Mabanja a Kholo Limodzi—Mkhalidwe Womakula
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRITAIN
“PALI mabanja ambiri a kholo lokhala lokha ku UK kuposa dziko lina lililonse ku Ulaya,” ikusimba motero The Times ya ku London. “Makolo olera okha ana . . . tsopano amayang’anira banja limodzi lililonse mwa mabanja asanu a ku UK a ana a zaka zosafika 18, poyerekezera ndi banja limodzi mwa mabanja asanu ndi aŵiri a ku Denmark ndi banja limodzi mwa mabanja asanu ndi atatu a ku Germany ndi France.”
Pa makolo khumi alionse olera okha ana ku Britain, asanu ndi anayi ndi akazi. Banja lodziŵika lopangidwa ndi atate ndi amayi limodzi ndi ana awo tsopano lotchedwanso nuclear family, langokhala ngati ‘lingaliro linanso la banja.’ Koma kodi nchifukwa ninji mabanja a kholo limodzi ali ofala kwambiri kuposa kale?
Chisudzulo ndi kupatukana ndizo zoputira zake zazikulu. Pamfundoyi Britain amatsatira United States, amene theka la maukwati ake amathera m’chisudzulo. Ndiponso, zimene anthu amafuna mu ukwati zasintha. Malinga ndi kunena kwa Zelda West-Meads wa Relate, gulu lolangiza m’nkhani za ukwati, zaka 20 kapena 30 zapitazo, “malo a amuna ndi akazi anali odziŵika bwino kwambiri. Mwamuna anali wopezera ndalama banja; mkazi anali wolisamalira.” Komano bwanji lero? “Lerolino maukwati angakhale otsitsimula ndi okondweretsa, komanso angakhale ovuta kwambiri. Akazi akufuna zambiri mu ukwati kuposa zimene amawo ndi agogo awo aakazi anafuna. Akufuna kufanana ndi amuna, mwamuna wabwino wowakonda, bwenzi labwino, ntchito yawo imene angagwire—ndiponso ana.”
Chisembwere chosonyezedwa m’zosangulutsa zonse chimachotsera ulemu banja lodziŵika. Achichepere amene amagonana ndi ena pa usinkhu waung’ono kwambiri kaŵirikaŵiri samadziŵa zotulukapo zake. Kwa iwo ukwati ndi mavuto, umachepetsa ufulu wawo, chopinga chosafunikira m’moyo.
Ena amasankha kukhala kholo lolera ana lokha; ena amakhala otero chifukwa cha mkhalidwe. Pamene amaumirizika kukhala kholo lolera ana lokha, anthu ambiri omwe anali mu ukwati amakhala opanda chimwemwe ndi kukhala kwawo okhaokha. Pakati pa ameneŵa pali anthu amene anali m’banja bwinobwino komano ataya mnzawo wa mu ukwatiwo mu imfa.
Komanso, pali awo amene maukwati awo akhala ovutana kwambiri. Iwo amapeza mpumulo mwa kulera ana awo ali okha. Ambiri a ameneŵa amayamikira za unansi umene akhala nawo ndi ana awo.
Ngakhale kuti pali zochititsa zambiri za kukula kwa mkhalidwe wa mabanja a kholo limodzi, pankhani ya mathayo ndi zovuta za tsiku lililonse, makolo olera ana ali okha amenewo amakhala ndi nkhaŵa zina zapadera. Kodi izo nzotani? Ndipo kodi ndimotani mmene makolo olera okha ana angasenzere bwino mathayo awo?