Mawu Oyamba
Kodi mukuda nkhawa chifukwa cha kukwera mitengo kwa zinthu? Kodi mumafunika kugwira ntchito maola ambiri kuti mungopeza zofunika pa moyo? Kodi mumakhala ndi nthawi yochepa yochita zinthu ndi anthu a m’banja lanu komanso anzanu? Ngati ndi choncho, nkhani zomwe zili mu Galamukani! iyi zikuthandizani. Muli malangizo amene angakuthandizeni kuti muzisangalala komanso kuti musamade nkhawa kwambiri. Nkhani yomaliza ikufotokoza za chiyembekezo chabwino kwambiri ndipo kudziwa zimenezo kungakuthandizeni ngakhale panopa.