Phunziro 30
Kulankhula Nkhani Kogwirizanika
1-3. Kodi kugwirizanika kwa nkhani kumagwira ntchito yanji, ndipo kungakhalepo motani?
1 Nkhani yogwirizanika imakhala yosavuta kwa omvetsera kuitsatira. Koma ngati siili yogwirizanika chidwi chawo chimatayika msanga. Mwachionekere, imeneyi ndi mfundo yofunikira chisamaliro chachikulu pamene mukukonza nkhani; choncho “Kugwirizanitsa nkhani ndi mawu olumikizira” kwaphatikizidwa pasilipi la Uphungu wa Kulankhula kuti mukuphunzire mosamalitsa.
2 Kugwirizanika kumatanthauza kulumikizika, kugwirizana kwa mbali zosiyanasiyana kuti zipange thunthu limodzi lomveka bwino. Nthaŵi zina zimenezi zimatheka ndi dongosolo la kalinganizidwe ka mbalizo. Koma m’nkhani zambiri pamakhala mbali zina zofunikira kugwirizanitsidwa mosamala kwambiri. M’zochitika zoterozo pamafunikira milatho yowolokera kuchoka pa mfundo imodzi kupita pa ina. Alipo mawu amene amagwiritsidwa ntchito kusonyeza mgwirizano wa maganizo amene anenedwa kale ndi atsopano, pofuna kusintha chifukwa cha nthaŵi kapena mfundo. Kumeneku kumatchedwa kugwirizanitsa mwa mawu olumikizira.
3 Mwachitsanzo, mawu oyamba, thunthu ndi mawu omalizira a nkhani yanu ndizo mbali zolekanalekana za nkhani, zosiyana ina ndi inzake, komabe ziyenera kugwirizanitsidwa pamodzi mwa mawu olumikizira. Ndiponso, mfundo zazikulu ziyenera kugwirizanitsidwa pamodzi m’nkhani, makamaka ngati sizili zokhudzana mwachindunji m’ganizo lake. Ndipo nthaŵi zina ndi masentensi okha kapena ndime zimene zimafunikira mawu olumikizira.
4-7. Kodi kugwiritsa ntchito mawu olumikizira kumatanthauzanji?
4 Ntchito ya mawu olumikizira. Kaŵirikaŵiri mlatho pakati pa maganizo ungayalidwe mwa kungogwiritsa ntchito mawu oyenera olumikizira. Naŵa ena a mawuwo: ndiponso, komanso, kuwonjezera apo, mofananamo, chifukwa chake, motero, choncho, pazifukwa zimenezo, malinga ndi zimenezo, kenako, pambuyo pake, komabe, kumbali ina, mosiyana ndi zimenezo, mwa njira ina, malinga ndi kumbuyoku, ndi ena otero. Mawu oterowo amagwirizanitsa masentensi ndi ndime bwino lomwe.
5 Komabe, luso lolankhula limenelo limafuna zoposa mawu olumikizira osavutawo. Pamene liwu limodzi kapena mawu ena sakwanira, pamafunikira mawu ena onga mlatho owolotsera omvetserawo pampatawo kupita ku ganizo lina. Mlatho umenewo ungakhale sentensi yathunthu kapena maganizo ena owonjezera.
6 Njira imodzi imene tingayalire mlatho pamipata imeneyo ndiyo kuyesa kugwiritsa ntchito tanthauzo la mfundo yapitayo kukhala gawo la mawu oyamba a zimene zikutsatirapo. Kaŵirikaŵiri timachita zimenezo mu ulaliki wathu wa kunyumba ndi nyumba.
7 Ndiponso, si mfundo zotsatizana zokha zimene ziyenera kugwirizanitsidwa pamodzi, koma nthaŵi zina ngakhale mfundo zina zotalikirana m’nkhaniyo. Mwachitsanzo, mawu omalizira a nkhani ayenera kugwirizanitsidwa ndi mawu oyamba. Mwinamwake ganizo kapena fanizo lotchulidwa poyamba nkhani lingatanthauziridwe m’mawu omalizira m’njira yolimbikitsa kapena yosonyeza mgwirizano wake pakati pa fanizolo kapena ganizolo ndi cholinga cha nkhaniyo. Kutchulanso mbali zina za fanizolo kapena ganizolo mwanjira imeneyo kumalumikiza bwino ndipo kumagwirizanitsa nkhani.
8. Kodi kugwiritsa ntchito mawu olumikizira kumadalira motani omvetsera?
8 Kugwirizanika koyenerana ndi omvetsera anu. Kuchuluka kwa mawu olumikizira oti mugwiritse ntchito kumadalira omvetsera anu. Koma sikuti omvetsera ena safunikira mawu olumikizira. M’malo mwake, omvetsera ena amangofunikira ochulukirapo, chifukwa cha kusadziŵa bwino mfundo zimene mufuna kuzigwirizanitsa. Mwachitsanzo, Mboni za Yehova zimagwirizanitsa msanga lemba lonena za mapeto a dongosolo la zinthu loipali ndi lemba lonena za Ufumu. Koma kwa munthu wina amene Ufumuwo wangokhala mkhalidwe wa maganizo chabe kapena mtima wa munthu, mgwirizano wake ungakhale wovutirapo kuuzindikira, moti pangafunikire kufotokoza ganizo lina lothandizira kuti mgwirizanowo uoneke. Ntchito yathu ya kukhomo ndi khomo imafuna kusintha koteroko nthaŵi zonse.
**********
9-13. Kodi kulankhula kotsatirika n’kutani, ndipo ndi njira ziŵiri zazikulu zotani zimene tingafutukulire mfundo?
9 Mbali ina ya kulankhula yofanana kwambiri ndi imeneyo ndiyo “Kulankhula kotsatirika ndi kogwirizanika,” ndipo iyinso ikupezeka pa fomu ya uphungu. Ndi yofunika kwambiri pa kulankhula kokopa anthu.
10 Kodi tikati kutsatirika tikutanthauzanji? Malinga ndi cholinga chathu m’nkhaniyi, tinganene kuti kutsatirika ndi luso la kalingaliridwe kolondola kapena kuganiza mwanzeru. Kumamveketsa nkhani chifukwa ndiyo njira yofotokozera mbali zosiyanasiyanazo koma zogwirizana. Kutsatirika kumasonyeza chifukwa chake mbalizo zimagwirizana ndi kuthandizana. Kulankhula kumakhala kogwirizanika ngati mafotokozedwe ake amafutukula mfundo pang’onopang’ono m’njira yogwirizanitsa mfundo zonse motsatizana. Kulankhula kotsatirika kungakhale kuja kotsatira dongosolo loyamba ndi chinthu chofunika kwambiri, kapena dongosolo la zaka kapena nthaŵi pamene zinthu zinachitika kapenanso kuchokera pa funso kupita ku yankho, kungotchulapo zingapo zokha.
11 Pofutukula mfundo za nkhani pali njira zazikulu ziŵiri zimene tingazitsate. (1) Tchulani choonadi kwa omvetserawo, kenako perekani umboni wochirikiza choonadicho. (2) Tchulani mfundo ina yolakwa imene ena amanena, ndipo poigwetsa ndi zoona, choonadi chidzaonekera chokha. Chimene chimangotsala kwa inu ndi kumveketsa bwino tanthauzo lake la choonadicho.
12 Palibe alankhuli aŵiri amene amalingalira mofanana. Chitsanzo chabwino kwambiri cha kalingaliridwe kosiyana pankhani imodzimodzi chikupezeka m’kalembedwe ka Mauthenga Abwino anayiwo. Ophunzira a Yesu anayi analemba za utumiki wake payekhapayekha. Nkhani ya aliyense inalembedwa mosiyana, koma onse analemba nkhani zomveka ndi zotsatirika. Aliyense anafotokoza nkhani yake ndi cholinga chofanana ndipo onse anachikwaniritsa cholingacho.
13 Pamfundo imeneyi phungu ayenera kudziŵa cholinga chanu ndi kuyesa kupenda tsatanetsatane wa mfundo zanu mwa kuona kuti kaya cholinga chake chakwaniritsidwa kapena ayi. Mukhoza kuthandiza iye limodzi ndi omvetsera anu, mwa kumveketsa bwino cholinga chanu, makamaka m’mawu anu oyamba ndi kusonyeza tanthauzo lake m’mawu omalizira.
14, 15. Fotokozani chifukwa chake kukhala ndi dongosolo labwino lofotokozera mfundo kuli kofunika kwambiri.
14 Mfundo zosanjidwa m’dongosolo labwino. Choyamba, pokonza mfundo zanu kapena autilaini yanu, onetsetsani kuti simukuphatikizapo mawu kapena ganizo limene lilibe maziko ake. Nthaŵi zonse dzifunseni mafunso aŵa: Kodi chotsatira chimene ndingayembekezeke kunena n’chiyani? Nditafika pamenepa, kodi funso lanzeru limene lingafunsidwe ndi lotani? Mutadziŵa funso limenelo, liyankheni nthaŵi yomweyo. Nthaŵi zonse okumvetserani ayenera kukhala okhoza kunena kuti: “Mwa zimene mwanena kale ndikuona kuti mfundo iyi ili yoona.” Ngati simunakhazikitse maziko alionse, mfundoyo ingaoneke yosatsatirika. Adzaona kuti chinachake chikusoŵeka.
15 Pokonza mfundo zanu muyenera kuona mbali zimene zimadalirana zokha. Onani mgwirizano wake ndi kuzilinganiza moyenerera. Kuli ngati kumanga nyumba. Palibe womanga aliyense angayambe kumanga makoma asanayambe wakhazikitsa maziko ake. Kapena sangaikiretu pulasitala kumakoma kenako n’kumayala mapaipi onse a madzi. Zilinso chomwecho pomanga nkhani. Mbali iliyonse iyenera kuthandizira pomanga thunthu limodzi, iliyonse m’malo ake, iliyonse ikumathandizira mbali yotsatirayo mwa kuikonzera malo. Nthaŵi zonse muyenera kukhala ndi chifukwa chofotokozera mfundo za nkhani yanu m’dongosolo limene mwasankha.
16-20. Kodi munthu angatsimikize motani kuti ali ndi mfundo zoyenerera zokhazokha m’nkhani yake?
16 Kugwiritsa ntchito mfundo zoyenerera zokhazokha. Mfundo iliyonse imene mugwiritsa ntchito iyenera kugwirizana kwambiri ndi nkhaniyo. Ngati siitero, idzaoneka kukhala yosayenerera, idzasoŵa malo; idzakhala mfundo yosafunika, ndiko kuti, yosathandiza kapena yosagwirizana ndi nkhani imene ikukambidwa.
17 Komabe, phungu wanu sadzangofulumira kunena kuti mfundo yakutiyakuti ndi yosayenerera imene kunja ingaoneke ngati yosagwirizana ndi nkhaniyo ngati mgwirizano wake uonekera bwino. Mwina mwasankha kugwiritsa ntchito mfundo imeneyo ndi cholinga chinachake, ndipo ngati igwirizana ndi mutu wa nkhani, ngati ili mbali ya nkhaniyo, ndiponso ngati itchulidwa m’njira yotsatirika, phungu wanu adzaivomereza.
18 Kodi ndi motani mmene mungadziŵire msanga mfundo zosayenerera pokonza nkhani yanu? Apa m’pamene autilaini ya mitu imathandiza kwambiri. Imathandiza kuika mfundo zanu m’magulu. Yesani kugwiritsa ntchito makadi kapena chinachake chofananako, mutalemba mfundo zonse zogwirizana pakadi iliyonse. Tsopano, sanjaninso makadiwo motsatira dongosolo limene mwasankha kufutukulira nkhaniyo. Zimenezo zidzathandiza kuona njira imene mungaperekere nkhaniyo, koma makamaka mudzakhoza kuzindikira chilichonse chosayenerana ndi mutuwo. Mfundo zimene sizipeza malo m’dongosolo limenelo ziyenera kusinthidwa kuti zipeze malo, ngati zili zofunikabe m’nkhaniyo. Koma ngati n’zosafunika, zichotsedwe chifukwa n’zosagwirizana ndi mutuwo.
19 Mwa zimenezi mutha kuona mofulumira kuti mutu wa nkhani yanu, umene mwausankha poganizira omvetsera komanso cholinga chanu, ndiwo umakuonetsani mfundo zoyenerera. Nthaŵi zina mfundo ina ingakhale yofunikira kukwaniritsa cholinga chanu, malinga ndi omvetsera anu, pamene kwa omvetsera ena kapena mutu wina, mfundo imeneyo ingakhale yosafunikira kapena yosayenerera m’pang’ono pomwe.
20 Mwa zonsezo, kodi kalongosoledwe ka mfundo za m’nkhani yanu kayenera kukhala kokwanira motani? Kalankhulidwe kotsatirika ndi kogwirizanika sikayenera kulephera chifukwa choyesa kulongosola mfundo ina iliyonse ya nkhani yanu. M’malo mwake, kukakhala bwino kwambiri kusankha njira imene idzakulolani kufotokoza mfundo zothandiza zokhazokha, pakuti nkhani za wophunzira ndi mbali yolangiza papologalamu ya sukuluyi. Komabe, mfundo zazikulu zothandiza kufutukula mutu wanu siziyenera kusiyidwa.
21. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti pasasiyidwe mfundo yaikulu iliyonse?
21 Kusasiya mfundo zazikulu. Kodi mumadziŵa motani ngati mfundo ili yaikulu kapena ayi? Imakhala yofunika ngati popanda imeneyo simungakwaniritse cholinga cha nkhani yanu. Zimenezo n’zoona makamaka m’nkhani yofuna kuilankhula motsatirika komanso mogwirizanika. Mwachitsanzo, kodi mungakhale bwanji ngati womanga nyumba wakumangirani nyumba yam’mwamba koma sanaike makwerero? Mofananamo, nkhani imene mfundo zina zofunika zasiyidwa poikamba siingakhale yotsatirika ndi yogwirizanika. Chinthu china chikusoŵeka ndipo ena mwa omvetsera adzatayika. Koma zimenezo sizichitika ngati nkhani ikambidwa mogwirizanika komanso motsatirika.