Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 9/8 tsamba 17
  • Liwu Lomvekapo Lokha Pamene Kuli Chete

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Liwu Lomvekapo Lokha Pamene Kuli Chete
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kuvumbula Zoipa za Nazi
    Galamukani!—1995
  • Kodi Kupulula Anthu Kungadzachitikenso?
    Galamukani!—2001
  • Pali “Nthawi Yokhala Chete”
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Chimene Matchalitchi Anakhalira Chete
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 9/8 tsamba 17

Liwu Lomvekapo Lokha Pamene Kuli Chete

ZAKA 50 kalelo chilombo chinaphedwa. Pamene dziko linatsegula chochinga kuti anthu aone bwinja la Ulamuliro wa Nazi wakugwawo, kunali kovuta kukhulupirira zodabwitsa zimene zinaoneka. Asilikali ndi anthu wamba omwe anangogwira pakamwa ndi kudabwa mwamantha poona mabwinja a chilombo chakupha anthucho.

Kumayambiriro kwa chaka chino anthu zikwi zambiri anakondwerera chaka cha 50 cha kumasuka ku misasa yachibalo mwa kuguba mwakachetechete m’mabwinja ake. Anayesa kulingalira za kukula kwake kwa upanduwo. Ndithudi, anthu 1,500,000 anaphedwa m’ndende yophera anthu ya ku Auschwitz yokha! Inali nthaŵi yokhala chete, nthaŵi yolingalira za nkhanza ya munthu kwa munthu mnzake. Kunali kopatsa mafunso ovutitsa maganizo kuona mauvuni owotcheramo anthu opanda moto, malo a misasa ya asilikali yopanda anthu, miyulu ya nsapato zolandidwa.

Lerolino anthu akuchita kakasi; ali okalipa. Chipululutso cha Nazi, chimene chinanyonga mamiliyoni a anthu m’magulumagulu, chimasonyeza uchiŵanda umene Chinazi chinali nawo. Koma kodi zinali motani panthaŵiyo? Kodi amene analankhula mopanda mantha ndani? Kodi amene sanatero ndani?

Kwa anthu ambiri, nthaŵi yoyamba imene anamva za kuphedwa kwa anthu ochuluka inali kumapeto kwa Nkhondo Yadziko II. Buku lakuti Fifty Years Ago—Revolt Amid the Darkness limafotokoza kuti: “Zithunzithunzi ndi mafilimu osonyeza malo ndi ndende zopherako anthu zimene maiko omenyana ndi Germany anatsegula kumasula andende mu 1944 ndi 1945 poyamba zinadabwitsa kwambiri anthu, makamaka m’maiko akumadzulo.”

Komabe, ngakhale pamene ndende zopheramo anthu zinali zisanamangidwe, panali liwu limene linali kulengeza zowopsa za Chinazi kupyolera mwa Galamukani! magazini amene tsopano lino muli nawo kumanja. Poyamba ankatchedwa The Golden Age ndiyeno anadzatchedwanso Consolation mu 1937. Kuyambira mu 1929, magaziniwa, ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, anachenjeza mopanda mantha za masoka a Chinazi, mogwirizana ndi uthenga umene unali pachikuto chake, “Magazini a Choona, Chiyembekezo ndi Kulimba Mtima.”

“Kodi munthu angakhale chete bwanji,” inafunsa motero Consolation mu 1939, “ponena za zochitika zowopsa za dziko monga Germany, kumene anthu opanda chifukwa 40,000 anamangidwa panthaŵi imodzi; kumene 70 a iwo ananyongedwa usiku umodzi m’ndende imodzi yokha; . . . kumene nyumba zonse, sukulu ndi zipatala za achikulire, amphaŵi, ndi opunduka, ndiponso nyumba za ana amasiye zonse zinawonongedwa?”

Ndithudi, ndimotani mmene munthu angakhalire chete? Pamene dziko lonse silinadziŵe kapena linali lokayikira za malipoti owopsa otuluka m’Germany ndi maiko amene anawalanda, Mboni za Yehova sizinathe kukhala chete. Zinadziŵa bwino lomwe nkhanza za boma la Nazi, ndipo zinalankhula mopanda mantha.

[Mawu a Chithunzi patsamba 17]

Chithunzi cha National Archives ya ku United States

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena