Phunziro 31
Khutiritsani Omvetsera Anu, Lingalirani Nawo
1, 2. Kodi kufotokoza kokhutiritsa ndiko chiyani?
1 Pamene mulankhula mumafuna kuti omvetsera anu atchere khutu. Koma si zokhazo. Mumafunanso kuti akhulupirire zimene mukufotokozazo ndi kuti achitepo kanthu. Iwo adzachitadi zimenezo ngati akhutiritsidwa kuti zimene mukunena n’zoona komanso ngati mitima yawo ili yabwino. Kukhutiritsa kumatanthauza kupereka umboni wothetsa chikayikiro chonse. Koma umboni wokha nthaŵi zina sumakwanira. Nthaŵi zambiri pamafunikanso mafotokozedwe ochirikiza umboniwo. Chifukwa chake, kukhutiritsa mwa mafotokozedwe kumaphatikizapo zinthu zitatu zazikulu: choyamba, umboni weniweniwo; chachiŵiri, tsatanetsatane kapena dongosolo la kaperekedwe ka umboniwo; chachitatu, mkhalidwe wake ndi njira zogwiritsidwa ntchito poupereka. Pamfundoyi yotchedwa “Kufotokoza kokhutiritsa,” pa fomu ya Uphungu wa Kulankhula, tidzalongosola zimene mulankhula, umboni umene muupereka, koma osati mmene muuperekera.
2 Kufotokoza kokhutiritsa kumadalira zifukwa zomveka, ndipo umo ndi mmene phungu wanu adzaonera mfundoyo. Umboni wanu uyenera kukhala wokhutiritsa ngakhale ngati munthu angauŵerenge papepala. Ngati kukhutiritsa kwa nkhani yanu kumadalira njira imene mukulankhulira, osati umboni umene mwagwiritsa ntchito pomveketsa mfundo yanu, pamenepo mudzafunikira kulimbikirabe kuti mukulitse luso limenelo kuti kufotokoza kwanu kuzikhala kodalirika ndi kopereka umboni weniweni.
3-6. Nenani chifukwa chake maziko ayenera kukhazikitsidwa.
3 Kukhazikitsa maziko. Musanafotokoze mfundo zanu, m’pofunika kuyamba mwakhazikitsa maziko oyenera. Muyenera kumveketsa bwino mfundo ya nkhani yanu. Ndiponso kumathandiza kukhazikitsanso mfundo yogwirizanapo mwa kugogomeza zinthu zofunika zimene mukuvomerezana.
4 Nthaŵi zina kumakhala kofunika kutanthauzira mawu kuti amveke bwino. Musaphatikizepo zilizonse zosagwirizana ndi nkhaniyo. Ndipo musadye mfulumira pokhazikitsa maziko anu. Akhazikitseni zolimba, koma mazikowo asakhale chimango chonse. Ngati mukutsutsa mfundo inayake, pendani mfundo zosiyanasiyana zogwiritsidwa ntchito poichirikiza kotero kuti mudziŵe kulakwa kwake ndi kuona mmene mungaperekere zifukwa zanu ndi mmene mungafikire pamfundo yeniyeni.
5 Pokonza nkhani yanu, muyenera kuyesa kuganizira zimene omvetsera anu akudziŵa kale m’nkhaniyo. Zimenezo zidzakuthandizani kudziŵa ukulu wa maziko amene muyenera kukhazikitsa musanayambe kufotokoza mfundo zanu.
6 Popeza Akristu ndi anthu osamala ndi akhalidwe, m’pofunika kuti tizilankhula mokoma mtima ndi moganizira ena, ngakhale kuti imeneyo sindiyo mfundo imene tikufotokoza panopa. Nthaŵi zonse gwiritsani ntchito uphungu wachikristu umene mumadziŵa ndipo tsegulani mitima ndi maganizo a omvetsera.
7-13. Fotokozani tanthauzo la mawu akuti “umboni womveka.”
7 Kupereka umboni womveka. Anthu sangokhulupirira zilizonse chifukwa chakuti inuyo mwalankhula, kapena chifukwa mumazikhulupirira. Nthaŵi zonse dziŵani kuti omvetsera anu salakwa konse pofunsa kuti, “N’chifukwa chiyani zimenezo zili zoona?” kapena kuti, “N’chifukwa chiyani mukunena kuti zili motero?” Choncho monga wolankhula nkhani, nthaŵi zonse mumafunikira kuyankha funso lakuti “Chifukwa chiyani?”
8 Poyankha mafunso akuti “Motani?” “Ndani?” “Kuti?” “Liti?” “Chiyani?” timangotchula zinthu. Koma poyankha funso lakuti “N’chifukwa chiyani?” timapereka zifukwa. Chifukwa cha chimenecho funso limenelo n’lapadera ndipo limafuna kuti mufotokoze zochulukirapo kuposa kungotchula zinthu. Limapatsa ntchito maganizo anu. Chifukwa cha chimenecho, pokonza nkhani yanu, dzifunseni funsolo mobwerezabwereza: “N’chifukwa chiyani?” Ndiyeno tsimikizani kuti mutha kupereka mayankho.
9 Pofuna kupereka zifukwa pazimene mukulankhulazo mungathe kugwira mawu a munthu wina amene anthu amam’khulupirira kuti ndiye ali ndi ukumu pankhaniyo. Zimenezo zikutanthauza kuti ngati iye ananenadi zimenezo, ndiye kuti ndi zoona chifukwa anthu akudziŵa kuti iyeyo amadziŵadi. Chimenecho chimakhala chifukwa chokwanira kuti anthu akhulupirire. Koma kwa ife, Mwiniukumu wonse pantchito yathu ndi Yehova Mulungu. N’chifukwa chake kugwira mawu a m’Baibulo ndi umboni wokwanira wotsimikiza zimene tinena. Umenewu ndi umboni wa “mawu onenedwa” chifukwa ndi mawu a mboni yokhulupirika.
10 Popereka umboni wa mawu onenedwa muyenera kutsimikiza kuti amaikhulupirira mboniyo. Ngati mboni zanu ndi anthu, dziŵani za mbiri yawo ndi mmene omvetsera adzawaonera. Anthu ambiri amavomereza kuti Baibulo ndi Mboni yochokera kwa Mulungu, koma ena amangoliona kukhala buku la munthu ndipo umboni wake samaukhulupirira kwenikweni. Zikakhala motero, sinthirani ku umboni wina kapena choyamba fotokozani chifukwa chake Baibulo lili loona.
11 Koma tichenjeze pano. Umboni wonse uyenera kugwiritsidwa ntchito moona mtima. Musapotoze tanthauzo la mawu ogwidwawo. Tsimikizani kuti zimene mukunenazo n’zimenedi mwini mawuwo ananena. Tchulani momvekera bwino gwero la umboni wanu. Komanso samalani ndi ziŵerengero. Ngati mutchula zolakwa, mungapalamule nazo. Kumbukirani munthu uja wosadziŵa kusambira, ndipo anamira pamtsinje wakuya pafupifupi mita imodzi yokha. Anali ataiŵala za dzenje limene linali pakati pa mtsinjewo lakuya pafupifupi mamita atatu.
12 Kuwonjeza pa umboni wa mawu onenedwa ndi anthu kapena Mulungu, palinso umboni wa zochitika. Umenewo ndi umboni wodalira mmene mukuonera zochitikazo m’malo mwa mawu ogwidwa a mboni. Kuti mutsimikizire maganizo anu ndi kuti umboni wanu wa zochitika ukhale wokhutiritsa, muyenera kukhala ndi zifukwa zokwanira zochirikiza maganizo anu.
13 Ngati umboni wonse umene mupereka (osati kwenikweni mwatsatanetsatane) uli wokwanira kukhutiritsa nawo omvetsera amene mukulankhula nawo, phungu wanu adzauona kukhala wokhutiritsa. Phunguyo adzadziika m’malo mwa omvetserawo ndi kudzifunsa kuti, “Kodi ndakhutira?” Akadziyankha kuti inde wakhutira, adzakuuzani kuti mwachita bwino.
14. Kodi kulongosola kwachidule kogwira mtima n’chiyani?
14 Kulongosola kwachidule kogwira mtima. Kulongosola kwachidule kumakhala kofunika nthaŵi zambiri pofuna kupereka mfundo zokhutiritsa. Ndi mbali yomalizira yolimbikitsa omvetsera kulingalira, kuti amvetse mfundo zimene mwafotokoza. Kulongosola kwachidule sindiko kungotchula mfundo basi, ngakhale kuti kwenikweni kumangokhala kunena kuti “popeza izi zili choncho, kapena, popeza zimenezo zili motero, tinganene kuti . . . ” Cholinga cha kulongosola kwachidule ndicho kumangirira pamodzi mfundo zonse kuti zimange mfundo imodzi. Nthaŵi zambiri kulongosola kwachidule kogwira mtima n’kumene kumamveketsa mfundo zokhutiritsa.
**********
15, 16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza omvetsera kulingalira?
15 Ngakhale kafotokozedwe kanu ka nkhani kangakhale komveka bwino, sikukhala kokwanira kungotchula zinthu. Muyenera kuzinena m’njira yothandiza omvetsera kulingalira, kuti amvetse zimene mukufotokoza ndi kuti afike pamaganizo amene inu mwafikapo. Izi n’zimene zimatchedwa “Kuthandiza omvetsera kulingalira,” pasilipi la Uphungu wa Kulankhula.
16 Muyenera kulisirira luso limeneli chifukwa Mulungu amalingalira nafe. Ndiponso, Yesu anafotokoza mafanizo ake kwa ophunzira ake nawaphunzitsa kuphunzitsa choonadi chimodzimodzicho kwa ena. Choncho, kuthandiza omvetsera kulingalira, kumatanthauza kugwiritsa ntchito njira zofunika kuthandiza omvetsera kumvetsa mfundo zanu, kuti afike pamaganizo amene muli nawo ndi kukhoza kukawaphunzitsa kwa winanso.
17, 18. Kodi mfundo yogwirizanapo tingaisunge motani?
17 Kusataya mfundo yogwirizanapo. Zimene mulankhula ndi mmene mukuzilankhulira n’zofunika pofuna kukhazikitsa mfundo yogwirizanapo pachiyambi penipeni pa nkhani yanu. Koma mfundo yogwirizanapo imeneyo musaitaye pamene mukupitiriza ndi nkhani yanu, chifukwa mungatayenso omvetsera anu. Muyenera kupitiriza kufotokoza mfundo zanu m’njira yokopa maganizo a omvetsera anu. Zimenezo zimafuna kuti musaiŵale maganizo awo pankhani imene mukukambirana ndipo gwiritsani ntchito zimene akuganizazo kuwathandiza kuona nzeru yake ya zimene mukufotokoza.
18 Chitsanzo chabwino kwambiri cha kukhazikitsa mfundo yogwirizanapo ndi kusaitaya mpaka kumapeto, ndiko kuti, kuthandiza omvetsera kulingalira, ndicho mafotokozedwe a mtumwi Paulo, olembedwa pa Machitidwe 17:22-31. Onani mmene iye anakhazikitsira mfundo yogwirizanapo pachiyambi pa nkhani yake ndi mmene anaisungira mpaka kumapeto. Pamene anatsiriza anali atakhutiritsa ena mwa omvetserawo za choonadi, kuphatikizapo woweruza amene analipo.—Mac. 17:33, 34.
19-23. Tchulani njira zimene tingamveketsere mfundo mokwanira.
19 Kufotokoza mfundo momveka bwino. Kuti omvetsera alingalire bwino za nkhani imene ikulankhulidwa, ayenera kumva mfundo zokwanira zofotokozedwa momveka bwino kotero kuti, ngati angazikane chisakhale chifukwa chakuti sanazimvetse bwino. Zili kwa inu kuwathandiza.
20 Kuti muwathandize kumvetsa, samalani kuti musafotokoze mfundo zochuluka kwambiri. Phindu la mfundo zanu lidzatayika ngati muzifotokoza mofulumira kwambiri. Dekhani kuti mufotokoze mfundo zanu bwinobwino kuti omvetsera anu amve komanso kuti azimvetsetse. Mutatchula mfundo yofunika, tayiranipo nthaŵi kuifutukula. Yankhani mafunso akuti N’chifukwa chiyani? Ndani? Motani? Chiyani? Liti? Kuti? M’njira imeneyo thandizani omvetsera anu kumvetsa bwino lomwe mfundozo. Nthaŵi zina mukhoza kutchula maganizo otsutsa mfundo yanu kapena oichirikiza pofuna kugogomeza nzeru ya mfundo yanu. Mofananamo, mutatchula mfundo inayake, kungakhale kothandiza kuperekapo fanizo kuti omvetsera aone tanthauzo lake. Komabe, m’pofunika kusamala. Kuti mfundo iliyonse mudzaifotokoza kufikira pati, zidzadalira nthaŵi imene muli nayo komanso kufunika kwake kwa mfundoyo m’nkhani yanu.
21 Nthaŵi zonse mafunso amathandiza omvetsera kuganiza. Mafunso osafuna yankho kuchokera kwa omvetsera, limodzi ndi kupuma koyenerera, zimalimbikitsa kulingalira. Ngati mukulankhula kwa munthu mmodzi kapena aŵiri, monga mu utumiki wakumunda, mungawalimbikitse kulankhula mwa mafunso pamene mukukambirana, ndipo m’njira imeneyo onetsetsani kuti akumvetsa ndi kuvomereza maganizo amene akuperekedwa.
22 Pakuti mukufuna kutsogolera maganizo a omvetsera anu, muyenera kufutukula mfundo zanu kuchokera pa zinthu zimene akuzidziŵa kale, kaya ndi zochitika za m’moyo wawo kapena zimene mwakambapo kale m’nkhani yanuyo. Choncho, pofuna kudziŵa ngati mfundo zina mwazimveketsa bwino, muyenera kuona zimene omvetsera anu anali kuzidziŵa kale m’nkhani yanuyo.
23 Nthaŵi zonse n’kofunika kuona mmene omvetsera anu akuchitira pofuna kutsimikiza ngati akukutsatirani. Pamene kukhala kofunikira, bwererani m’mbuyo ndi kumveketsa bwino mfundo zina musanapitirize ndi mfundo zina. Athandizeni kuganiza nthaŵi zonse, apo phuluzi adzalephera msanga kutsatira malingaliro anu.
24. Kodi kuthandiza omvetsera kuona mmene nkhaniyo ikuwakhudzira kuli ndi cholinga chabwino chotani?
24 Kuonetsa omvetsera mmene nkhaniyo ikuwakhudzira. Pofotokoza mfundo zilizonse, onetsaninso cholinga chake pankhaniyo. Ndiponso, khalani wolimbikitsa m’nkhani yanuyo, mukumafulumiza omvetsera anu kuchitapo kanthu molingana ndi mfundo zimene zaperekedwa. Ngati iwo akhutiradi ndi zimene mwanena, adzachitapo kanthu msanga.