri, chifukwa cha kusiyana kwa malingaliro a osemawo, pamakhala kusiyana kwakukulu pakati pa nyawu zimene zimagwiritsiridwa ntchito m’kulambira ndi zija zosemedwa kaamba ka alendo akumaiko ena. Buku lakuti Masks of Black Africa likuti: “Wosemayo . . . anasonkhezeredwa ndi chikhulupiriro chakuya, kuchitira ulemu kwake cholinga chake cha kutulutsa mzimu wamphamvuyonse, ndipo, pokhala ndi malo ameneŵa, anatero kuti akwaniritse thayo lake lapadera mu fukolo. Pamene chikhulupiriro cha chipembedzo chimenechi . . . chinazirala, ntchito yakeyo, ngakhale ngati anaichita mwaluso, inakhala yakufa ndiponso yotsika.”
Awo amene amasunga nyawu m’myuziyamu kaŵirikaŵiri amapenda mosamalitsa ntchito imene nyawuyo yachita m’fuko limene ikuchokera kuposa amene amasunga zinthu zakale zaumisiri zawamba. Komabe, chidziŵitso chachindunji chotero kaŵirikaŵiri sichipezeka chifukwa cha njira imene nyawu zambiri zapezedwera m’zaka zapitazo. Zina zinasonkhanitsidwa monga zikumbukiro, zina zinali zina za zinthu zofunkhidwa mu nkhondo, ndiponso zina zinasonkhanitsidwa zochuluka kaamba ka malonda. Chotero, tanthauzo loyambirira ndi ntchito ya nyawu iliyonse kaŵirikaŵiri sizimadziŵika bwino.
Tanthauzo la Nyawu kwa Akristu
Motero, nyawu zili ndi tanthauzo lina kwa awo amene amalondola chipembedzo chamwambo ndipo lilinso ndi tanthauzo lina kwa awo amene amazisunga monga zinthu zaumisiri ndi zamwambo. Kwa Akristu, zili ndi tanthauzo linanso.
Baibulo limafotokoza momvekera bwino kuti m’nyawu kapena mtengo umene yasemedwako mulibe mphamvu ya mizimu. Mneneri Yesaya akufotokoza kupusa kwa munthu amene amagwiritsira ntchito mbali ina ya mtengowo kuphikira chakudya chake ndi kuwotha moto wake ndiyeno nasema mbali ina yotsalayo kukhala mulungu amene amampempha thandizo. (Yesaya 44:9-20) Mfundo yofananayo imagwira ntchito pa nyawu zachipembedzo.
Komabe, Akristu amazindikira kuti pali “magulu a mizimu yoipa kumiyamba.” (Aefeso 6:12, NW) Pansi pa ulamuliro wa Satana, amasokeretsa anthu ndi chipembedzo chonyenga.—Chivumbulutso 12:9.
Akristu amadziŵanso kuti ziŵanda zimagwiritsira ntchito zinthu zina kulankhulana ndi anthu. Motero, atumiki a Mulungu samasunga kanthu kalikonse kamene kali kogwirizana ndi chipembedzo cha mizimu, kaya likhale zango, chithumwa, kapena khoza lamatsenga, kapena nyawu. Potero amatsatira njira ya Akristu oyambirira a ku Efeso. Ponena za iwo Baibulo limati: “Ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anaŵerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.”—Machitidwe 19:19.
Awo amene afuna kutumikira Yehova samagwiritsira ntchito nyawu kapena kuzisunga kapena kanthu kena kalikonse kogwirizana ndi kulambira konyenga. Ndemanga ya Pius, mkulu Wachikristu ku Nigeria ndi yoona: “Nyawu zimasonyeza maganizo achipembedzo a awo amene amazigwiritsira ntchito. Nyawu zili ndi maina ndipo zimalemekezedwa kapena kuwopedwa modalira ndi mulungu amene zikuimira. Sindingaike nyawu m’nyumba mwanga chifukwa chakuti zimenezi sizingakondweretse Yehova ndiponso chifukwa chakuti alendo angalingalire kuti ndimagwirizana ndi zikhulupiriro za chipembedzo chimene zimaimira.”
Akristu oona amadziŵa kuti lamulo la Mulungu lomveka loperekedwa kwa Israyeli linali lakuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje.”—Eksodo 20:4, 5.
[Bokosi patsamba 24]
Nyawu m’Mafuko Ambiri
Kodi liwu lakuti “nyawu” limatanthauzanji kwa inu? M’mafuko ena liwulo ndi lophiphiritsira kutanthauza kubisa kanthu kena. Ngati mumakonda maseŵero, mungaganize za nyawu kukhala chinthu china chotetezera kuvulala kumaso, monga ngati mu baseball ndi fencing. Mwinamwake mukuganiza za mask ya gasi, mask ya opaleshoni, kapena mask ya paphwando.
Komabe, kwa anthu ambiri lerolino, nyawu zimatanthauza chipembedzo. The New Encyclopædia Britannica imati: “Nyawu zoimira mizimu yopatulika kapena yoyera yabwino ndi yoipa m’magule achipembedzo—makamaka mu akachisi Achibuda a ku Nepal, Tibet, ndi Japan ndi m’mafuko aakulu a anthu akumidzi—zimapanga [ka]gulu koimira milungu yopatulika. Kaŵirikaŵiri zimalambiridwa monga mmene mafano amalambiridwira.”
Nyawu zachipembedzo zimapezeka m’mafuko onse ndipo zili zakale kwambiri. Mwinamwake kwa makolo athu zinali ndi mbali yofunika m’moyo wachipembedzo ndi wa fuko. Buku lakuti Masks—Their Meaning and Function likuti: “Poyamba, nyawu iliyonse inali ndi tanthauzo koposa, ndipo nyawu yeniyeniyo kapena munthu woivala mwanjira yosadziŵika bwino anaimira mphamvu inayake kapena mzimu.”