Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 10/10 tsamba 3
  • “Anthu Asiyiratu Kukhulupirirana”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Anthu Asiyiratu Kukhulupirirana”
  • Galamukani!—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Nchifukwa Ninji Kudalirana Kukuvuta?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Tingayambenso Kudalirana!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Anyamata Awiri Oukitsidwa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 10/10 tsamba 3

“Anthu Asiyiratu Kukhulupirirana”

Ku West Africa, mnyamata wina wa zaka 12 anagonekedwa m’chipatala atamwa mankhwala achabechabe a malungo amene mayi ake anagula ku sitolo yogulitsa mankhwala yovomerezedwa ndi boma. Dokotala wina anati: “Kwa zaka 15, takhala tikupeza mankhwala achinyengo akugulitsidwa m’malo osiyanasiyana.”a

Makolo a mwana wongobadwa kumene ku Asia anakhumudwa kwambiri atazindikira kuti mkaka umene ankapatsa mwana wawo, womwe ankati umawonjezera mavitamini, unali ndi mankhwala enaake oopsa. Kenako mwanayo anamwalira chifukwa cha mkaka umenewu.

Munthu wina wabizinezi ku America, yemwe anthu ankamukhulupirira kwambiri, anapezeka kuti ndi wachinyengo ndipo ankabera anthu ndalama zambirimbiri. Anthu ambiri anakhumudwa atazindikira kuti ndalama zawo za penshoni zimene ankasungitsa kwa mkuluyu zalowa m’madzi. Ndipo akatswiri azachuma akuti zimene mkuluyu wakhala akuchita ndi “chinyengo chachikulu chomwe sichinachitikeponso m’zaka 100 zapitazi.”

PAFUPIFUPI munthu aliyense anakhumudwitsidwapo ndi munthu amene ankamukhulupirira kwambiri, munthuyo atamuchitira zachinyengo. Malinga ndi nyuzipepala ya ku France ya Le Monde, mavuto azachuma omwe ali padziko lonse anayamba makamaka chifukwa chakuti “anthu asiyiratu kukhulupirirana.”

Kodi n’chiyani chachititsa kuti anthu ‘asiye kukhulupirirana’ masiku ano? Kodi pali munthu amene mungamukhulupirire?

[Mawu a M’munsi]

a Nkhaniyi inalembedwa m’nyuzipepala ya Le Figaro, yomwe imasindikizidwa ku Paris, m’dziko la France.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena