Mungapeze Thandizo
Kodi munthu amene mumamukonda wamwalira?
Pitani pa jw.org, ndipo fufuzani nkhani yakuti “mfundo zothandiza amene aferedwa.”
Kodi mukukumana ndi mavuto azachuma?
Pitani pa jw.org, ndipo fufuzani nkhani yakuti “muzigwiritsa ntchito ndalama mwanzeru.”
Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘Kodi pali chifukwa chilichonse chokhalira ndi moyo?’
Pitani pa jw.org, ndipo fufuzani nkhani yakuti, “kodi kudzipha ndi njira yabwino yothetsera mavuto?” komanso yakuti “kodi mukuona kuti palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo?”
Kodi mukuvutika ndi matenda okhalitsa?
Pitani pa jw.org, ndipo fufuzani nkhani yakuti, “ngati mukudwala matenda aakulu.”
M’Baibulo muli malangizo omwe angathandize wina aliyense m’banja kuti azikhala moyo wabwino. Mfundo zake zingathandize munthu kukhala woganiza bwino komanso kumachita zinthu mwachilungamo.—MIYAMBO 1:1-4.
Tikukulimbikitsani kuti muphunzire Baibulo. Onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? popanga sikani kachidindo aka kapena pitani pa jw.org.