Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 7/8 tsamba 18-20
  • Kodi Ndingathe Bwanji Kupirira Matenda Aakulu Chonchi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingathe Bwanji Kupirira Matenda Aakulu Chonchi?
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maganizo Abwino
  • Kupeza Dokotala Womvetsa Zinthu
  • Funafunani Thanzi Labwino!
  • Chithandizo Kuchokera kwa Amene Muli Nawo Pafupi
  • Gwiritsirani ntchito Maganizo ndi Thupi Mwanzeru
  • Musatope ndi Kuleka!
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndikudwala Chonchi?
    Galamukani!—1997
  • Kuvomereza Kuti Zachitika
    Galamukani!—2011
  • Kodi Ndinalakwa Chiyani Kuti Ndidwale Chonchi?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • “Ndasunga Chikhulupiriro”
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 7/8 tsamba 18-20

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingathe Bwanji Kupirira Matenda Aakulu Chonchi?

JASON anali ndi zaka 18 chabe, koma zimaoneka ngati zolinga zake zonse m’moyo nzosatheka tsopano. Amalingalira zodzakhala mtumiki wa nthaŵi zonse wachikristu, koma anatulukira kuti anali ndi Crohn—matenda oŵaŵa ndi ofooketsa a m’mimba. Komabe, lerolino Jason akutha kupirira matendawo.

Mwinamwake inunso mukuvutika ndi matenda aakulu. Mu kope lapitalo, Galamukani! analongosola mavuto amene achinyamata monga inu amakumana nawo.a Tiyeni tsopano tione mmene mungamakhalire.

Maganizo Abwino

Kuti mupirire matenda ena aliwonse zimafuna kuti mukhale ndi maganizo abwino. Baibulo limati: “Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala; koma ndani angatukule mtima wosweka?” (Miyambo 18:14) Kuda nkhaŵa kwambiri kumapangitsa kuchira kukhala kovuta. Jason anapeza zimenezi kukhala zoona.

Poyamba, Jason anali kulimbana ndi kuchotsa maganizo oipa, monga mkwiyo, umene umamtsendereza. Chinamthandiza nchiyani? Akulongosola kuti: “Nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zonena za kupsinjika maganizo zinandithandiza kwambiri kukhala ndi maganizo abwino. Tsopano ndimayesa kuona tsiku lililonse palokha.”b

Carmen wazaka 17 anayamba kuonapo zabwino zokha pamavuto ake. Ngakhale kuti amadwala matenda a sickle-cell anemia, amalingalira za mwaŵi womwe ali nawo. “Ndimalingalira za ena omwe ali odwala kwambiri kuposa ine omwe sangathe kuchita zomwe ndimatha kuchita,” iye akutero. “Choncho ndimakhala wosangalala osati wachisoni kwambiri.”

Miyambo 17:22 imati: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino.” Ena angaganize kuti kuseka nkosayenera pamene ukudwala kwambiri. Koma chimwemwe ndiponso mabwenzi abwino zimasangulutsa malingaliro anu ndipo zimakupangitsani kufuna kumakhalabe ndi moyo. Kunena zoona, chimwemwe ndi khalidwe laumulungu, ndi chimodzi cha zipatso za mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Mzimu umenewo ungakupangitseni kukhala wachimwemwe ngakhale kuti mukulimbana ndi matenda.—Salmo 41:3.

Kupeza Dokotala Womvetsa Zinthu

Kupeza dokotala yemwe amamvetsetsa bwino ana ndi kothandiza. Malingaliro a mwana amasiyana ndi a munthu wamkulu. Ashley anali ndi zaka khumi chabe pamene anapita ku chipatala chifukwa cha chotupa m’bongo. Dokotala wa Ashley anamuthandiza mofatsa ndipo anagwiritsira ntchito maina a zinthu omwe iye akanatha kumva. Anamuuza za mmene matenda ake akadali mwana anamchititsira kuti adzakhale dokotala. Anamlongosolera mofatsa koma momvekera bwino mmene ati ampatsire mankhwala: motero anadziŵa zimene zingachitike.

Inu pamodzi ndi makolo anu mukayenera kupeza madokotala amene adzakulemekezani ndipo amene adzamvetsetsa zomwe mukufuna. Ngati pazifukwa zina simukusangalala ndi chithandizo chimene mukulandira, muli ndi ufulu wonena zimenezi kwa makolo anu.

Funafunani Thanzi Labwino!

Nkoyenera kuti mulimbane ndi matenda mwanjira iliyonse yomwe mungathe. Mwachitsanzo, muyenera kudziŵa bwino kwambiri za matenda anuwo. “Munthu wodziŵa ankabe nalimba,” mwambi wa m’Baibulo umatero. (Miyambo 24:5) Kudziŵa bwino kungakupangitseni kusaopa zotsatira.

Kuwonjezera apo, wachinyamata wodziŵa zinthu angathe kumalankhulapo pa chithandizo chomwe akupatsidwa ndiponso mpamene angalandire chithandizo mosavuta. Mwachitsanzo, angazindikire kuti sayenera kusiya kumwa mankhwala popanda dokotala kuvomereza. Carmen, wotchulidwa poyamba paja, anaŵerenga mabuku onena za matenda a sickle-cell anemia, monga momwe makolo ake nawonso anachitira. Zomwe anaŵerengazo zinawathandiza kupeza mankhwala omwe anathandiza Carmen kwambiri.

Afunseni adokotala mafunso oyenerera—ngati nkotheka osati kamodzi chabe—ngati simukumvetsetsa kanthu kena. Osanena zomwe mukuganiza kuti adokotala angakonde kumva, m’malo mwake nenani moona mtima zomwe mukulingalira ndi momwe mukumvera. Monga momwe Baibulo limanenera, “zolingalira zizimidwa popanda upo.”—Miyambo 15:22.

Panthaŵi ina Ashley amaoneka kukhala wosamasuka kulankhula za matenda ake. Amangonena kwa amayi ake okha. Wantchito wa za umoyo anamfunsa payekha: “Kodi ukulingalira kuti sakukuuza zonse?” Ashley anavomera. Choncho wa za umoyoyo anamsonyeza Ashley makadi ake ndi kumlongosolera bwinobwino. Anapemphanso kuti adokotala azipeza mpata wolankhula ndi Ashley mwachindunji, osati kumangouza ena chabe. Mwa kunena zomwe anali kuganiza, Ashley anatha kupeza chithandizo chomwe amafuna.

Chithandizo Kuchokera kwa Amene Muli Nawo Pafupi

Pamene wina m’banja adwala kwambiri, limakhala vuto la banja lonse, lolira kuthandizana. Achibale a Ashley ndi mpingo wachikristu anachitapo zambiri kumthandiza. Mpingo umakumbutsidwa kaŵirikaŵiri kuti iye ali kuchipatala. Abale ndi alongo amapita kaŵirikaŵiri kukamzonda, ndipo amalithandiza banjalo kuchita ntchito za panyumba ndiponso kuphika kufikira pamene banjalo linapezanso mtendere. Ana a mumpingomo amabwera kukamuona Ashley kuchipatala panthaŵi imene analiko bwino koti nkucheza naye. Izi zimasangalatsa osati Ashley yekha komanso ana anzakewo.

Komabe, ena asanayambe kuthandiza, ayenera kudziŵa bwino kaye kuti mukufunadi thandizo. Carmen amadalira makolo ake ndi akulu mumpingo kuti amlimbikitse mtima ndi kumthandiza mwauzimu. Komanso amaona anzake akusukulu omwe amasonkhana nawo limodzi kukhala othandiza. “Amandimvera chisoni,” Carmen akutero, “ndimaona kuti amandisamalira.”

Nthaŵi zina sukulu yanu ingakuthandizeni pokupatsani malangizo pa za mankhwala oyenera ndi za mmene mungapezere thandizo la ndalama kuchokera kuboma ndiponso nthaŵi zina angabwere kudzathandiza iwo eni. Mwachitsanzo, mphunzitsi wa Ashley anauza kalasi lake kuti limlembere kalata ndi kupita kukamuona. Ngati aphunzitsi anu sakumvetsetsa mavuto amene mukukumana nawo, kungakhale koyenera kuti makolo anu akakambitsirane nawo mwaulemu.

Gwiritsirani ntchito Maganizo ndi Thupi Mwanzeru

Pamene muli wodwala kwambiri, simungathe kuchita kena kalikonse koma kugwiritsira ntchito mphamvu zanu zonse zimene muli nazo kuyesayesa kuti muchire. Ngati sindinu wofooka kwambiri, pali zinthu zambiri zothandiza zimene mukhoza kuchita. Mlembi Jill Krementz anakambapo mawu pa zimene anaona pamene ankafufuza zoti alembe m’buku lake lakuti How It Feels to Fight for Your Life: “Ndili ndi chisoni kuti ndatha zaka ziŵiri ndikuyenda m’khonde mwa chipatala ndiponso kuona ana ambiri [odwala] ali dwii pa TV. Tiyenera kuwalimbikitsa ana ameneŵa kuti aziŵerenga kwambiri. Bedi la kuchipatala ndi malo abwino oti munthu nkugwiritsirapo ntchito mutu wake.”

Kaya muli kunyumba kapena kuchipatala, kumagwiritsira ntchito maganizo anu kaŵirikaŵiri kukhoza kukuthandizani kupezako bwino. Kodi mwayesapo kulemba makalata kapena ndakatulo? Kulemba zithunzi? Ngati muli ndi mphamvuko ndithu bwanji osayesa kuphunzira kuimba chiŵiya china choimbira? Ngakhale mutakhala kuti ndinu wofookerapo, pali zambiri zomwe mukhoza kuchita. Ndithudi, chinthu chabwino koposa chomwe mungachite ndicho kukhala ndi chizoloŵezi chopemphera kwa Mulungu ndiponso kuŵerenga Mawu ake, Baibulo.—Salmo 63:6.

Malinga ndi momwe mukumvera m’thupi, kuchitako maseŵera olimbitsa thupi kukhoza kukuthandizani kupeza bwinoko. Ndicho chifukwa chake kaŵirikaŵiri zipatala zimakhala ndi programu ya maseŵera olimbitsa thupi ya achinyamata odwala. Nthaŵi zambiri maseŵera oyenera olimbitsa thupi samangothandiza kuti muchire msanga chabe komanso amathandiza kuti mukhale wosangalala.

Musatope ndi Kuleka!

Pamene anali pamavuto aakulu, Yesu anapemphera kwa Mulungu ndiponso kumkhulupirira, ndipo analingalira za chimwemwe chomwe adzakhala nacho mtsogolo osati mmene anali kuvutikira. (Ahebri 12:2) Mavuto ake anamphunzitsa zambiri. (Ahebri 4:15, 16; 5:7-9) Analola kuthandizidwa ndi kulimbikitsidwa. (Luka 22:43) Analingalira za moyo wa ena m’malo mwa mavuto ake.—Luka 23:39-43; Yohane 19:26, 27.

Ngakhale kuti mwina mungakhale wodwala kwambiri, mukhozabe kulimbikitsa ena. Mkulu wake wa Ashley, Abigail, analemba pa lipoti lake la kusukulu motere: “Munthu amene ndimamsirira kwambiri ndi mng’ono wanga. Ngakhale kuti amakagonekedwa m’chipatala ndi kuikidwa mapaipi m’mitsempha ndiponso kumabayidwa majekeseni, koma amaonekabe wokondwa!”c

Jason sanagwe mphwayi ndi kuleka zolinga zake, m’malo mwake anangosintha pang’ono. Tsopano cholinga chake ndicho kukatumikira kumene kuli kusoŵeka kwa alaliki a Ufumu wa Mulungu. Mutakhala ndi mavuto ngati a Jason, simungathe kuchita zonse zimene mumafuna. Chofunika ndicho kuzoloŵera kumakhala monga mmene mulili, osati mwamantha kwambiri kapenanso kumangodzilekerera. Dalirani Yehova kuti akupatseni nzeru ndiponso mphamvu kuti muchite zomwe mungathe. (2 Akorinto 4:16; Yakobo 1:5) Ndipo kumbukirani kuti nthaŵi ikudza pamene dziko lidzakhala paradaiso, pamene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Inde, tsiku lina mudzakhalanso athanzi!

[Mawu a M’munsi]

a Onani Galamukani! ya May 8, 1997, masamba 28-30.

b Onani Nsanja ya Olonda, October 1, 1991, tsamba 15; March 1, 1990, masamba 3-9; ndi Galamukani! yachingelezi ya October 22, 1987, masamba 2-16; November 8, 1987, masamba 12-16.

c Onaninso Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 116-27.

[Chithunzi patsamba 19]

Mkulu wake Abigail akusirira kulimba mtima kwa Ashley

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena