Ndife Mabwenzi Odalirana Kwambiri
TRACY ndi galu wonditsogolera, wakuda wazaka 10, mtundu wa agalu wotchedwa Labrador retriever. Chifukwa cha iyeyo ndikhoza kuyenda bwinobwino. Ndi mnzanga ndipo amanditonthoza. Choncho nzosadabwitsa kuti ndafika pomkonda kwambiri ndi kuti ndife mabwenzi odalirana kwambiri.
Nthaŵi zina, anthu mosafuna amandikhumudwitsa, zomwe Tracy sanachitepo. Mwachitsanzo, tsiku lina ndinamusiya Tracy kunyumba ndipo ndinali kuyenda ndi mnzanga. Tinali kukambitsirana mosangalala pamene mwadzidzidzi ine ndinagwera pansi. Mnzangayo anaiŵala kuti ndine wakhungu, ndipo sanandichenjeze kuti kumene ndinali kuponda sikunali bwino. Zoterezi sizikanachitika ndikanakhala ndi Tracy.
Kamodzi, Tracy anapulumutsa moyo wanga. Ndinali kuyenda mu msewu pamene mwadzidzidzi galimoto yalole inayamba kukhotakhota mosalamulirika italunjika kuli ine. Ndinamva kulira kwa injini yake, koma monga wakhungu, sindinaone komwe imaloŵera. Tracy anaona nazindikira za ngoziyo ndipo mwansanga anandikoka nandipulumutsa.
Ndine Wakhungu Inde, Koma Ndipenya
Ndinabadwa mu 1944 kummwera kwa Sweden ndipo ndine wakhungu chibadwire. Ndinatumizidwa kusukulu ya boding’i ya ana akhungu, kumene ndinaphunzira kulemba ndi kuŵerenga za akhungu. Ndinakonda nyimbo, makamaka kuimba piyano. Nditatsiriza maphunziro ku sukulu ya sekondale, ndinapitiriza kuphunzira zinenero ndi nyimbo pa Yunivesite ya Göteborg.
Komabe, moyo wanga unasintha kwamuyaya pamene Mboni ziŵiri za Yehova zinafika pakhomo langa ku yunivesite. Mwamsanga ndinayamba kumapita ku misonkhano ya Mboni ndipo ndinayambanso ngakhale kuwuzako ena zimene ndinali kuphunzira. Mu 1977, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mu ubatizo wa m’madzi. Ngakhale ndine wakhungu, mwa kuphunzira Mawu a Mulungu, ndinalandira kanthu kena kamtengo wapatali—maso auzimu.
Lero ndimadziona kuti ndili bwino kuposa awo amene ali nawo maso mwakuthupi koma ndi akhungu mwauzimu. (Yerekezerani ndi Yohane 9:39-41.) Ndimakondwa popeza ndimachita ngati ndikuliona dziko latsopano la Mulungu mmene, malinga ndi lonjezo lake, maso a akhungu adzapenya—inde, mmene zofooka zonse za m’thupi zidzachizidwa ndipo ngakhale akufa adzauka!—Salmo 146:8; Yesaya 35:5, 6; Machitidwe 24:15.
Ngakhale kuti ndine wosakwatiwa ndiponso wakhungu, ndi Tracy ngati mnzanga wokhulupirika, ndimakhala bwinobwino. Dikirani ndinene momwe amandithandizira pantchito yanga yakuthupi ndi kuchitanso utumiki monga mmodzi wa Mboni za Yehova. (Mateyu 24:14; Machitidwe 20:20; Ahebri 10:25) Koma choyamba, ndiwonjezere pang’ono kunena za Tracy.
Amsankha Kukalandira Maphunziro Apadera
Pamene Tracy anali ndi miyezi isanu ndi itatu yokha, anamyesa ngati angathe kukhala galu wotsogolera akhungu. Anapezeka kuti ngwabata, wosavuta kuphunzitsa, ndi kuti samaopa msanga phokoso la mwadzidzidzi. Choncho, anampereka kubanja lina kwakanthaŵi kuti aphunzire momwe makhalidwe apanyumba alili. Kenako, atakula, anamtumiza kusukulu yophunzitsa agalu otsogolera akhungu.
Pasukulu imeneyi Tracy anaphunzira kuchita zimene agalu otsogolera akhungu afunikira kuchita, monga kuthandiza yemwe adzakhala mbuye wakeyo kupeza pomwe pali chitseko, masitepe, geti, ndi njira. Anaphunziranso kayendedwe ka m’njira za piringupiringu ndi momwe angadutsire misewu. Anamphunzitsanso kuima atafika m’mbali mwa msewu, kutsatira maloboti, ndi kudzera kutali ndi zinthu zopatsa ngozi. Pambuyo pophunzira miyezi ngati isanu, anali wokonzeka kuyamba ntchito. Apa mpamene anandipatsa Tracy.
Zomwe Tracy Amandichitira
Mmaŵa uliwonse Tracy amandidzutsa kuti ndimudyetse. Ndiye timakonzekera za kuntchito. Ofesi yanga ili pamtunda wokwanira ngati mphindi 20 kuyenda kuchokera panyumba yathu. Inde, njira ndimaidziŵa, koma ntchito ya Tracy ndi kundithandiza kuti ndikafike wosagunda magalimoto, anthu, milingoti yamagetsi, kaya china chilichonse. Tikafika, iye amagona kunsi kwa desiki langa. Ndiye, nthaŵi yopuma masana timapita koyenda.
Madzulo, tikabwerako ku ntchito, chigawo chosangalatsa kwambiri cha tsiku chimayambika. Apa mpamene Tracy amanditsogolera mu ulaliki wakunyumba ndi nyumba, ndi kunyumba zomwe ndimachititsako maphunziro a Baibulo. Anthu ambiri ndi aubwenzi kwa iye, amamusisita ndi kumkumbatira ndipo nthaŵi zina amandipatsa chakudya chake. Timapezekanso pa misonkhano yachikristu mlungu uliwonse. Tikatha ana amakonda kumpatsa moni ndi kumkumbatira zomwe Tracy amasangalala nazo kwambiri.
Ndidziŵa kuti Tracy ndi galu basi ndipo tsiku lina adzafa. Izi zidzatanthauza kuti ndidzafunikira kupeza galu wina wonditsogolera. Koma, padakali pano, ndife ogwirizana ndiponso timadalirana. Ngati Tracy sali pafupi, ndimakhala ndi nkhaŵa, ndipo iye ngati sakunditsogolera amanjenjemera ndipo satha kukhazikika.
Kufunika kwa Kumvetsetsa
Chodabwitsa nchakuti, nthaŵi zina anthu amayesa kutilekanitsa. Amaona Tracy monga galu mwina chiŵeto wamba ndipo samvetsa ubwenzi wathu wodalirana Kwambiri. Anthu ameneŵa ayenera kumvetsetsa kuti kwa ine Tracy ali ngati mpando wa magudumu kwa munthu wopuwala. Kutilekanitsa kuli ngati kundichotsera maso.
Ngati anthu atamvetsetsa ubwenzi wathu ndi Tracy, mavuto adzachepa. Mwachitsanzo, anthu nthaŵi zonse amalola mpando wa magudumu koma si kaŵirikaŵiri kumlola galu wotsogolera akhungu. Anthu ena amaopa agalu, mwinanso samaŵakonda chabe.
Uthenga wonena za agalu otsogolera akhungu, wofalitsidwa ndi Swedish Association for the Visually Handicapped, ndi wothandiza. Umati: “Galu wotsogolera akhungu ndi thandizo loyenda la opuwala maso. Inde, aposa ngakhale pamenepo. Ali thandizo koma lamoyo. . . . Ndi bwenzi lomwe silidzakukhumudwitsani.”
Ndithudi, Tracy ndiye maso anga mumdima, ndipo amandithandiza kumakhala bwinobwino monga kungathekere tsopano. Komabe, ndimakhulupirira kuti posachedwa, m’dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu, ndidzatha kuona kukongola kochititsa kaso kwa chilengedwe. Chotero, ndatsimikiza mtima tsopano kusunga maso anga auzimu.
Motero, mutu wa Tracy uli pa miyendo yanga, takonzeka tsopano kuti timvetsere tepi ya magazini ya Nsanja ya Olonda yatsopano.—Yosimbidwa ndi Anne-Marie Evaldsson.