1995 Bwanji Nanga za Mtsogolo Mwathu?
“Dziko lifunikira chitsogozo chabwinopo kuposa kupempha anthu kulandira demokrase ndi kugulitsana malonda mwaufulu—komano palibe chilichonse.”—Will Hutton, Guardian Weekly.
PA LINGALIRO la munthu, mawu amenewo angakhale ngati oona. Dziko likuonekera kukhala lili losoŵa chitsogozo chodalirika choloza kumene kuli mtendere, chisungiko, chilungamo, kusakondera, ndi boma labwino. Munthu wayesa pafupifupi mtundu uliwonse wa boma, kuyambira pa maufumu kufikira ku malipabuliki, kuyambira pa maulamuliro opondereza kufikira ku mademokrase, ndipo akungopezabe kuti dziko lake nlosalamulirika. Nangano kodi ayenera kutembenukira kuti?
Pali chosankha—njira yopita ku dziko lachiwawa chambiri, upandu, chinyengo, chisalungamo, kusakhulupirika kwa achipembedzo ndi andale, udani wa utundu, kulima pamsana osauka. Imeneyo ndi njira imene ena amanena kuti ikupita ku kusalamulirika kwa zinthu.
Ndiyeno pali njira ina yovuta, yodzimana yopita ku dziko labwino kwambiri lozikidwa pa yankho la Mulungu la boma, lopezeka m’Baibulo. Njovuta chifukwa chakuti imafuna kulimba mtima, kudzimana, lingaliro lauzimu pa moyo, ndi kukhulupirira Mulungu wachifuno. Koma kuti munthu athe kuyendamo ayeneranso kukhala wodzichepetsa—wodzichepetsa pamaso pa Mlengi wake. Ayenera kutembenukira kwa Mulungu kaamba ka ulamuliro wolungama. Mtumwi Wachikristu Petro analangiza kuti: “Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa iye nkhaŵa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.”—1 Petro 5:6, 7; Chivumbulutso 4:11.
Kodi Ndani Amene Amasonkhezera Udani?
Munthu mwa iye yekha sangasinthe dzikoli kuti likhale labwino—anthu adyera oipa ali ambiri ndi amphamvu kwambiri. Mneneri Yeremiya analondola pamene analemba kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Munthu sangalongosole bwino mapazi ake mopindulitsa banja lonse la munthu, popanda Mulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kuwonjezera pa kupanda ungwiro kwathu kwa choloŵa nthaŵi zonse pamakhala mdani wosaoneka uja, Satana, amene ali wokonzekera kusonkhezera udani, monga momwe anachitira ku Rwanda, kusonkhezera anthu kuphana.—Genesis 8:21; Mateyu 4:1-11.
Kuti asonkhezere kukondera, udani, ndi mbanda m’mitima ya anthu ndi m’maganizo, Satana waloŵetsa m’mitundu ya anthu malingaliro a kukonda mtundu wamunthuwe, fuko, ndi chipembedzo. Maphunziro a udani ozika mizu kwambiri ameneŵa amayambidwa paukhanda ndi makolo amene maganizo awo ali opotokera pamkhalidwewo, kaŵirikaŵiri chifukwa cha mwambo wa zaka zambiri. Ndiyeno mwambo umenewo umachirikizidwa ndi madongosolo a sukulu ndi ziphunzitso zachipembedzo. Motero anthu ambiri amaleredwa ali ndi udani ndi kukondera m’mitima. Amaphunzitsidwa, kuipitsidwa maganizo kuyambira paukhanda, kuti aukire munthu mnzawo pamene asonkhezeredwa ndi atsogoleri opanda makhalidwe andale ndi achipembedzo. Kuchuluka kwa mawu osonkhezera opanda nzeru ndi onyanyula kungabutse moto waukulu, umene umapha anthu mu “kuyeretsa fuko” kapena kupulula anthu.
Posonyeza zimene zingachitike posachedwapa mtsogolo, Martin van Creveld, wolemba mbiri ya nkhondo ku Israel, analemba mu The Transformation of War kuti “Mwa lingaliro lapatali limene lilipo, pakukhala ngati kuti pali chiyembekezo champhamvu chakuti anthu otengeka maganizo ndi . . . chipembedzo adzasonkhezera kwambiri nkhondo” m’maiko a Kumadzulo kuposa nthaŵi ina iliyonse “m’zaka 300 zapitazo.” Motero chipembedzo, m’malo mwa kukhala chochititsa mtendere ndi kutukulira anthu kumkhalidwe wauzimu, chikupitiriza kukhala m’malo ake a m’mbiri osonkhezera udani, mikangano, ndi kupha.
Mtsogolo mwa Mtundu Wina Mulonjezedwa
Ngati anthu ati apeze moyo m’dziko lolungama latsopano, pamenepo ayenera kukhala ndi phande m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesaya wakuti: “Iye [Yehova] adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake. . . . Adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:3, 4.
Kodi ndani lero amene akulabadira ulosi wabwino kwambiri umenewu padziko lonse? Kodi ndani amene anafa ku Rwanda m’malo mwa kupha okhulupirira anzawo a fuko lina? Kodi ndani amene anafera m’misasa yachibalo ya Nazi m’malo mwa kutumikira m’magulu ankhondo a Hitler? Kodi ndani amene asankha kuthera nthaŵi yaitali m’ndende za m’maiko ambiri m’malo mwa kuphunzira nkhondo? Ali awo amene alandira kukwaniritsidwa kwa Yesaya 54:13: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.”
Mboni za Yehova padziko lonse zili ndi mtendere umenewo tsopano lino chifukwa chakuti zalandira chiphunzitso cha Yehova chochokera m’Mawu ake, Baibulo. Zimatsatira ziphunzitso ndi chitsanzo cha Kristu Yesu. Ndipo kodi iye ananenanji? “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) Mboni za Yehova zimasonyeza chikondi chimenechi kwakuti, ngakhale kuti poyamba anali Akatolika ndi Aprotesitanti, tsopano amagwira ntchito momvana pamodzi ku Northern Ireland. Ngakhale kuti kale anali adani chifukwa cha chipembedzo, tsopano ali ogwirizana monga Akristu ku Israel, Lebanon, ndi ku maiko ena. Samaphunziranso nkhondo. Zinthu zikanasintha chotani nanga ngati anthu onse m’dziko akanalabadira mawu a Yesu ndi kuwagwiritsira ntchito m’miyoyo yawo!
Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti dziko latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu lili pafupi, dziko limene lidzalamuliridwa ndi boma lakumwamba. Kodi izo zili ndi maziko otani okhalira ndi chiyembekezo chotsimikizirika chimenecho?
Kuchitapo Kanthu kwa Mulungu Motsimikiza Kolonjezedwako
M’Mawu ake, Baibulo, Mulungu walonjeza za ulamuliro wolungama kwa anthu onse omvera. Kupyolera mwa mneneri wake Danieli, iye analosera kuti m’nthaŵi yamapeto a dongosolo lino, adzakhazikitsa boma lolungama lachikhalire. “Masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Umenewu ndi ulamuliro wa Ufumu umodzimodziwo umene Kristu anaphunzitsa okhulupirira kuupempha mu pemphero lake lotchuka kuti: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.
M’pemphero limenelo timapempha Mulungu kukwaniritsa malonjezo ake onena za ulamuliro wake wolungama. Ndipo timadziŵa kuti Mulungu sanganame. Paulo ananena za “moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthaŵi zosayamba.” (Tito 1:2; Ahebri 6:17, 18) Ndipo kodi Mulungu walonjezanji? Mtumwi Petro akuyankha kuti: “Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:13; Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:1-4.
Ulamuliro wolungamawo usanayambe kugwira ntchito mokwanira pa dziko lapansi pano, ntchito yoyeretsa yaikulu iyenera kuchitidwa. Maulosi a Baibulo mogwirizana amasonyeza kuti ntchito imeneyi ya kuchotsa Satana ndi magulu ake oipa idzachitidwa posachedwapa. (Onani Mateyu, chaputala 24; Luka, chaputala 21; ndi Marko, chaputala 13.) Kuyeretsa komaliza kumeneku kumatchedwa nkhondo ya Armagedo, “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.”—Chivumbulutso 16:14, 16.
Mosasamala kanthu za mmene ambiri angaganizirire, chaka cha 2000 sichili chofunika kwenikweni. Ndi iko komwe, a Dziko Lachikristu okha ndi amene amanena za detilo. Magulu ena ali ndi njira zawo zoŵerengera madeti. Chimene chili chofunika nchakuti tsopano ino ndiyo nthaŵi ya kutembenukira kwa Mulungu ndi ku Mawu ake kuti musonyeze “chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:1, 2) Chimene chili chofunika nchakuti tsopano ndiyo nthaŵi yanu ya kusankha—kaya kuyenda ndi kukapeza mtsogolo modalitsidwa ndi Mulungu kapena kupitiriza kuyenda m’njira yogwiritsa mwala imene dziko la Satana limapereka. Tikukulimbikitsani kusankha njira ya Mulungu. Sankhani moyo!—Deuteronomo 30:15, 16.
[Mawu Otsindika patsamba 14]
“Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano.”—2 Petro 3:13
[Chithunzi patsamba 13]
Mitundu idzasuladi malupanga awo kukhala zolimira kokha mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu