Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 9/8 tsamba 15-16
  • Mbali Yanu m’Mapemphero Anu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbali Yanu m’Mapemphero Anu
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingathandizire Motani?
  • Chitanipo Kanthu!
  • Yehova Amachita Mbali Yake
  • Zimene Zili Mʼbuku la 2 Samueli
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Kodi Mulungu Amamvetsera Pamene Mupemphera?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Tizitsanzira Atumiki a Yehova Amene Anali Okhulupirika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Anthu Amene Amakhulupirira Yehova Amakhala Olimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 9/8 tsamba 15-16

Lingaliro la Baibulo

Mbali Yanu m’Mapemphero Anu

ILI kumbali kwa phiri itayang’anizana ndi mzinda, mfumu yakuda nkhaŵayo iima kaye kusinkhasinkha za nyumba yake yachifumu yaulemerero, mzinda waukuluwo, ndi tsoka logwera banja lake. Gulu la nkhondo lalikulu lasonkhana kummwera ndipo tsopano likulinga kumzindawo. Nduna za boma zapanduka, ndipo unyinji wa anthu akuchirikiza apanduwo. Mfumuyo pokhala yachisoni, ipemphera kwa Mulungu. Monga munthu wopembedza wodzipereka, chidaliro chake chakuti Mulungu adzamva pempho lake ndi kulepheretsa zolinga za ochita chiŵembuwo. Ndiyeno, akumafulatira mzinda waulemererowo, atsika paphiripo napitiriza kulinga kumpoto kuchipululu chimene chili kutsidya la mtsinje. Kodi angachitenso chiyani? Nkhaniyo tsopano ili m’manja mwa Mulungu.

Momwemonso, anthu odzichepetsa okhulupirira lerolino amatembenukira kwa Mulungu m’pemphero panthaŵi ya mavuto ali ndi chitsimikizo chotonthoza chakuti kuwonjezera pa kupereka zitsogozo zomveka za mmene angapempherere, Baibulo limasonyeza kuti Yehova Mulungu ndiye “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Ndife otsimikiza kuti onse ofuna Mulungu moona mtima iye adzawamva.

Komabe, kodi chikhulupiriro ndi pemphero zili zokwanira? Kodi tili ndi mbali yotani pa mayankho a mapemphero athu?

Kodi Tingathandizire Motani?

Mfumu yotchulidwa poyambayo inali Mfumu Davide ya Israyeli wakale. Atayang’anizana ndi chiŵembu cha Abisalomu mwana wake wopanduka ndi phungu wake wonyenga Ahitofeli, iye anasankha kuthaŵa ku Yerusalemu ndi kukabisala mumzinda wamalinga wa Mahanaimu kuchipululu kummaŵa kwa mtsinje wa Yordano. Mwachionekere pokhala wokhumudwa, wopsinjika mtima, ndi wakuda nkhaŵa kwambiri, anachonderera Yehova m’pemphero, akumati: “Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofeli ukhale wopusa.” (2 Samueli 15:11-15, 30, 31) Komabe, Davide anachita zambiri kuposa kungopemphera chabe. Anayesayesa kwambiri kuti pemphero lake liyankhidwe. Motani?

Iye anayamba kale kwambiri kuyesayesa kumeneko zisanayambe ziyeso zomwe anayang’anizana nazo. Pazaka zambiri, ngakhale asanakhale mfumu, Davide anasonyeza kuti anali mlambiri wokhulupirika wa Yehova. (1 Samueli 16:12, 13; Machitidwe 13:22) Anafika pa kukonda Mulungu. Chotero, poyesedwa Davide anali ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzamva pemphero lake ndi kuyankha mwa njira yoyenera.

Ndi mmenenso zilili lerolino. Kaŵirikaŵiri njira yaikulu yothandizira mayankho a mapemphero athu ndiyo kutsatira uphungu wa Baibulo monga njira ya moyo nthaŵi zonse. Kutsatira mokhulupirika zitsogozo zimene Mulungu watipatsa koteroko kumatichititsa kukhala mabwenzi ake apamtima. Kuyandikana ndi Mulungu kumeneku ndi chikhulupiriro chotero ziyenera kukhalapo ziyeso zisanayambe. Ziyenera kukhala ngati maziko olimba pamene pamamangidwa nyumba; iwo ayenera kukhalapo nyumbayo isanamangidwe. Motero tikhoza—ngakhale tsopano, ziyeso zisanayambe—kuthandizira kuti mapemphero athu ambiri aziyankhidwa.

Chitanipo Kanthu!

Ngakhale kuti ubwenzi wa Davide ndi Mulungu unakhala wothandiza kwambiri, iye anazindikiranso kuti sakanangoyembekezera yankho la pemphero lake popanda kuchitapo kanthu. Mosiyana ndi zimenezo, Davide anachitapo kanthu monga momwe ikusonyezera njira yanzeru imene anaitenga pambuyo pa pemphero lake.

Pakati pa mabwenzi okhulupirika a Davide panali Mwaariki wina wotchedwa Husai. Husai anakumana ndi mfumu yothaŵayo pa phiri la Azitona. Ngakhale kuti anafuna kuthaŵa pamodzi ndi Davide, Husai anamvera pamene Davide anamchonderera kukhala mumzinda. Anayenera kunamizira kuti anali kumbali ya Abisalomu, kotero kuti ayese kulepheretsa uphungu wa Ahitofeli phungu wachiŵembu, ndi kuti azidziŵitsa Davide zochitika. (2 Samueli 15:32-37) Malinga ndi zimene anayembekezera, Husai anakhoza kuchititsa Abisalomu kumdalira. Tsopano Yehova anayenera kuloŵererapo.

Ahitofeli waluntha koma wachinyengo anafotokoza njira yabwino koposa imene analingalira. Anauza Abisalomu kumpatsa amuna 12,000 kuti akaukire Davide usiku womwewo pamene anali kuthaŵa, ali wosakonzeka ndi wosatetezereka—kupha kumene kukanachititsa chipandukocho kupambana! Komabe, zimene ambiri anadabwa nazo zinali zakuti Abisalomu anapempha uphungu kwa Husai pankhaniyi. Iye anauza Abisalomu kuima kaye ndi kusonkhanitsa khamu lamphamvu la amuna, otsogozedwa ndi Abisalomu mwiniyo osati wina aliyense. Mwa mphamvu ya Yehova, analandira uphungu wa Husai. Mwachionekere, Ahitofeli atazindikira kuti mwa kutsatira uphungu wa Husai iwo adzagonjetsedwadi, anabwerera kwawo nadzipha.—2 Samueli 17:1-14, 23.

Panalibe kukayikira kuti Yehova anayankha pemphero la Davide—monga momwedi anapempherera. Chitsanzo cha Davide cha kuchita monga mwa pemphero lake chili ndi phunziro labwino koposa kwa onse ofuna thandizo kwa Mulungu mwa pemphero.

Yehova Amachita Mbali Yake

Zoona, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupempha chakudya chawo cha tsiku ndi tsiku nawalonjeza kuti ngati aika zinthu za Mulungu poyamba, Iye adzasamalira zofuna zawo. (Mateyu 6:11, 33) Mwachitsanzo, ngati munthu ndi lova, ayenera kuchita monga mwa pemphero lake lofuna chakudya mwa kuchita zonse zotheka kuti apeze ntchito kapena kudzipangira ntchito.

Pachilichonse chimene tichitchula m’mapemphero athu, kukhoza kwathu kuthandizira yankho lake kumasiyanasiyana kwambiri. Nthaŵi zina tingachite zochuluka ndipo nthaŵi zina tingachite zochepa, ngati tingatero nkomwe. Chofunika sindicho zimene tikhoza kuchita ndi zimene sitikhoza koma kuchita zonse zimene tingathe.

Tili otsimikiza kuti Yehova amadziŵa mikhalidwe yathu ndi maluso athu. Amadziŵa bwino zimene titha kuchita, ndipo sangafune konse kuti tichite zoposa zimene tingachite. Kaya tingachite zochuluka kapena zochepa, Yehova adzakwaniritsa mosoŵamo. Amayamikira ndipo amachirikiza zoyesayesa zathu ndiponso amachita mogwirizana nazo kuti apereke yankho labwino koposa kwa onse okhudzidwa.—Salmo 3:3-7.

Ali mkati mwa mavuto, Mfumu Davide anakhoza kulankhula ndi chidaliro kuti: “Chipulumutso ncha Yehova; dalitso lanu likhale pa anthu anu.” (Salmo 3:8) Chidaliro chathu m’mphamvu ya Yehova limodzi ndi kuchita kwathu mbali yothandizira, yaikulu kapena yaing’ono, zichititsetu mapemphero athu kuyankhidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena