1945-1995—Kodi Zakhala Zaka 50 za Kupita Patsogolo?
KODI mwaona kuwongolera zinthu kwina m’moyo wanu m’zaka 50 zapitazi?a Lingalirani za mankhwala. M’maiko ena, monga Britain, Canada, Cuba, ndi Sweden, kuyamba kuthandiza osauka kwa aboma, ndi njira zake za mankhwala zothandiza anthu, kunapereka chitsimikiziro chakuti mosasamala kanthu za mkhalidwe wa ndalama wa wodwala, madokotala ndi zipatala zidzakhala zokonzekera kuthandiza onse.
Ngakhale maiko ena osatukuka akhoza kuwongolera miyezo yaumoyo ya nzika zawo. JAMA (The Journal of the American Medical Association) inavomereza kuti “maunduna azaumoyo a maiko ena osatukuka akhoza kupereka thandizo lamankhwala ofunika kwa onse pamtengo umene anthu a m’maiko awo angathe kulipirira. . . . Kupita patsogolo kwapadera kwachitidwa pochepetsa imfa zamakanda ndi ana ku China, Costa Rica, Sri Lanka, ndi ku chigawo cha Kerala ku India.”
Kuwongokera m’Zachuma
Poyerekezera ndi mkhalidwe wa chuma mu 1945, anthu ambiri ali mu mkhalidwe wabwino kwambiri wakuthupi mu 1995. Ambiri amene zaka 50 zapitazo sakanatha kugula zinthu zokwera mtengo tsopano ali ndi galimoto, ma TV, ma VCR, makina a CD, mafiriji, mafoni a m’thumba, ndi zinthu zina za moyo wamakono. Mwinamwake inu ndinu mmodzi wa anthu ambiri amenewo.
Zili monga momwe olemba mpambo wa buku lakuti A History of Private Life akufotokozera kuti, “kwa zaka makumi atatu pambuyo pa Nkhondo Yadziko II France [limodzi ndi maiko ena a kumadzulo kwa Ulaya] anatukuka m’chuma pang’onopang’ono, kumene, ngakhale kuti sikunathetse kusiyana kwa magulu a anthu, kunadzetsa kulemerera kwa magulu onse a anthu. Pokhala ndi nyumba ‘yabwinopo’ galimoto ‘yabwinopo,’ ndi wailesi yakanema, pamodzi ndi thandizo lina la boma ndi mankhwala amakono, aliyense anatha kukhala ndi moyo wabwinopo, ngati zitalephera kukhala monga paradaiso wa pa dziko lapansi.”
Komabe, funso nlakuti, Kodi kukhala ndi zinthu zambiri zakuthupi kumatanthauza kuti anthu ali opeza bwino kwambiri? Kodi kuchuluka kwa mapindu a kuthupi kumatanthauza kuti moyo uli bwino kwambiri kapena uli wotetezereka bwinopo? Kukhala ndi chuma chambiri kwa ena kumasiya anthu ambiri akali osauka. Zimenezo zimachititsa kuwonjezereka kwa kufuna kuba kwa anthu, kulanda, chinyengo, ndi upandu wina wambiri wachiwawa kwambiri. Ena a anthu osauka amatsimikiza kupeza chuma—mwalamulo kapena mopanda lamulo. Mwachitsanzo, mu New York City, galimoto zoposa 100,000 zimabedwa chaka chilichonse. Mapindu achuma chakuthupi samapereka chitetezo chotsimikizirika kwambiri pa moyo.
Mbali zina zawongoleredwa, ngakhale kuti si monga momwe ena anafunira.
Akazi—Kale Ndiponso Tsopano Lino
Nkhondo Yadziko II inapereka chisonkhezero chatsopano kwa akazi ena. Ambiri anali atazoloŵera kukhala anakubala ndi akazi apanyumba, pamene mwamuna anali wopezera zosoŵa zabanja. Nkhondo yadziko yachiŵiri inasintha zonsezo. Amuna anatumizidwa kunkhondo, ndipo mwadzidzidzi akazi anali kugwira ntchito m’mafakitale azida zankhondo kapena m’ntchito zina zimene zinali za amuna. Posachedwapa, ena aloŵa m’magulu ankhondo ndipo aphunzira kupha. Akazi ambiri analandira malipiro ndipo anaona moyo watsopano wokhala ndi ufulu wake wachuma. Uwu unali mng’alu waung’ono umene potsirizira unatsegulira khomo la “mkazi womasulidwa” wamakono. M’nkhondo ya kufuna kufanana ndi amuna, akazi ena amanena kuti akazi akali kutalibe kwambiri m’maiko ambiri. Amanena kuti pali “chopinga” chimene chimadodometsa kukwezedwa kwawo m’ntchito zambiri.
Kusamuka kwa Unyinji Kudzetsa Mavuto
Kusintha kwina kwakukulu m’zaka 50 zapitazo ndiko kuchoka m’midzi ndi kuleka ulimi kwa anthu poyesayesa kupeza moyo wabwinopo m’mizinda. Kwa ena zimenezi zachitikadi. Koma kodi nchiyani chimene chachitikira enawo?
Chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambiri amasamukira m’mizinda yokhala ndi anthu ochulukitsitsa kale, mmene muli nyumba zochepa ndi zokwera mtengo. Kodi nchiyani chimene chimachitika? Zithando zimene zimakhala malo obukirako matenda, upandu, ndi chiwawa chandale. Zisimba zodzipangira zimenezi, zopangidwa ndi makhadibodi, matabwa, kapena malata otayidwa, ndizo makumbi, ma barraca, kapena ma chabola (Chispanya), amene amakhalamo anthu osauka ndi oponderezedwa a m’dzikoli. Zithando zimenezi— ma favela m’Chipwitikizi, ndi ma gecekondu m’Chitheki (kutanthauza “chomangidwa usiku”)—ndizo moyo wa anthu ena amene sanganyalanyazidwe, kaya ndi mu Afirika, India, South America, kapena kwina kulikonse.
Zimene Zilipo ndi Zimene Zili Mtsogolo mwa Maiko Ena a mu Afirika
Kodi munthu anganenenji za Afirika? Madokotala ena aŵiri analemba mutu wa nkhani yawo wakuti “Afirika pa Mphembenu—Chenjezo la Tsoka Koma Osati Lopanda Chiyembekezo cha Mtsogolo” mu JAMA. Anavomereza kuti mikhalidwe ya ndale ndi anthu kumbali yaikulu ya Afirika ili ndi mavuto angozi. Analemba kuti: “Mbali ya kumunsi kwa Sahara ya Afirika [dera la maiko 45], zaka zake 20 zapitazo zakhala zatsoka. Chigawocho chakanthidwa ndi njala, chilala, nkhondo zachiŵeniŵeni, chinyengo chandale, AIDS, kukula kofulumira kwa chiŵerengero cha anthu, kuchepa kwa chakudya cholimidwa, kuguga kwa nthaka . . . Akatswiri akuvomerezana pa kuneneratu kwakuti kutsika kwina kwa chuma, umphaŵi, ndi mavuto zidzachitikadi, kwakanthaŵi.” Nkhani imodzimodziyo ikusimba kuti maiko 32 mwa 40 osauka kwambiri a padziko ali kumunsi kwa Sahara wa Afirika.
Nangano bwanji za makhalidwe amene alipo m’dziko? Nkhani yotsatira idzafotokoza mwachidule “kupita patsogolo” kwa dziko pa mbali imeneyi.
[Mawu a M’munsi]
a Chifukwa cha kuchepa kwa malo, nkhani yathu sikufotokoza mbali zonse za kupita patsogolo kapena kusintha m’theka lothera la zaka zana.
[Mawu a Chithunzi patsamba 6]
Chithunzi cha USAF
[Mawu a Chithunzi patsamba 7]
Chithunzi cha NASA