Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 9/8 tsamba 9-11
  • Potsiriza Pake Tsogolo Lopanda Choopsa!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Potsiriza Pake Tsogolo Lopanda Choopsa!
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zochititsa Zikuluzikulu
  • Kugwirizana kwa Mayiko Onse mu Ulamuliro wa Boma la Padziko Lonse
  • “Bata ndi Chisungiko”
  • Kulekeka kwa Zida za Nyukliya—Motani?
    Galamukani!—1988
  • Chiwopsezo cha Nyukliya Chichotsedwa Kotheratu!
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Angaichititse Ndani?
    Galamukani!—2004
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Angaipeŵe?
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 9/8 tsamba 9-11

Potsiriza Pake Tsogolo Lopanda Choopsa!

“Dziko lonse lapuma, liri du; iwo ayamba kuimba nyimbo.”—YESAYA 14:7.

“DZIKO lathu lili ndi anamatetule pa zida za nyukiliya koma makanda pa kuchita zabwino. Tikudziŵa zambiri za nkhondo kuposa mmene timadziŵira za mtendere, tikudziŵa zambiri za kupha kuposa za kukhala ndi moyo.” Mawu amenewo amene anayankhula mkulu wa asilikali wa ku United States mu 1952, akutikumbutsa mawu a m’Baibulo akuti: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Anthu akakhala ndi zida za nyukiliya, angachite zinthu zoopsa kuposa kungovulaza ena; iwo angathe kuwafafaniziratu!

Anthu ambiri amavomereza kuti kukhala ndi zida za nyukiliya komanso kuzigwiritsa ntchito ndi zolakwika mwachikhalidwe. Mwachitsanzo, George Lee Butler amene kale anali mkulu wa asilikali a nkhondo ya m’mwamba a dziko la United States, ananena kuti: “Chifukwa chokha chakuti winawake ali ndi nkhokwe yosungira zida imene muli zida za nyukiliya chimatidziŵitsa kuti mwinamwake tingathe kuona . . . ngati kuti kuzigwiritsa ntchito si koopsa kwenikweni. Kuteroko ndi kulakwa kwabasi.”

Komabe, mkulu wina wa ku Britain amene amalemba nkhani mu nyuzipepala, Martin Woollacott ananena kuti: “Zida za nyukiliya zikukopabe anthu, ngakhale kuti akatswiri ndi aphunzitsi a makhalidwe abwino akunena kuti zidazi ndi zosafunika komanso zowononga. Mayiko amakhulupirira kuti amazifuna zidazo chifukwa cha zifukwa zomveka zachitetezo; ndipo amazifunitsitsa kwambiri chifukwa chakuti zida za nyukiliya mosakayikira zimachititsa adani mantha aakulu ndipo zimenezi andale komanso asilikali amazidziŵa ndiye amafuna atamaopsa choncho.”

N’zoona kuti pa zaka makumi asanu zapitazi, anthu ayesetsa kupewa nkhondo ya nyukiliya. Koma m’nthaŵi yomweyonso, zida wamba zagwiritsidwa ntchito kupha anthu zikwi zosaŵerengeka. Mwakuyang’ana zimene munthu wachita munthu sungalephere kuganiza kuti, m’tsogolo muno, zida zoopsa za nyukiliya zimenezi zidzagwiritsidwa ntchito.

Zochititsa Zikuluzikulu

Kodi chizoloŵezi chokonda nkhondo chimene anthu ali nacho chingaletsedwe? Ena amanena kuti anthu amachita nkhondo chifukwa chautsiru, kudzikonda, komanso mtima woipa woputa dala anzawo. Katswiri wamaphunziro wina wotchedwa Kenneth Waltz anati: “Ngati zimenezi zili zifukwa zazikulu zoyambitsa nkhondo, ndiye kuti nkhondo zingathe ngati anthu atasinthidwa maganizo komanso kuunikiridwa.”

Ena amanena kuti nkhondo zimayambika chifukwa cha mmene ndale zilili m’mayiko. Chifukwa chakuti dziko lililonse loima palokha limachita zinthu zolikomera, mikangano imabuka mosapeŵeka. Ndiye pakuti palibe njira imodzi yodziŵika bwino ndi yodalirika yothetsera mikangano, nkhondo imabuka. William E. Burrows ndi Robert Windrem analemba motere m’buku lawo lotchedwa Critical Mass: “Mbali yovuta kwambiri ndi yandale. Ulamuliro uliwonse sungakhale wamphamvu ngati olamulira ake choyamba sanatsimikize mtima pandale kuletsa kapena ngakhale kuchepetsa kufala kwa zida zamphamvu kwambiri.”

Taganizirani za nkhani imene akukambiranabe yakuti avomereze mfundo za mu Mgwirizano Woletseratu Kuyesa Zida za Nyukiliya. Nyuzipepala ya Guardian Weekly inalongosola kuti kukambirana kumeneku kuli ngati “kunenerera malonda kwapakati pa mayiko okhala ndi zida za nyukiliya ndi mayiko amene amabisa kuti ali nazo kapena ali ndi njira zakuti angathe kuzipeza mosavuta.” Nkhani yomweyi inavomereza kuti: “Pamagulu aŵiri onseŵa palibe limene limaganizako zotaya zida zawo kapena luso lawo lopangira zidazo, kapena kutsatira mfundo iliyonse imene ilipo yakuti zichepetsedwe.”

Mwachionekere, mgwirizano wa mayiko onse n’ngwofunika kuti kuopa zida za nyukiliya kutheretu. Buku lotchedwa Critical Mass likuti: “Ndiye kuti monsemo kukhulupirirana kuyenera kuloŵa m’malo mwa kugwirizana kuti ngati mutaputana mubwezerana, . . . apo ayi ndiye kuti m’tsogolo muno mukhala zoopsa.” Koma tsoka ilo, kugwirizana ndiponso zokambirana za mayiko lero kaŵirikaŵiri zimafanana ndi zimene mneneri Danieli analongosola zaka mazana 26 zapitazo kuti: ‘Anena mabodza pagome limodzi.’—Danieli 11:27, Byington.

Kugwirizana kwa Mayiko Onse mu Ulamuliro wa Boma la Padziko Lonse

Komabe, Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu mwiniyo amafuna kuti padziko lonse padzakhale kugwirizana pansi pa ulamuliro wa boma lamphamvu zedi la padziko lonse. Anthu miyandamiyanda mosadziŵa akhala akupempherera boma limeneli akamanena Pemphero la Ambuye lakuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Ufumu ndi boma. Ndipo Mkulu wa boma la Ufumu limeneli ndi Kalonga wa Mtendere, Yesu Kristu. Mawu a Mulungu akutitsimikizira kuti: “Za kuyenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha . . . Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.” (Yesaya 9:6, 7) Baibulo limalonjeza kuti boma limene lidzalamulidwe ndi Yesu limeneli ‘lidzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse,’ kapena kuti maboma a anthu.—Danieli 2:44.

Boma la padziko lonse limeneli lidzabweretsa mtendere weniweni ndi chisungiko— koma osati mwakuzengereza kukwaniritsa mapangano a kuletsa zida za nyukiliya kapena mwakupanga mapangano osadalirika oletsa zida. Salmo 46:9 akulosera kuti Yehova Mulungu “aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.” Kuchita zinthu mongoyerekezera sikudzakhala kwabwino. Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Kristu umenewu sudzachepetsa chabe zida za nyukiliya—udzazichotseratu pamodzinso ndi zida zina zonse za nkhondo.

Sipadzakhalanso kuopa zida za nyukiliya chifukwa chakuti sipadzakhalanso mayiko amphamvu kwambiri, mayiko achiwawa, kapena zigaŵenga. Mtendere weniweni udzafalikira: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.” Mawu ouziridwa ameneŵa akuchokera kwa Mulungu amene sanganame.—Mika 4:4; Tito 1:2.

Malingana ndi Salmo 4:8, mtendere weniweni ndi chisungiko zingapezedwe kudzera m’makonzedwe a Yehova Mulungu okha basi: “Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino [“ndikhale mosungika,” NW].” Monga mmene zochitika m’mbiri ya anthu zasonyezera momvetsa chisoni, lonjezo lililonse la “mtendere ndi chisungiko” wosabweretsedwa ndi Ufumu wa Yehova ndiye kuti ndi lonama.—Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 5:3.

“Bata ndi Chisungiko”

Koma nanga bwanji za chizoloŵezi cha anthu chokonda nkhondo? “Okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.” (Yesaya 26:9) Kuphunzira chilungamo kumeneku kudzakhudza kwambiri chizoloŵezi cha anthu ndi mikhalidwe ya dziko: “Ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika [“ndi utumiki wa chilungamo chenicheni, bata ndi chisungiko,” NW] ku nthaŵi zonse.” (Yesaya 32:17) Malingaliro alionse okonda kuputana kapena khalidwe lokonda chiwawa zidzaloŵedwa m’malo ndi kukondana ndi anzathu ndiponso kuderana nkhaŵa. Anthu odzakhala padziko lapansi “adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.

M’kanenedwe kaulosi, Yesaya analosera kuti anthu a zizoloŵezi za uchinyama adzasinthidwa. Iye anakambapo za nthaŵi imene “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova.” Ndipo zotsatira zake zidzakhala zakuti, “mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. . . Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera.”—Yesaya 11:6-9.

Kukhulupirira malonjezo a Mulungu ameneŵa kwachititsa kuti Mboni za Yehova ziziyembekezera zabwino m’moyo. Tikamayang’ana m’tsogolo, sitiona dziko lapansi losakazidwa ndi mabomba a nyukiliya. M’malo mwake, timaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Baibulo lakuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Ena anganene kuti chikhulupiriro choterechi ndi chopanda maziko ndiponso si chenicheni. Koma kodi ndani amene amaganiza zinthu zopanda maziko? Munthu amene amakhulupirira lonjezo la Mulungu kapena amene amangokhulupirira mabodza amene andale amalonjeza? Kwa anthu okondadi mtendere, yankho n’lodziŵikiratu.a

[Mawu a M’munsi]

a Mboni za Yehova zathandiza athu miyandamiyanda kulandira uthenga wa chiyembekezo wa m’Baibulo kudzera m’phunziro la Baibulo lapanyumba laulere. Mungathe kukonza kuti adzakuyendereni polembera kalata kwa ofalitsa magazini ino kapena popita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya kumene mumakhala.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

“Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4

[Chithunzi patsamba 9]

M’dziko latsopano la Mulungu, mabanja “adzakhala mosungika,” ndipo zida zankhondo za mitundu yonse zidzachotsedwa

[Chithunzi patsamba 10]

Chizoloŵezi chokonda nkhondo chimachepetsedwa anthu akamaphunzira ndi kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, Baibulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena