Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 11/8 tsamba 3
  • Aids—Mliriwu Ukupitirizabe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aids—Mliriwu Ukupitirizabe
  • Galamukani!—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Aids—Kodi Tingayembekezerenji m’Tsogolo?
    Galamukani!—1998
  • Kuthandiza Awo Amene Ali ndi AIDS
    Galamukani!—1994
  • “Sipanakhaleko Mliri Wosakaza Kwambiri Chonchi N’kale Lonse”
    Galamukani!—2002
  • Aids—Mmene Tingalimbanirane Nayo
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 11/8 tsamba 3

Aids—Mliriwu Ukupitirizabe

KAREN anakulira kummaŵa kwa United States.a Popeza anali wa Mboni za Yehova, sanachitepo chiwerewere paunamwali wake wonse. Pamene anali ndi zaka 23 mu 1984, anakwatiwa ndi Bill, amene anali atakhala wa Mboni kwa zaka ziŵiri zokha. Anadalitsidwa mwakukhala ndi ana aŵiri, wamwamuna ndi wamkazi.

Pofika mu 1991 anali atakondana kwambiri ndipo anali osangalala zedi. Kumapeto kwa chakacho, palirime la Bill panatuluka banga loyera limene silinathe. Anapita kuchipatala.

Patapita nthaŵi pang’ono, Karen ndi ana aja anali panja kuwola zinyalala. Bill anakhala pamasitepe a pakhomo ndi kumuitana Karen kuti abwere kudzakhala pafupi naye. Anamkumbatira mchiuno ndi kunena misozi ili m’maso kuti amamkonda ndipo amafuna kukhala naye kosatha. Koma nanga bwanji anali ndi misozi? Dokotala anati Bill ayenera kuti ali ndi HIV, kachilombo koyambitsa matenda a AIDS.

Banja lonselo linakapimidwa. Bill ndi Karen anapezeka kuti ali nako. Bill anali atatenga kachilomboko asanakhale wa Mboni za Yehova; ndipo iye anapatsirako Karen. Anawo anapezeka kuti alibe kachilombo. Pakutha zaka zitatu, Bill anamwalira. Karen anati: “Sindidziŵa kuti ndinganene bwanji mmene zimakhalira kuona mwamuna amene umakonda ndipo umafuna kukhala naye kosatha, yemwe kale anali wokongola, akumafooka pang’onopang’ono nkufika powonda kwambiri. Kaŵirikaŵiri ndinkalira usiku. Iye anamwalira kutangotsala miyezi itatu kuti zaka khumi zikwane kuchokera pamene tinakwatirana. Iye anali tate ndiponso mwamuna wabwino.”

Ngakhale kuti dokotala anauza Karen kuti sakhalitsa atsatira mwamuna wake, iye adakali moyo. Tsopano mpamene anayamba kusonyeza zizindikiro zakuti akudwala matenda a AIDS.

Karen ndi mmodzi chabe mwa anthu pafupifupi 30 miliyoni omwe ali ndi kachilombo ka HIV kapena akudwala AIDS, chiŵerengero chachikulu kuposa cha anthu onse a ku Australia, Ireland, ndi Paraguay mutaŵaphatikiza pamodzi. Pali kuyerekezera kwakuti mu Afirika muli anthu 21 miliyoni omwe ali ndi nthendayi. Malinga nziŵerengero za a bungwe la United Nations, pomadzafika m’chaka cha 2001, chiŵerengerocho chidzafika 40 miliyoni. Lipoti lina la bungwe la UN linanena kuti nthendayi ikulingana ndi miliri yoopsa kwambiri imene inachitikapo m’mbiri. Mwa anthu onse akulu omwe ali pausinkhu woti nkugonana ndi wina a zaka kuyambira 15 kufika 49, mmodzi aliyense pa anthu 100 ali nkachilombo ka HIV. Mwa ameneŵa ndi mmodzi yekha mwa khumi amene amadziŵa kuti ali nako. M’maiko ena mu Afirika, pa anthu akuluakulu 100, okwana 25 ali nako.

Kuyambira pamene mliriwu unayambika m’chaka cha 1981, anthu pafupifupi 11.7 miliyoni anafa ndi AIDS. Pali kuyerekezera kwakuti mu 1997 mokha, anthu pafupifupi 2.3 miliyoni anafa. Komabe, anthu ali ndi malingaliro atsopano olimbanirana ndi AIDS. Zaka zingapo zapitazi, chiŵerengero cha anthu odwala AIDS chatsika m’maiko olemera. Kuwonjezera apo, mankhwala omwe amasonyeza ngati atha kuchiritsa amapatsa anthu odwala malingaliro akuti adzachira ndi kukhala ndi moyo wautali.

Kodi mungadzitetezere bwanji ku nthenda ya AIDS? Kodi pachitika zotani posachedwapa pantchito yoyesa kuchiritsa ndi kukonza mankhwala? Kodi nthendayi idzathetsedwa? Mafunso ameneŵa ayankhidwa m’nkhani zotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Tasintha Maina.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena