3. N’chifukwa Chiyani Anthu Abwino Amavutika?
Chifukwa Chake Kudziwa Yankho la Funsoli Kuli Kofunika
Zimaoneka kuti n’zopanda chilungamo kuti anthu abwino azivutika. Zimenezi zimachititsa anthu ena kuona kuti palibe chifukwa chokhalira munthu wabwino.
Taganizirani Izi
Anthu ena amakhulupirira kuti munthu akafa amakabadwanso. Iwo amanena kuti munthu amene ankachita zabwino akabadwanso amakhala ndi moyo wabwino, koma amene ankachita zoipa akabadwanso amakhala moyo wovutika. Malinga ndi zimene anthuwa amakhulupirira, ngakhale munthu atakhala wabwino pano, akhoza kumakumanabe ndi mavuto ngati ankachita zinthu zoipa “m’moyo wa m’mbuyomu.” Komabe . . .
Kodi cholinga cha kuvutikaku chingakhale chiyani popeza munthu amene akuti akafa amabadwanso, sakumbukira n’komwe zimene ankachita m’moyo wa m’mbuyomu?
N’chifukwa chiyani panopa timayesetsa kukhala ndi moyo wathanzi komanso kupewa ngozi, chonsecho tikhoza kumavutikabe chifukwa cha zinthu zoipa zimene tinkachita m’moyo wa m’mbuyomu?
KUTI MUDZIWE ZAMBIRI
Onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika? pa jw.org.
Zimene Baibulo Limanena
Kuvutika si chilango chochokera kwa Mulungu.
Koma m’malomwake zimangochitika, ndipo nthawi zambiri zimachitika chifukwa choti tili pamalo olakwika komanso pa nthawi yolakwika.
“Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano, amphamvu sapambana pankhondo, anzeru sapeza chakudya, omvetsa zinthu nawonso sapeza chuma, ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa, chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”—MLALIKI 9:11.
Uchimo umachititsanso kuti tizivutika.
Nthawi zambiri anthu akamanena kuti “tchimo” amatanthauza zinthu zoipa zimene munthu amachita. Komabe Baibulo limagwiritsa ntchito mawuwa potanthauza za uchimo umene anthu onse, abwino ndi oipa omwe, anatengera.
“Anandilandira mu zowawa za pobereka ndili wochimwa. Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.”—SALIMO 51:5.
Uchimo wabweretsa mavuto ambiri kwa anthu.
Wachititsa kuti anthufe tisakhale pa ubwenzi wabwino ndi Mlengi wathu komanso wachititsa kuti tisamagwirizane ndi anzathu, tizikhala ndi maganizo oipa, komanso kuti tiwononge dzikoli. Zimenezi zachititsa kuti anthu onse azikumana ndi mavuto ambiri.
“Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.”—AROMA 7:21.
“Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa.”—AROMA 8:22.