Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Ninji Ndikudwala Chonchi?
PAMENE Jason anali ndi zaka 13, analingalira zodzatumikira pa Beteli monga mtumiki wa nthaŵi zonse, pamalikulu adziko lonse a Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York. Iye anapanga bokosi la thabwa nalitcha bokosi lake la Beteli. Anayamba kuikamo zinthu zomwe anaganiza kuti nkudzakhala zofunika pamene adzayamba utumiki wake pa Beteli.
Komabe, miyezi itatu yokha litapita tsiku lake lakubadwa la 18, Jason anapezedwa ndi matenda a Crohn—matenda a mmimba osatha, opweteka ndi osoŵetsa ufulu. “Zinandimwaza mtima” iye akukumbukira tero. “Zimene ndinachita ndi kuimbira foni atate ku ntchito ndiye nkumalira. Ndinadziŵa kuti, kaya zikhale bwanji cholinga changa chopita ku Beteli chathera pomwepo.”
Chachikulu chomwe chimapangitsa ‘cholengedwa chonse kubuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano,’ ndi matenda. (Aroma 8:22) Achichepere mamiliyoni osaŵerengeka ali m’gulu la odwala. Achichepere ambiri amachira pambuyo pake. Koma ena amavutika ndi matenda osatha, nthaŵi zina, akayakaya. Zina za zoŵaŵa zomwe achichepere amavutika nazo kaŵirikaŵiri ndi phumi, matenda a shuga, matenda a sickle-cell, matenda opatsirana, khunyu, matenda amaganizo, ndi kansa. Achichepere ena amakhala ndi matenda osiyanasiyina panthaŵi imodzi.
‘Nchifukwa Ninji Zimenezi Zikundichitikira?’
Matenda kaŵirikaŵiri amayambitsa kupsinjika maganizo, kuwonjezera pa kuvutika mthupi. Mwachitsanzo, ngati matenda akulepheretsani kupita kusukulu kwa miyezi, sikuti mudzakhalira pamaphunziro pokha komanso mudzadzimva wobindikira wosiyana ndi anzanu. Pamene Sunny wazaka 12 alephera kupita kusukulu chifukwa choloŵaloŵa m’chipatala amada nkhaŵa, ‘Nchiyani chomwe anzanga akuchita m’kalasi? Nchiyani chomwe ndaphonya lero?’
Mofananamo, mungaone ngati mwasiya kukula mwauzimu ngati muli odwala kwambiri moti nkulephera kupezekapo pamisonkhano yachikristu kapenanso kuŵerenga Baibulo. Zikafika pamenepo, ndiye kuti mufunikira chithandizo kwambiri kuti mulimbe mtima ndi kuti mulimbe mwauzimu. Poyamba simungakhulupirire kuti muli ndi matendawo. Kenako, mungakwiye, mwina kudzikwiyira, poganiza kuti mukanapewa matendawo. Mungafune kulira kuti, ‘Nchifukwa ninji Mulungu walola zimenezi kundichitikira?’ (Yerekezerani ndi Mateyu 27:46.) Ndithudi, munthu mwachibadwa amapsinjika maganizo.
Ndiponso, wachichepere angafikenso poganiza kuti ngati achita khama pazinthu zina, monga ngati kukhala ndi makhalidwe abwino, Mulungu adzamuchiritsa. Komabe, maganizo otero angakukhumudwitseni, chifukwa Mulungu salonjeza machiritso ozizwitsa panthaŵi ino.—1 Akorinto 12:30; 13:8, 13.
Mwinamwake munali kuyembekezera kuti simudzafa—kuti mudzakhalapo pamene Mulungu adzabweretsa “chisautso chachikulu.” (Chivumbulutso 7:14, 15; Yohane 11:26) Ngati mumayembekezera zimenezo, mungadabwe kwambiri mutadziŵa kuti muli ndi matenda amene angawononge moyo. Mungaganize kuti mwina mwalakwa ndipo Yehova wakwiya, kapena mungaganize kuti Mulungu wakusankhani kuti akuyeseni umphumphu wanu. Komabe, uku si kuganiza kwabwino. “Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu,” amatero Mawu a Mulungu. (Yakobo 1:13) Panthaŵi ino anthu amadwala ndi kufa, zimene zili za chisoni, ndipo ife tonse “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika,” zimatikhudza—Mlaliki 9:11.
Kulimbana ndi Mantha
Mwinanso mungachite mantha kwambiri mutagwidwa ndi matenda aakulu. Buku lotchedwa kuti How It Feels to Fight for Your Life limanena zomwe anapeza kwa achichepere 14 okhala ndi matenda aakulu. Mwachitsanzo, Anton, wazaka khumi, amaopa kuti adzafa phumi litamugwira kwambiri. Ndipo Elizabeth, wazaka 16, amene ankadwala kansa ya m’mafupa, ankaopa kupita kukagona kuti mwina sakadzukanso.
Komabe, achichepere ena, ali ndi mantha amtundu wina—amaopa kuti mwina palibe yemwe adzafune kukwatirana nawo mwinanso amaopa kuti sadzakhala ndi ana athanzi mtsogolo. Achichepere ena amaopa kuti mwina matendawo adzapatsirako ena a m’banja mwawo, kaya matendawo amayambukira kapena satero.
Ngakhale ngati matendawo ayamba kuchepa, akayambanso basi mantha amayambanso. Ngati munagwidwako ndi mantha otero, inu mukudziŵa kuti amakhala manthadi. Mwaŵi wake ngwakuti, mantha obweransoŵa amatha pakapita nthaŵi. Tsopano inu mungayambe kuganiza za mavutowo mwanzeru.
Vuto la Kudwala
“Pamene uli wachinyamata, umaganiza kuti ndiwe wolimba,” akutero Jason, wotchulidwa poyamba uja. “Koma, mwadzidzidzi, umapeza kuti ndiwe wosalimba nkomwe utadwala kwambiri. Umamva ngati wakalamba tsiku lomwelo, chifukwa uyenera kumangokhala ndipo osachita zambiri.” Inde, ufulu wanu utachepa zimaŵaŵa.
Jason anapeza kuti vuto lina lalikulu limakhalapo pamene ena akulephera kumvetsa vuto lako. Jason ali ndi matenda omwe tingati ndi “matenda osaoneka.” Maonekedwe ake athupi amabisa vuto la mkati mwake. “Thupi langa siligaya chakudya monga momwe liyenera kuchitira,” Jason akulongosola, “choncho ndimadya kaŵirikaŵiri ndipo ndimadya chakudya chambiri kuposa momwe ambiri amadyera. Koma, ndimakhala wowondabe. Ndiponso, nthaŵi zina ndimatopa kwambiri kwakuti ndimalephera kutsegula maso anga masana. Koma anthu amanena mawu osonyeza kuti iwo amaganiza kuti ndine wolobodoka kapena waulesi. Amanena zinthu monga zakuti: ‘Ukudziŵa kuti ungachite bwino kuposa pamenepa. Koma sukuyesa nkomwe!’”
Jason ali ndi azing’ono ake ndi azichemwali ake omwe nthaŵi zonse samvetsetsa chifukwa chake iye sangathe kuchita zomwe ankachita kale, monga kuŵatenga kupita kokaseŵera mpira. “Koma ndimadziŵa kuti ngati nditavulala,” Jason akutero, “zingatenge milungu kuti ndikhale bwino. Iwo amakonda kuyerekeza zoŵaŵa zanga ndi zawo nkumati, ‘Akungolira kuti muzimuona.’ Iwo amva kuŵaŵa kwambiri akabzungunuka phazi, choncho sangamvetsetse mmene ndimamvera ine.”
Ngati matenda anu akuoneka kuti akuwonjezera mtolo pa banja lanu, mungavutike ndi kudzimva wolakwa. Makolo anu nawonso angadzimve olakwa. “Makolo anga amakhulupirira kuti ndiwo anandipatsa matenda,” akutero Jason. “Nthaŵi zonse ana amazoloŵera matendawo atakhalitsa. Koma makolo zimawavuta. Amandipepesa mobwerezabwereza. Nthaŵi zonse ndimayesetsa kuwatonthoza.”
Kupita Kuchipatala—Si Maseŵera
Maulendo osatha opita kwa dokotala angakhale ochititsa nkhaŵa. Angakumvetse ngati ndiwe wopanda pake ndi wosatha kuchita kalikonse. Kukhala m’chipinda chopimira kudikira nthaŵi yako kumaopsa. “Umadzimva . . . wosungulumwa ndipo kungakhale bwino ngati wina angakhale nawe,” akutero Joseph, wazaka 14, wodwala mtima. Nzachisoni kuti, ana ena sapeza chilimbikitso chotere, ngakhale kwa makolo awo.
Kupima nakonso kungadzutse nkhaŵa. Ndithudi, nthaŵi zina kumavumbula zosasangalatsa. Ndiye, pambuyo pake, ungafunike kulimbana ndi nkhaŵa kwa masiku kapena milungu ukudikira zotsatira. Koma zindikirani ichi: Kupimidwa kuchipatala sikuli ngati kulemba mayeso kusukulu; kudwala sikutanthauza kuti mwalephera m’njira ina yake.
Kwenikweni, kupima kungasonyeze zinthu zofunikira. Kungasonyeze kuti muli ndi matenda omwe akhoza kuchiritsika mosavuta. Mwina, ngati sitero, kupima kungathandize kusonyeza zomwe mungachite kuti muzoloŵere kumakhala ndi vutolo. Mwina kungasonyezenso kuti simukudwala matenda akutiakuti omwe mumaŵaganizira. Choncho musamafulumire kutaya mtima.
Kuda nkhaŵa kwambiri kudzangokulefulani. Baibulo limanena kuti: “Nkhaŵa iŵeramitsa mtima wa munthu.” (Miyambo 12:25) M’malo mwake, Mulungu amafuna kumuuza zakukhosi zathu. Tikayenera kukhulupirira kuti iye amasamala za ife ndi kuti adzatitsogoza ndi kutipatsa nzeru kuti tilimbane ndi mavuto m’njira yabwino yothekera.—Salmo 41:3; Miyambo 3:5, 6; Afilipi 4:6, 7; Yakobo 1:5.
Tingakhale okondwa kuti Mlengi, Yehova Mulungu, wapanga makonzedwe obweretsa dziko latsopano lolungama. Iye adzadzutsa ngakhale omwe anafa, kuŵapatsa mwaŵi wosangalala m’dziko latsopano. Baibulo limatitsimikizira kuti panthaŵiyo, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.
Mpaka panthaŵiyo, inu muyenera kupirira matenda ovutawo. Komabe, pali zambiri zomwe mungachite kuti mukhoze kupirira matenda anuwo. Tidzakambitsirana zimenezi mu nkhani yamtsogolo.
[Chithunzi patsamba 29]
Mungafunse kuti, ‘Nchifukwa ninji Mulungu walola zimenezi kundichitikira?’