Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fu tsamba 3-32
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
  • M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumene Chithandizo Cheni-Cheni Chingapezeke
  • Chifukwa Chake Kupanda Chisungiko Kukuwononga Moyo wa Anthu
  • MAkonzedwe Amene Akupangitsa M’tsogolo Mosungika Kukhala Mothekera
  • Chisungiko Chimene Chingapezedwe Tsopano
  • Chimene Mungachite
  • Chisungiko Chenicheni—Tsopano Ndiponso Kosatha
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Imene Ikulowetsamo Inu
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
    “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Zayandikira!
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
Onani Zambiri
M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
fu tsamba 3-32

Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere

1. Kodi ndi mtundu wotani wa chisungiko umene mungakonde kaamba ka inu mwini ndi okondedwa anu?

ANTHU a makhalidwe onse a moyo ali ndi chikhumbo chenicheni cha chisungiko. Ndithudi chimenecho ndicho chimene inu mukuchifuna kaamba ka inu mwini inu mwini ndi okondedwa anu. Anthu ochuluka amafuna zoposa chabe lonjezo la mikhalidwe yabwino irinkudza nthawi ina yosatsimikizirika ndi yamtsogolo. Pali mavuto a moyo amwamsanga amene akukumana nafe patsopano lino. Chimene chikufunika ndicho kanthu kena kamene kamapereka chisungiko chenicheni tsopano ndi kamene kadzapitirizabe kutero m’zaka zirinkudzazo. Kodi chisungiko choterocho nchothekera?

2. (a) Kodi Baibulo, pa Yesaya 32:17, 18, limanenanji ponena za chisungiko? (b) Kodi mikhalidwe yotero’yo ikukukondweretsani?

2 Pali anthu amafuko onse, okhala m’mbali zonse zadziko lapansi, amene akukhulupirira kuti nchothekera. Chisungiko chimene chikuwakondweretsa chinafotokozedwa kale-kale ndi mneneri wa Mulungu wouziridwa amene analemba kuti: “Nchito ya chilungamo cheni-cheni iyenera kukhala mtendere; ndi utumiki wa chilungamo chenicheni, bata ndi chisungiko ku nthawi zonse. Ndipo anthu anga ayenera kukhala m’malo okhala amtendere ndi mokhala modalirika kotheratu ndi m’malo opuma osavutitsidwa.” (Yesaya 32:17, 18, NW)a Zikwi mazana ambiri za anthu m’mbali zonse zadziko lapansi zikuyambiratu kusangalala ndi chisungiko chamtendere mosasamala kanthu za chipwirikiti cha dziko chiripochi, ndipo ziri ndi chifukwa choyembekezerera mtsogolo mwaulemerero kwambiri. Inunso mungalandire mapindu oterowo pamodzi nawo.

3. Kodi pali kanthu kena’nso kamene Baibulo limalonjeza kamene kadzachititsa chisungiko kwa mtundu wa anthu? (Chivumbulutso 21: 4, 5)

3 Anthu amenewa akuyembekezera nthawi, imene tsopano iri pafupi kwambiri, pamene ‘kudzakhala kulibe aliyense wopangitsa anthu kunjenjemera’—nthawi pamene kudzakhala mapeto a kuswa lamulo, mapeto a upandu kuchuma cha munthu ndi kwa munthu mwiniyo. (Mika 4:4) Iwo ali ndi chifukwa chomveka chokhulupirika kuti anthu ambiri amene tsopano ali ndi moyo adzawona tsiku pamene njala sidzakhalakonso, chifukwa chakuti “padziko lapansi padzakhala dzinthu zochuluka.” (Salmo 72:16, NW) Ndipo iwo akuyembekezera kuwona iwo eni kukwaniritsidwa kwa lonjezo lakuti ‘Mulungu adzapukuta msozi uliwonse pamaso pawo, ndipo sikudzakhalanso imfa, ngakhale kulira maliro ngakhale mfuu ngakhala zopweteka sizidzakhalako’nso. Zinthu zakale zapita.’ (Chivumbulutso 21: 3, 4). Kodi iwo angatsimikizire motani kuti zinthu zoterozo zidzachitikadi? Chifukwa chakuti malonjezo amenewa akupezeka m’Mawu a Mulungu mwini, Baibulo.

4. Ngakhale kuli kwakuti anthu anagwiritsiridwa ntchito kulemba, kodi n’chifukwa ninji zinthu zolembedwa m’Baibulo ziri kweni-kweni zochokera kwa Mulungu? (2 Timoteo 3:16, 17)

4 Zimene Baibulo limanena ponena zamtsogolo mwathu siziri chabe chotulukapo cha zoyesayesa za anthu kumasulira mikhalidwe ya zochitika za m’dziko. Anthu anagwiritsiridwa ntchito kulemba, koma maganizo awo anatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu. Motero uthengawo ngwochokera kwa Mulungu. Ponena za magwero a zamkati mwake, Baibulo leni-leni’lo limati: “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pachokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.” (2 Petro 1:20, 21) Sikuyenera kukhala kotivuta lerolino kuzindikira mmene Mulungu anachitira zimenezi. Ngakhale anthu opita kutali mumlengalenga atumiza mauthenga kudziko lapansi, ndipo amenewa alandiridwa momvekera bwino kwambiri. Kodi Mulungu kumwamba, mumkhalidwe wapamwamba kwambiri, sakadatumiza mauthenga kwa anthu okhulupirika amene anali ogwirizana naye? Ndithudi! Pamenepo, pokhala ndi chifukwa chabwino, tikukupemphani kuti mupende zimene Baibulo limanena ponena za mmene mungapezere mtsogolo mosungika.

Kumene Chithandizo Cheni-Cheni Chingapezeke

5. Kodi ndi lingaliro lotsimikizirika lotani limene Baibulo limatilimbikitsa kukhala nalo kulinga kundalama ndi chuma china chakuthupi? (Mlaliki 7:12) 

5 Baibulo limatithandiza kuwona moyo motsimikizirika. Ndi cholinga cha ubwino wathu wosatha, limatifulumiza kuika chidaliro chathu m’zimene zidzakhala. Lerolino anthu mamiliyoni ambiri amaika chidaliro chawo m’chuma chakuthupi. Ngakhale kuti likuvomereza phindu la ndalama ndi chuma china chakuthupi, Baibulo limasonyeza kuti zimenezi siziri chinthu chachikulu m’moyo. Limafotokoza chowonadi chosakanika chakuti “ngakhale pamene munthu ali ndi zochuluka moyo wake sumachokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15, NW) Chuma chingataye phindu lake. Icho chingabedwe kapena kuwonongedwa. Moyo wa mwiniyo ungaikidwedi paupandu ndi munthu wina wofuna kuba ndalama zake. Chisungiko chenicheni chiyenera kukhala chiri kwina. Koma kuti?

6. Kodi n’chifukwa ninji sikuli koyenera kuika ziyembekezo zathu zonse za m’tsogolo palonjezo la atsogoleri aumunthu?

6 Pali anthu amene akumanga ziyembekezo zawo zonse zamtsogolo pa zimene ztsogoleri aumunthu akulonjeza. Koma kodi inu muyenera kutero? Popanda ngakhale kutulutsa chikaikiro chakuti kaya atsogoleri ali onse ali oona mtima kapena okhoza, Baibulo likufika pachitima cha nkhaniyo mwa kutikumbutsa kuti iwo onse amafa. Mwanzeru limachenjeza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitaika.” (Salmo 146:3, 4) Motero, kwakukulu-kulu, atsogoleri aumunthu amasonkhezera zochitika za mbali yaing’ono ya mtundu wa anthu kwa zaka zowerengeka zokha. Ponena za chisungiko chosatha, iwo sangakupatseni mofanana ndi mmene iwo eni sangadzipezere.

7. (a) Kodi ndani kweni-kweni ali wokhoza kutipatsa chisungiko chosatha, ndipo kodi n’chifukwa ninji? (Machitidwe 17:28)(b) Kodi tifunikira chiani ngati titi tisangalale ndi chisungiko chimene’cho?

7 Koma pali Mmodzi amene angapereke. Iye ndiye Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansi iri lisanalengedwe, iye analiko; ndipo kwa nthawi yaitali zaka zino za zana la makumi awiri zitatha, iye adzapitiriza kukhalako. Monga momwe Salmo 90:2 limanenera kwa iye kuti: “Inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.” Iye ndiye Magwero a moyo ndi Amene wapatsa Dziko lapansi mphamvu ya kuchirikiza zamoyo. Motero, moyo wathu watsopano lino ndi ziyembekezo zathu za mtsogolo zikudalira pa iye. Ndicho chifukwa chake ife tikufunikira unansi wabwino ndi iye ngati titi tisangalale ndi chisungiko chirichonse chenicheni.

8. (a) Kodi Mulungu akufu-nafuna anthu a mtundu wotani? (b) Chifukwa cha chimene’cho, kodi n’chiyani chimene ife monga anthu tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita m’malo mwakuti tikwaniritse chofunika chimene’cho? (Mateyu 7:21-23)

8 Kodi izi zikutanthauza kuti zonse zimene zikufunika ndizo kukhala ndi chipembedzo china m’moyo wako? Kukakhala kolakwa kunena zimenezo. Awo kwa amene Mulungu akubvomera kuperekako unansi wobvomerezeka ndi iyemwini ali mtundu wina wa anthu. Mtundu wotani? Baibulo limawafotokoza motere: “Olambira oona adzalambira Atate ndi mzimu ndi chowonadi, pakuti, ndithudi Atate akufunafuna otero kuti amlambire. Mulungu ndi Mzimu, ndipo awo omlambira ayenera kulambira ndi mzimu ndi choonadi.” (Yohane 4:23, 24, NW) Kodi ndinu munthu amene amalambira Mulungu ‘ndi choonadi’? Kodi mwapenda zikhulupiriro zanu mothandizidwa ndi Mawu a Mulungu, kuti muone ngati izo zikugwirizana kotheratu ndi zimene zalongosoledwa m’menemo ndi “Mulungu wa choonadi”? (Salmo 31:5) Kodi muli wofunitsitsa kutero? Ziphunzitso ndi machitidwe zimene sizigwirizana ndi choonadi ziribe phindu losatha kwa ali yense. Zimachititsa anthu kunyalanyaza m’mene zinthu ziriri kweni-kweni; zimatsogoza anthu m’njira yolakwa. Chikhutiro chimene chimadza ndi chisungiko cheni-cheni chingapezedwe kokha ngati munthu akufuna’di kudziwa choonadi, ndipo ali wofunitsitsa kupanga masinthidwe pamene akufunikira kuti agwirizanitse moyo wake ndi chowonadi. Chimodzi cha zowonadi zofunika koposa chimalowetsamo kudziwika kwa Mulungu iyemwini.

9. (a) Kodi dzina leni-leni la Mulungu ndani? (b) Kodi ndi lemba liti limene mungaligwiritsire ntchito kuti mutsimikizire kwa bwenzi limene liri dzina la Mulungu?

9 Kodi mukudziwa dzina lake leni-leni? Sindiro ‘Mulungu” kapena “Ambuye.” Amene’wo ali maina aulemu, monga momwedi “Bambo” ndi “Mfumu” aliri maina aulemu. Komabe, malinga ndi kunena kwa Authorized Version of the Bible (lotembenuzidwa mu 1611 C.E.), Salmo 83:18 limati: “Inu, amene dzina lanu lokha liri YEHOVA, ndinu wapamwamba-mwamba pa dziko lonse lapansi.” Iri sindiro dzina limene anthu apatsa Mulungu. Monga momwe kwasonyezedwera mu Revised Version of the Bible (American Standard Edition, yofalitsidwa mu 1901 C.E.), Mulungu akudzinenera yekha pamene akuti: “Ine ndine Yehova, limene’lo ndiro dzina langa.” (Yesaya 42:8) Matembenuzidwe ena a Malemba oyamba Achihebri amatembenuza dzina’lo kukhala “Yahweh.”

10. (a) Kodi n’kofunika kweni-kweni kudziwa ndi kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu? (Machitidwe 15:14) (b) Ngati tikukonda Yehova, kodi ndi motani mmene ife enife tiyenera kugwiritsira nchito dzina limenelo? (Yesaya 43:10)

10 Otembenuza ena angaganizire kuti iwo akupangitsa Baibulo kukhala lolandirika kwa anthu ambiri mwa kusagwiritsira ntchito dzina leni-leni la Mulungu, koma kodi iwo akukhala oona mtima monga otembenuza pemene ayesa kubisa dzina limene limapezeka mobwereza-bwereza kwambiri koposa lina liri lonse m’zolembedwa za chinenero choyamba? Mulungu woona amafuna kuti anthu adziwe dzina lake. Iye anamveketsa chimenechi pamene anauza mtumiki wake Mose kuti auze wolamulira wa Igupto wakale ponena za chifukwa chake Mulungu anam’sungabe kufikira nthawi imene’yo. Kodi chinali chifukwa ninji? Mulungu anati, “Kuti ndikuwonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa padziko lonse lapansi.” (Eksodo 9:16) Nkofunika kuti tigwiritsire ntchito dzina la Mulungu, tikumatero mwaulemu. Ndipo ngati tikukonda chowonadi, sitidzakaikira kuzidziwikitsa monga olambira Yehova, Mulungu woona yekha.

11. Kodi ndi motani mmene Mulungu amaonera kugwiritsiridwa nchito kwa mafano m’kulambira? (Salmo 115:3-5; Deuteronomo 7:25)

11 Komabe, tiyenera kukhala osamala, kuti tisagwirizanitse dzina la Mulungu ndi kanthu kena kamene iye samakabvomereza. Kumbukirani kuti, “Mulungu ndi Mzimu, ndipo awo om’lambira ayenera kulambira ndi mzimu ndi chowonadi.” (Yohane 4:24, NW) Ngati tizindikira cheni-cheni chakuti “Mulungu ndi Mzimu,” ndipo ngati tim’lambira “ndi mzimu,” ndiko kuti, m’njira zauzimu, sitidzagwiritsira ntchito zinthu zakuthupi kuti ziimire Mulungu. ‘Palibe munthu anaona Mulungu,’ malinga ndi kunena kwa Yohane 1:18, motero nkosatheka kupanga chithunzi-thunzi chirichonse kapena fano losema la iye. Fano limene silingathe kuona kapena kumva kapena kulankhula, limene silingatukule ngakhale chala kuti lithandize awo amene akulambira pamaso pake, silingaimire bwino lomwe Mulungu wamoyo. Ndithudi, mafano ena sanalinganizidwe kuti aimire Mulungu mwini’yo, koma funso ndiro, Kodi izo ndizo zinthu zothandizira kulambira? Pamene Mulungu anapereka Malamulo Khumi, iye anafotokoza momveketsa bwino kuti mafano sanayenera kupangidwa kaamba ka chifuno chotero’cho. Iye analamula kuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chirichonse cha zinthu. . . usadzipembedzere izo, usazitumikire izo.” (Eksodo 20:4, 5) Mmalo mwa kugwiritsira kwathu ntchito zinthu zimene Yehova samazivomereza, kukonda chowonadi kudzatithandiza kufika pakudziwa Mulungu monga momwe iye alire kweni-kweni.

12. (a) Kodi Yehova ndi Mulungu wa mtundu wotani? (b) Kodi ndiiti ya mikhalidwe yake imene imakukondweretsani kwenikweni?

12 Mikhalidwe yake iri yakuti iyo imapindula chidaliro cha munthu aliyense amene amakonda chilungamo. Ina ya mikhalidwe imeneyi, yonga ngati mphamvu yaikulu-kulu ndi nzeru zimene zimaposa kwambiri zija za munthu aliyense, nzooneka m’ntchito zake za zinthu zolengedwa. Ndipo kodi simubvomera kuti kukongola kwa kulowa kwa dzuwa, nyimbo yokoma ya mbalame, kununkhira kwa maluwa, ndi kukoma kosiyana-siyana kumene mumasangalala nako zonse zimasonyeza chikondi cha Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu? Koma Baibulo limapitirira pa zimene’zi, likumatiuza zambiri ponena za Mulungu. Limavumbula kuti Yehova amachirikiza chimene chiri cholungama, koma kuti iye alinso wachifundo ndi wolingalira. Limam’fotokoza motere: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.” (Eksodo 34: 6, 7) Ndipo Baibulo limasimba zochita za Mulungu kwa zaka mazana ambiri ndi mtundu wa Israyeli wakale, zochita zimene zimasonyeza mwamphamvu mikhalidwe imene’yo. Mbiri yolembedwa imene’yo imatsimikiziranso kuti “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Iye amafuna kuti mitundu yonse ya anthu isangalale ndi unansi wabwino ndi iye, ndipo iye mokoma mtima wapanga makonzedwe kotero kuti umenewu uli wothekera.

13. Kodi ndi motani m’mene moyo wa munthu umayambukiridwira pamene aika’di chidaliro chake mwa Yehova? (Miyambo 3:5, 6)

13 Pamene munthu akukulitsa kuyamikira mikhalidwe yambiri yabwino ya Mulungu woona, kodi nchiyani chimene chimachitika? “Dzina” la Mulungu limawonjezeka m’tanthauzo kwa iye. Iye amaika chidaliro chake mwa Yehova, akumachita zinthu m’njira ya Mulungu ndipo, chifukwa cha chimene’cho, iye amawona chinjirizo. Kuli monga momwe Miyambo 18:10 imanenera kuti: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.”

14. (a) Kodi n’chifukwa ninji m’tsogolo mwathu mukudalira pa Yehova? (b) Kodi ndi chosankha chachikulu chotani chimene chikuyang’anizana ndi munthu aliyense? (Deuteronomo 30:19, 20)

14 Chinjirizo limene’lo limaphatikizapo ziyembekezo zanu zam’tsogolo. Ndithudi, m’tsogolo mwa mtundu wonse wa anthu mumadalira pa Yehova. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti dziko lapansi’li liri chilengedwe chake ndipo onse amene akukhala pa ilo ali odalira pamakonzedwe ake ochirikiza moyo. M’Baibulo wafotokoza chifuno chake cha kupereka mikhalidwe yokhalira ndi moyo yosungika ndi yosangalatsa kaamba ka anthu ake. Palibe chiri chonse kumwamba kapena padziko lapansi chingaletse Mulungu Wamphamvuyonse kukwaniritsa chifuno chake. Komabe, chifuno chimene’cho sichimatilanda ufulu wa kusankha. Sichimakhazikitsa choikidwiratu cha ali yense wa ife popanda kukhala kwathu ndi chonena chirichonse munkhani’yo. Koma chimatipatsa chosankha chachikulu: Kodi kuyamikira zonse zimene Yehova watichitira, ndi zimene adzachitabe mtsogolo, kumatisonkhezera kugwirizanitsa miyoyo yathu ndi chifuniro chake? Kulephera kwa munthu kukhulupirira sikudzasintha chenicheni chakuti Yehova ndi Mulungu wowona, ndiponso sikudzasintha chifuno Chake. Koma kungatsimikizire kaya ngati munthuyo iyemwini akupindula ndi chifuno chachikondi chimene’cho. Chosankha’cho chiri kweni-kweni pakati pa moyo ndi imfa.

Chifukwa Chake Kupanda Chisungiko Kukuwononga Moyo wa Anthu

15. Kodi ndi zina za zinthu zotani zimene zikupangitsa moyo lero lino kukhala wopanda chisungiko?

15 Kuti tizindikire m’mene chifuno cha Yehova chimachititsira chisungiko cheni-cheni, tingadzikumbutse mopindulitsa choyamba cha zinthu zimene zikupangitsa moyo lerolino kukhala wopanda chisungiko. Pakati pa zimene’zi pali kupanda chikondi, kusalemekeza lamulo, kulephera kulemekeza chuma cha ena, ndi kugwiritsira ntchito mabodza ndi chiwawa kuti munthu apeze zofuna zake. Ndipo’nso, sitinganyalanyaze matenda ndi kuzindikira kuti tsiku lina, kaya posachedwa kapena pambuyo pake anthu amafa. Mwa kukumana nazo kwathu ndi kuwona komwe, tikudziwa m’mene zinthu zimene’zi zimayambukirira moyo wa anthu. Koma kodi zonse’zi zinachitika motani? Yankho likupezeka m’Baibulo.

16. Pachiyambi, kodi n’chiani chimene chinachititsa chisungiko chimene Adamu ndi Hava anali nacho? (Genesis 1:31; 2:8, 15)

16 Bukhu loyamba leni-leni la Baibulo limatiuza kuti pamene Yehova analenga makolo athu oyamba aumunthu, Adamu ndi Hava, ntchito yake inali yabwino kwambiri. Panalibe cholakwika m’kupangidwa kwawo chimene chikanachititsa matenda; pamaso pawo iwo anali ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha. Mwachikondi, Mulungu anawapatsa munda wokongola, paradaiso mu Edeni, monga malo awo okhala. Moolowa manja anaphatikiza m’munda wao wokhala zomera zochuluka zobala mbewu ndi mitengo yobala zipatso kuti ziwachirikize. Iye anadzaza’nso miyoyo yao ndi chifuno mwa kuwauza kulamulira nsomba, mbalame ndi nyama zonse, ndi kulima dziko lapansi ndi kulidzaza ndi ana awo kufikira dziko lonse lapansi litakhala ngati paradaiso amene iye anawaikamo. M’malo otero’wo lingaliro la chisungiko linali kokha lachibadwa. Koma kanthu kena kanafunidwa kwa iwo ngati iwo akanati apitirize kukhalabe ndi chisungiko chimene’cho.

17. (a) Kodi n’chiani chimene chinafunika kwa Adamu ndi Hava ngati iwo akanati apitirize kukhala osungika? (b) Kodi Yehova anayesa kumvera kwao motani, ndipo kodi n’chifukwa ninji chimene’chi chinali nkhani yofunika? (Luka 16:10)

17 Iwo anafunikira kuzindikira malo ao mogwirizana ndi Mulungu. Dziko lapansi ndi zinthu zonse zokhala mu iro zinali za Mlengi wao, motero iye anali ndi kuyenera kwa kusankha m’mene zimenezi zikanagwiritsiridwira ntchito. Moyo weni-weni-‘wo unali mphatso yodalira pakanthu kena; ndiko kuti, Adamu ndi Hava akanapitirizabe kusangalala nawo pokha-pokha ngati iwo akanapitirizabe kukwaniritsa chofunika cha kumvera kwachikondi kwa Atate wawo wakumwamba. Kuti agogomezere ukulu wa chofunika chimenechi, Yehova anaika pa munthu lamulo iri: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Kumvera kukanasonyeza kulandira kwa munthu’yo Mulungu monga Wolamulira; kusamvera kukanatanthauza kukana chifuniro changwiro cha Mulungu. Lamulo limeneli silinalowetsemo vuto lirilonse; silinalande munthu’yo chirichonse chimene iye anachifuna, koma linapereka chiyeso chofewa, komabe champhamvu, chija chimene chinali choyenerera kumikhalidwe imene iye anakhalamo. Linapatsa Adamu ndi mkazi wake Hava mwai wa kusonyeza kukonda kwao Atate wao wakumwamba.

18. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene zikuchititsa kupanda chisungiko zimene zinaonekera choyamba mogwirizana ndi uchimo wa Adamu ndi Hava ndi pambuyo pake? (b) Monga momwe kwafotokozedwera pa Aroma 5:12, kodi ana onse a Adamu ayambukiridwa motani?

18 Cholembedwa cha Baibulo m’Genesis chaputala chachitatu chimasonyeza kuti iwo analephera. Mwadala iwo anadya mtengo umene Mulungu “analetsa.” Chisungiko chimene anthu awiri’wo anali nacho papitapo chinaonongedwa. Zinthu zeni-zeni‘zo zimene zikuchititsa kupanda chisungiko lero lino zinakhalako kwa nthawi yoyamba panthawi imene’yo. Panali kusakonda Mulungu, kusalemekeza lamulo lake ndi kulephera kulemekeza chuma chake. Atakanidwa ndi Mulungu, Adamu ndi Hava anathamangitsidwa mu Edene. Kunja kwa paradaiso, ambiri a ana ao, kuphatikizapo mwana wawo weni-weni Kaini, anakhala oipa moonjezereka pamene anayamba kuchita chiwawa. Ngakhale awo amene sananyalanyaze mwadala lamulo la Mulungu amva m’matupi mwao mwa iwo eni ziyambukiro za cholowa cha uchimo. Monga momwe Aroma 5:12 amafotokozera kuti: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”

19. (a) Kodi chipanduko’cho mu Edene chinayambidwa ndi yani? (Chivumbulutso 12:9) (b) Kodi iye anakhala bwanji Satana ndi Mdyerekezi? (Yakobo 1:14, 15)

19 Komabe, kuyenera kuzindikiridwa kuti, kachitidwe koyamba komka ku chipanduko sikanayambe ndi Adamu kapena mkazi wake. Baibulo likuchula “njoka” kukhala ikulankhula kwa Hava, ikumam’kopa ndi chinyengo kuti aswe lamulo la Mulungu. Ndithudi, njoka yeni-yeni singalankhule; ndipo Baibulo pambuyo pake likusonyeza mphamvu imene inali kutseri kwa njoka imene’yo kukhala munthu wauzimu wosawoneka. Munthu wauzimu amene’yu sanalengedwe kuti akhale woipa. Koma, monga momwe kunaliri ndi anthu, mwana wauzimu wa Mulungu amene’yu anali ndi ufulu wa kusankha, kukhoza kusankha m’mene akagwiritsirira ntchito mphamvu zake. Mwa kulingalira zikhumbo zoipa, iye anakulitsa kunyada; iye anafuna zolengedwa zina kuti zim’lambire monga mulungu. Mwanjira imene iye analondola kuti afikire cholinga chake anadzipanga kukhala wotsutsa Mulungu, Satana, ndi woneneza, Mdyerekezi.

20. (a) Polankhula ndi Hava, kodi ndi mawu otani amene Satana ananena? (b) Kodi n’chifukwa ninji iye sanapititse patsogolo mkhalidwe wake mwa kuchitapo kanthu pa zimene Satana ananena?

20 Iye anafikira Hava, choyamba akumafunsa mafunso ndipo kenako akumatsutsa mwachindunji Mulungu mwa kuuza Hava kuti: “Kufa simudzafai [ngati mutadya mtengo woletsedwa’wo]; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umene’wo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:1-5) Zimene’zi zinamvekera kwa mkazi’yo ngati kanthu kena kabwinopo koposa zimene anali nazo. Koma mwa kuzikhulupirira, kodi iye anapezadi chisungiko chokulirapo? Kodi mwamuna wake anapititsa patsogolo mbali yake mwa kugwirizana naye m’cholakwa? Ai; zonse zinali bodza. Zimene’zi zinatsimikiziridwa kotheratu pamene iwo anafa, ndipo kufikira lerolino anthu akupitiriza kufa.

21. (a) Kodi ndi nkhani zofunika kwambiri zotani zimene zinadzutsidwa mu Edene muja, ndipo kodi zimenezi zimayambukira motani chisungiko cha zolengedwa zonse? (b) M’masiku a Yobu, kodi ndi chinenezo china chotani chimene chinanenedwa, ndipo kodi icho chinatanthauzanji? (Yobu 1:7-12; 2:1-5)

21 Nkhani zofunika zinadzutsidwa mu Edene m’menemo, ndipo zimene’zi zikukhudza chisungiko cha zolengedwa zonse. Kunena zowona kwa Mulungu kunakaikiridwa, ndipo zimene’zi zinakaikiritsa kuyenera ndi kulungama kwa ulamuliro wake. Kunasonyezedwa kuti munthu akakhala bwino kwambiri atamapanga zosankha zake za iye mwini ponena za chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa, atamaika miyezo yake-yake, atamachita monga wodzilamulira. Kupanduka kwa Satana ndi kulephera kwa anthu awiri oyamba’wo kukhala okhulupirika kwa Mulungu kunadzutsa funso lonena za chimene zina za zolengedwa zaluntha za Mulungu zikachita. Kodi aliyense akakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu? Pambuyo pake, m’masiku a munthu’yo Yobu, Satana adanena kuti awo amene anatumikira Mulungu anatero kokha chifukwa cha mapindu awo, osati chifukwa cha chikondi. “Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe?” Satana anatero. (Yobu 1:9) Iye anatanthauza kuti palibe aliyense amene akasunga umphumphu ku ulamuliro wa Yehova ngati iye, mdani wa Mulungu, ataloledwa kumuyesa. Mtundu wa anthu sukanasangalala’nso ndi chisungiko chotheratu kufikira nkhani zimene’zi zitathetsedwa. Komabe, Yehova anadziwa kuti nkhani zimene’zo zikatha kuthetsedwa mokhutiritsa kwambiri okonda chilungamo onse, ndipo iye anapanga makonzedwe okhala ndi cholinga chimene’cho.

MAkonzedwe Amene Akupangitsa M’tsogolo Mosungika Kukhala Mothekera

22. (a) Popereka chiweruzo pa makolo athu oyamba, kodi n’chiyani chimene Yehova anapanga kukhala chothekera kaamba ka ife? (2 Petro 3:9) (b) Kodi makonzedwe a Yehova kaamba ka mtsogolo mwa mtundu mwa anthu akuzikidwa pa yani?

22 Pamene chiweruzo chinaperekedwa pa makolo athu oyamba chifukwa cha kupandukira kwawo Mulungu, Yehova sanaiwale ana ao osabadwa. Mwachikondi iye anapanga chifuno chimene chikupangitsa kukhala kothekera kwa aliyense wa ife kudzisankhira kaya tikufuna kukhala pansi pa ulamuliro waumulungu. Chifuno chimene’cho chikuzikika pa Mwana wa Mulungu Yesu Kristu.

23. (a) Kodi Yesu anali ndi moyo wa mtundu wotani asankhale munthu? (b) Kodi n’chifukwa ninji sitingam’che kukhala Mulungu kapena kukhala wofanana ndi Mulungu? (Yohane 17:3)

23 Mwana amene’yu anali woyamba weni-weni wa zolengedwa za Yehova za kumwamba. Baibulo limatiuza kuti, “Mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko.” (Akolose 1:15-17) Koma panthawi yoikidwa ya Mulungu, Mwana wake anasiya m’mbuyo ulemerero wake wakumwamba ndipo anabadwa mozizwitsa monga munthu padziko lapansi. Mngelo Gabrieli, amene anatumidwa pasadakhale kukanena za kubadwa’ko, sananene kuti mwana wodzabadwayo akakhala Mulungu. M’malo mwake, iye anakulengeza kukhala kubadwa kwa “Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35) Yesu iye mwini sanadziche kukhala Mulungu. Iye sanachite ngati Satana, amene anafuna kulambiridwa. Moonadi iye anati: “Atate ali wamkulu ndi Ine.” (Yohane 14:28) Chifukwa cha chimene’cho, kuti tisangalale ndi unansi woyenera ndi Mulungu wa choonadi, sitiyenera kupereka malo ena anchito kwa Mwana wake, tikumam’cha kukhala Mulungu kapena kukhala wofanana ndi Mulungu.

24. Kodi n’chiyani chimene chinachitidwa ndi kusonyeza kwa Yesu umphumphu wake potsenderezedwa kwambiri monga munthu padziko lapansi?

24 Padziko lapansi pano Yesu anakumana ndi zinthu zimene sanakumane nazo ndi kale lonse. Kumwamba iye anali wopanda liwongo m’kuchita chifuniro cha Atate wake. Koma kodi iye akapitiriza kukhala wokhulupirika monga munthu padziko lapansi, maka-maka ngati iye akanamvetsedwa ululu ndi kunyozedwa kosayenera? Satana anatsimikizira kusonyeza kuti palibe aliyense, ngakhale Mwana wa Mulungu woyambirira amene’yu, akakhala wokhulupirika atayesedwa. Koma Yesu mokhulupirika anamamatira ku Mawu a Mulungu, akumawadalira monga chitsogozo chake, akumawagwira mawu m’kutsutsa chiyeso. Mwamphamvu anakana chitsenderezo cha kuchita cholakwa, kuti: “Choka Satana! Pakuti kwalembedwa, ‘Ndiye Yehova Mulungu wako uyenera kulambira, ndipo ndi kwa iye yekha uyenera kuperekako utumiki wopatulika.’” (Mateyu 4:10, NW) Kufikira ku imfa Yesu anasunga kukhulupirika kwake kwa Yehova monga Wolamulira, ndipo kumene’ku pansi pa ziyeso zowawa kwambiri koposa chiri chonse chimene Adamu anakumana nacho. M’njira imene’yi Yesu anachotsera dzina la Atate wake zinenezo zonama zimene zinanenedwa ndi Satana. Yesu anatisonyeza m’mene tingalakire ziyeso mwa chitsanzo chake, ndi m’mene tingasonyezere kuti ife nafenso tiri ochirikiza okhulupirika a ulamuliro wa Yehova.

25. Kodi n’chiyani’nso china chimene chinatuluka mu imfa ya Yesu monga munthu wangwiro, ndipo kodi chimene’cho chimapangitsa chiani kukhala chothekera kwa ife? (1 Timoteo 2:3-6)

25 Komabe, zambiri koposa chabe chitsanzo chabwino kwambiri zinaperekedwa kaamba ka ife ndi Mwana wa Mulungu. Yesu iye mwini anafotokoza kuti anadza “kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.” (Marko 10:45) Kumene’ku kunali kofunika ngati mtundu wa anthu ukanati udzachotseredwe uchimo, ndi matenda ndi imfa zimene zinachokera m’kuchimwa. Malinga ndi kunena kwa lamulo la Mulungu, mtengo wa dipo uyenera kukhala moyo wangwiro wa munthu, kuti ulingane ndi moyo wangwiro wa munthu wotayidwa ndi Adamu. Palibe mbadwa yopanda ungwiro ya Adamu ikadaupereka. Mwachikondi Yehova iyemwini anapanga makonzedwe’wo. Anatuma Mwana wake wa iyemwini kudziko lapansi. Ndiyeno, motsatizana ndi imfa ya Yesu, Mulungu anamuukitsira’nso kumoyo, tsopano monga munthu wauzimu, ndipo analandira mtengo wa moyo wake waumunthu monga nsembe ya mtundu wa anthu. Imene’yi inatitsegulira mwawi wa kupeza’nso chimene Adamu anataya. Monga momwe Baibulo limafotokozera kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ha, zimene’zo zikutitheketsera ziyembekezo zabwino kwambiri chotani nanga, ngati tingasonyeze chikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, tikumaphunzira zimene anaphunzitsa ndi kukhala ndi moyo mogwirizana nazo kotheratu!

26. (a) Kodi n’chifukwa ninji Yesu sanalowe m’zochitika za ndale zadziko? (Yohane 18:36) (b) Kodi ndi mkhalidwe wotani ponena za maboma umene Yesu anaphunzitsa atsatiri ake kukhala nao? (Mateyu 22:17-21)

26 Chikhulupiriro chotero’cho chimaphatikizapo kuzindikira ntchito imene Yehova wapereka kwa Mwana wake m’boma. Yesu sanalowe m’zochitika za ndale za dziko za m’nthawi yake; anadziwa kuti palibe boma liri lonse la anthu linachirikiza ulamuliro wa Yehova. Mosasamala kanthu za chimene olamulira otero’wo anganene ponena za kukhulupirira mwa Mulungu, iwo onse anali kuika miyezo yao ya iwo eni yonena za chabwino ndi choipa. Motero, kaya anadziwa kapena ai, iwo onse anali kutsatira chitsogozo cha mdani wa Mulungu, Satana Mdierekezi, amene Baibulo limam’dziwikitsa kukhala “wolamulira wa dziko lapansi.” (Yohane 14:30, NW) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kukhoma misonkho yawo, kukhala omvera malamulo, malinga ngati Mulungu analola maboma a anthu kukhalapo. Koma anamveketsa bwino lomwe kuti chiyembekezo chokha kaamba ka mtsogolo mosungika chiri mwa njira ya Ufumu wa Mulungu, boma lolungama kwambiri logwira nchito liri kumwamba kweni-kweni’ko ndi kumachita ulamuliro pamtundu wonse wa anthu. Chifukwa cha chimene’cho, anawaphunzitsa kupemphera kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” Yesu anawafulumiza kukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo a Ufumu umene’wo monga momwe aperekedwera m’Baibulo. Ndipo iye anawalamula kulalikira “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu” kwa anthu kuli-konse.—Mateyu 6:10; 24:14, NW.

27. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, ndipo kodi tingasonyeze motani kuuyamikira kwathu? (Mateyu 6:33)

27 Ufumu umene’wo ndiwo chida cha Yehova chokwaniritsira chifuniro chake. Udzagwirizanitsa zolengedwa zonse zaluntha kachiwiri pansi pa ufumu wa Yehova. Ophatikizidwa m’kukhala ziwalo za boma lakumwamba limene’lo adzakhala anthu otengedwa m’dziko lapansi lino amene asonyeza kukhulupirika kwa chichirikizo chawo chokhulupirika ku uchifumu wa Yehova, ulamuliro wake. Amene’wa akutchedwa “kagulu kankhosa.” (Luka 12:32) Bukhu lotsirizira la Baibulo limasonyeza kuti iwo ali olekezera ku “zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, ogulidwa kuchokera kudziko.” (Chivumbulutso 14:1, 3) Komabe, wamkulu kwa amene mphamvu ya Ufumu yaperekedwa, ndiye Mwana weni-weni wa Mulungu Yesu Kristu. Mokwaniritsa ulosi waumulungu, iye ndiye amene Yehova akuperekako “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, am’tumikire.” (Danieli 7:13, 14) N’kofunika kwambiri kwa ali yense wa ife kukhala ndi moyo mogwirizana kwambiri ndi kakonzedwe kaumulungu kamene’ko. Awo amene akukana kutero sadzaloledwa kosatha kuwononga chisungiko cha ena.

28. (a) Kodi ulamuliro wa anthu wakhala kwa utali wotani, ndipo kodi n’chifukwa ninji siudzapitiriza kwa nthawi yaitali kwambiri tsopano? (Yeremiya 17:5) (b) Kodi zimene’zi zidzatanthauzanji kwa Satana? (c) Kodi n’chiani chimene chidzachitikira maboma a anthu? (d) Kodi n’chiyani chimene chidzachitikira anthu oipa? (e) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira awo amene ali onyalanyaza ulamuliro wa Yehova? (2 Atesalonika 1:6-9)

28 Chiyambire chipanduko’cho mu Edene, anthu akhala ndi zaka zikwi zisanu ndi chimodzi za kulawa zipatso za ulamuliro wa anthu. Wakhala tsoka. Moyenerera, Baibulo limasonya kumbadwo uno kukhala umene m’kati mwake Mulungu adzapereka ziweruzo zake. Kodi chimene’chi chidzatanthauzanji kwa mdani wamkulu wa mtundu wa anthu, Satana Mdyerekezi? Iye ndi ziwanda zake adzasiyitsidwa kugwira ntchito kotheratu, ‘ataponyedwa m’phompho’, osakhoza kusocheza mtundu wa anthu. (Chivumbulutso 20:1-3) Kodi kuperekedwa kwa ziweruzo za Mulungu kudzatanthauzanji kumaboma a anthu? Baibulo likuneneratu kuti, “Ufumu’wo . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu [a anthu] onse’wa ndipo uwo wokha udzakhala kunthawi zosatha.” (Danieli 2:44, NW) Kodi kudzatanthauzanji kwa onama, mbala, ndi awo amene amachita chiwawa? “Woipa adzatha psyiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzipeza palibe.” (Salmo 37:10) Kodi kudzatanthauzanji kwa awo amene mwamphwayi amanyalanyaza ulamuliro wa Yehova? M’masiku a Nowa, “sanadziwa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse,” ndipo kudzakhala kofanana tsopano pamene Mulungu agwiritsira ntchito Mwana wake kupereka chiweruzo cholungama.—Mateyu 24:39.

29. Kodi zonsezi zidzatanthauzanji kwa ochirikiza okhulupirika a ulamuliro wa Yehova? (Chivumbulutso 7:9, 10, 13, 14)

29 Koma kodi zonse’zi zidzatanthauzanji kwa awo amene asonyeza kuti iwo ali ochirikizi okhulupirika a ulamuliro wa Yehova? Zidzatanthauza chipulumutso kulowa m’dongosolo latsopano lolungama la Mulungu. M’zochita za Mulungu ndi mtundu wakale wa Israyeli, chitsanzo chinaperekedwa cha chiyambukiro chimene chimene’chi chidzakhala nacho pamoyo. Kunachitika monga momwe’di Mulungu anafotokozera Mose kunena kuti: “Muyenera . . . kukhala m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga chuma, ndipo ndithudi iye adzakupatsani mpumulo kwa adani anu onse okuzingani, ndipo mudzakhaladi mosungika.” (Deuteronomo 12:10, NW) Ponena za mikhalidwe mkati mwa kulamulira kwa Mfumu Solomo, kunalembedwa kuti: “Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pampesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani [kutali ku mpoto] mpaka ku Beeriseba [kum’mwera].” (1 Mafumu 4:25) Mogwirizana ndi lamulo la Mulungu, banja liri lonse linali ndi malo akeake olima ndi okhalapo. Kumvera Mulungu kunachititsa dalitso lake, ndipo, monga momwe iye analonjezera, limene’li linaphatikizapo ‘mvula ya dziko’lo panyengo yake.’ (Deuteronomo 11:13-15) Munali chisungiko cha chuma.

30. Monga momwe kwafotokozedwera mu Salmo 72, kodi ndi mikhalidwe yotani imene imachititsa chisungiko imene idzapezeka padziko lonse lapansi pansi pa Ufumu wa Mulungu?

30 Zimene’zo zinalembedwa m’Baibulo, osati chabe monga cholembedwa cha m’mbiri basi, koma kaamba ka chilimbikitso chathu. Ambuye Yesu Kristu, uyo amene Yehova wamuika kukhala mfumu padziko lonse lapansi, akuchedwa m’Malemba kukhala “woposa Solomo.” (Luka 11:31) M’kulamulira kwa Kristu, mikhalidwe yabwino kwambiri’di koposa ija imene inali mu Yuda ndi Israyeli m’kati mwa masiku a Solomo idzafika padziko lonse lapansi. Salmo 72 limafotokoza mokondweretsa madalitso’wo motere: “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita Ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje [Firate] kufikira malekezero a dziko lapansi. Adzaombola moyo wawo kuchinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wamtengo pamaso pake. M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pamapiri.” (Salmo 72:7, 8, 14, 16) Mkhalidwe umene udzakhala panthawi imeneyo udzakhala umene unafotokozedwa ndi Yesu Kristu kwa munthu wina amene anapempha kuti akumbukiridwe pamene Yesu analowa mu Ufumu wake. Yesu anamuuza kuti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:43.

31. (a) Kodi kudzakhala kothekera motani ngakhale kwa akufa kupindula ndi makonzedwe abwino kwambiri amene’wa? (b) Kodi oukitsidwa’wo adzakhala akubwerera kuchokera kuti? (Ezekieli 18:4; Yobu 14:13)

31 Awo amene angakhale atamwalira kale chifukwa cha kulandira kwawo uchimo kuchokera kwa Adamu sadzaiwalidwa panthawi imene’yo. Iwo’nso akuphatikizidwa munsembe ya dipo ya Mwana wa Mulungu. Baibulo limaneneratu molimbikitsa kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Kodi zimene’zi zikutanthauzanji? Baibulo limanena kuti “amoyo adziwa kuti adzafa; koma ponena za akufa, sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5, NW) Iwo ali opanda moyo m’manda. Pamenepo, chiukiriro, chimatanthuza kubwerera’nso kumoyo. Kupatulapo awo a “kagulu ka nkhosa” amene adzakhala ndi moyo wakumwamba limodzi ndi Yesu Kristu, awo onse oukitsidwa adzakhala mu mpangidwe wa anthu, ali ndi chiyembekezo pamaso pao cha kukhala ndi moyo kwamuyaya padziko lapansi pompano.

32. (a) Kodi matenda ndi imfa zidzachotsedwa mwanjira yotani? (b) Kodi inu mwini mukufuna kupindula ndi makonzedwe amenewa amene Yehova wapereka kaamba ka m’tsogolo mosungika?

32 Imene’yi idzakhala nthawi ya kubwezeretsedwa kwa banja laumunthu kumkhalidwe woyamba. Motsogozedwa ndi Ufumu wakumwamba chizindikiro chiri chonse cha uchimo ndi ziyambukiro zake zonse zidzachotsedwa mwa kugwiritsira ntchito phindu la nsembe ya Yesu kwa onse amene akusonyeza chikhulupiriro. Pamene anali padziko lapansi, Yesu anasonyeza chimene ichi chikatanthuza kwa mtundu wa anthu. Anachiritsa mtundu uliwonse wa matenda, ngakhale kubwezeretsa kuwona kwa akhungu ndi kuchiza opunduka. M’dongosolo latsopano la Mulungu dziko lapansi lidzadzaza anthu amene adzalandira madalitso otero’wo. Lonjezo laumulungu ndiro: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhala’nso imfa; ndipo sipadzakhala’nso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyamba’zo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Inde, zinthu zonse zimene zapangitsa moyo kukhala wopanda chisungiko zidzakhala kulibe!

33. Kodi pali chisungiko cheni-cheni chiri chonse chimene cingapezedwe pa tsopano lino?

33 Koma si chiri chonse chimene chimachititsa chisungiko chasungidwira mtsogolo. Zambiri zingapezedwe patsopano lino.

Chisungiko Chimene Chingapezedwe Tsopano

34. Kodi ndi zinthu zotani zochulidwa pano zimene zikachititsa chisungiko chanu chachikulu?

34 Mosasamala kanthu za mikhalidwe ina imene munthu ayenera kukumana nayo m’moyo, anthu ochuluka adzabvomereza kuti munthu aliyense amene chakudya cha tsiku ndi tsiku ndi zobvala zokwanira zatsimikiziridwa kwa iye amakhala ndi chisungiko chachikulu kwambiri. Ndipo’nso, ngati, anthu amene iye kwakukulu-kulu amakhala nawo ali ndi chikondi cheni-cheni kwa wina ndi mnzake, chimene’chi chikawonjezera mbali ina kuchisungiko chimene’cho. Ndipo ngati anadziwa zimene ziri m’tsogolo, zimene’zi, nazo’nso, zikathandizira kuchepetsa pang’ono lingaliro liri lonse la kusatsimikizira. Koma unyinji wa anthu sukusangalala ndi lingaliro la chisungiko lotero’lo. Kodi zimene’zo zikutanthauza kuti malonjezo a chisungiko operekedwa m’Mau a Mulungu adzakwaniritsidwa kokha m’tsogolo? Kapena kodi anthu ngakhale tsopano angapeze chisungiko mwa kukhulupirira malonjezo amene’wo ndi kuchita mogwirizana nawo? Kodi pali anthu amene tsopano akutero mogwirizana?

35. (a) Kodi ndi pansi pa mikhalidwe yotani imene Mulungu amanena kuti adzapereka chakudya cha tsiku ndi tsiku ndi zobvala pa tsopano lino? (b) Kodi ndani amene ali ndi chisungiko chotero’cho, ndipo kodi iwo amapeza motani makonzedwe amene’wa? (Aefeso 4:28)

35 Akristu awo ochedwa Mboni za Yehova apeza Mawu a Mulungu kukhala oona ndipo aona kuti kuwagwiritsira ntchito m’miyoyo yao kumadzetsa mapindu abwino kwambiri patsopano lino. Mapindu amene’wo amachokera m’kupereka kufunika koyenera ku zinthu zauzimu m’moyo wanu wa tsiku ndi tsiku. Ndithudi, munthu aliyense padziko lapansi, kaya ngwokonda zauzimu kapena ai, angapindule ndi zimene dziko lapansi limatulutsa. Koma Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amakhala ndi chikondwerero chapadera m’thanzi la awo amene amaika utumiki wake poyamba. Kuti alimbikitse chikhulupiriro cha ophunzira ake, Yesu anati: “Musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimene’zo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimene’zo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimene’zo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:31-33) Koma kodi iwo amapeza motani zinthu “zonse zimene’zo,” zimene zikufunika kuti zichirikize munthu m’njira yakuthupi? Sikuli kwakuti mpingo Wachikristu umawachirikiza mwandalama. M’malo mwake, iwo onse ali ogwira ntchito ofunitsitsa. Ndipo, pamene anthu apanga’di Ufumu wa Yehova ndi chilungamo chake kukhala zinthu zazikulu m’miyoyo yawo, Mulungu amadalitsa zoyesa-yesa zao za kupeza zofunika zamoyo. Amayankha pemphero lao la “mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.” (Mateyu 6:11) Yehova sakulonjeza atumiki ake chuma chochuluka pamene dziko la lero lino liripobe, koma amawatsimikiziritsa kuti iwo adzapeza zimene kweni-kweni akuzisowa. Ndipo palibe winanso amene ali wokhoza bwino kuona kuti iwo akuzipeza.

36. (a) Kodi ndi mitundu yotani ya khalidwe ndi mkhalidwe imene imatulutsa kupanda chisungiko? (b) Kwakukulu-kulu, kodi ndi mkhalidwe wotani umene ukusoweka pakati pa anthu a mtundu umene’wo? (c) Kodi n’kuti kumene Yesu ananena kuti chikondi chotero’cho chikapezedwa?

36 Wopereka zosowa zakuthupi wamkulu’yo amapangitsa’nso kanthu kena’nso kupezeka kamene kali kofunika kuchisungiko tsopano. Monga momwe mungazindikirire bwino lomwe, kukhala ndi zofunika za moyo zakuthupi sikudzapangitsa munthu kuona kukhala wokhutira ndi wosungika ngati atsamwali ake ali anthu amene alibe chikondwerero cheni-cheni mwa iye. Kupanda chisungiko kumawonjezeredwa pamene anthu amanena bodza ndi kunyenga; pamene agwiritsira ntchito lirime lawo mosadera nkhawa kweni-kweni malingaliro a ena; pamene alingalira ena chifukwa cha chuma chakuthupi; kawonekedwe ka khungu kapena mtundu wake; ndi pamene “kukoma mtima” kumasonkhezeredwa kawiri-kawiri ndi cholinga chobisika ndi chadyera. Chimene chikusoweka kwambiri pakati pa anthu a mtundu umene’wo ndicho chikondi-nkhawa yeni-yeni yopanda dyera kaamba ka anthu ena. Kodi chikondi chotero’cho chingapezedwedi-osati chabe pakati pa anthu owerengeka, koma monga mkhalidwe wapadera wa gulu lonse la anthu? Yesu Kristu akutitsimikiziritsa kuti chingapezedwe’di. Iye anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” Ndipo iye anadziwa kuti kudzakhala anthu otero’wo m’tsiku lathu, chifukwa chakuti anauza ophunzira ake kuti: “Onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.”—Yohane 13:35; Mateyu 28:20.

37. Kodi Baibulo limatithandiza motani kudziwa amene ali ndi chikondi chotero’cho? (1 Yohane 4:20, 21)

37 Ngati mwaona kuti chikondi chimene’chi chikusoweka pakati pa atsamwali anu, pamenepo mufunikira kuyang’ana kwina. Baibulo, pa 1 Yohane 4:8, likupereka chitsogozo chofunika’cho, kuti: “Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” Motero, ndipo pakati pa anthu amene ‘akudziwa Mulungu’ pamene chikondi chotero’cho chingapezedwe. Ndithudi izi sizikutanthauza kuti mudzachipeza pakati pa awo amene akudziwa Yehova, Mulungu woona yekha, amene amachitira ulemu dzina lake ndi amene moona mtima amayesa kugwirizanitsa miyoyo yao ndi chifuniro chake. Mapindu ochokera m’gulu lotero’lo ali oonekera.

38. Kuphatikiza pakungokhala pakati pa anthu otero’wo, kodi n’chiani’nso chimene munthu angachite chimene chidzachititsa chisungiko chake ndi kusangalala kwake ndi moyo?

38 Ndithudi, m’njira imene’yi munthu samakhala wosayambukiridwa ndi ziyambukiro za khalidwe loipa la mbali ina yonse ya dziko lapansi. Komabe, pamene iye mwini abvomereza kudalira kwake pa Mulungu nalandira kotheratu muyezo wa Mulungu wa choyenera ndi cholakwa monga momwe waperekedwera m’Baibulo, amapindula kwambiri. Iye amachinjirizidwa kulowa m’zochitika zimene zikachititsa kokha zobvuta ndi chisoni. Monga momwe Miyambo 1:33 imanenera kuti: “Koma wondimvera ine [ndiko kuti, nzeru yaumulungu] adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.” Moyo wake ungathe kukhala wodzazidwa ndi tanthauzo leni-leni ngati augwiritsira ntchito mogwirizana ndi chifuniro cha Mlengi. M’malo mwa kuona kugwiritsidwa mwala kumene anthu ambiri-mbiri amakuwona, iye angapeze chisangalalo chimene chimachokera m’kuthandiza ena kudziwa chothetsera cheni-cheni chimodzi chokha mavuto a mtundu wa anthu—ufumu wa Mulungu. Yesu Kristu ananeneratu ntchito yotero’yo, kuti: “Mbiri yabwino imene’yi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14, NW.

39. Kodi ndi motani m’mene Mboni za Yehova zimalingalirira ponena zam’tsogolo, ndipo kodi n’chifukwa ninji? (Luka 21:28-32)

39 Pamene awo amene akulowa m’ntchito yolalikira imene’yi akuyang’ana m’tsogolo, iwo sakudzazidwa ndi mantha. Pokhala ataphunzira Baibulo, ndi kukhulupirira zimene limanena, iwo akudziwa zimene ziri mtsogolo. M’malo mwa kukhala ogwiritsidwa mwala ndi chochitika chirichonse chosakondweretsa m’zochitika zadziko, iwo amaona m’zinthu zimene’zi kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo onena za mapeto a dongosolo la zinthu iri. Iwo akudziwa kuti posachedwapa, mu mbadwo uno, Mulungu adzawononga onse amene akupitiriza kunyalanyaza ulamuliro wake woyenera ndi amene akuumirira kuwononga kusangalala ndi moyo kwa anthu anzao. Iwo akuyembekezera mwachidaliro kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo choperekedwa pa 2 Petro 3:13, (NW), amene akuti: “Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuziyembekezera monga mwa lonjezo lake, ndipo m’zimenezi mudzakhala chilungamo.”

40, 41. (a) Motero, kodi n’chifukwa ninji kuli kwakuti Mboni za Yehova zimasangalala ndi chisungiko chachikulu kwambiri pa tsopano lino, ngakhale kuli kwakuti zikukhala m’kati mwa dziko lovutika? (b) Kodi chisungiko chimene Mboni za Yehova ziri nacho chiri kanthu kena kamene inu mukukafuna?

40 Umene’wo ndiwo mtundu wa chisungiko chimene olambira Achikristu a Yehova Mulungu akusangalala nacho pa tsopano lino, awo amene “akulambira Atate ndi mzimu ndi chowonadi.” Chikuchokera m’kugonjera kwawo kumiyezo yolungama ya Yehova ndi kuigwiritsira ntchito m’miyoyo yawo. Monga momwe kunanenedweratu pa Yesaya 32:17, 18, (NW), kuti “Ntchito ya chilungamo cheni-cheni iyenera kukhala mtendere; ndi utumiki wa chilungamo chenicheni, bata ndi chisungiko kunthawi zonse. Ndipo anthu anga ayenera kukhala m’malo okhala amtendere ndi mokhala modalirika kotheratu ndi m’malo opuma osavutitsidwa.” Iwo ali achirikizi okhulupirika a ulamuliro wa Yehova. Iwo samaika miyezo yao-yao ya chabwino ndi choipa. Iwo sakuyesa kuthetsa mabvuto adziko lapansi mwa iwo okha. Moyamikira iwo akulandira ndi kuchirikiza makonzedwe achikondi amene Yehova wapereka, Ufumu wake wokhala m’manja mwa Yesu Kristu.

41 Kodi mungafune kukhala ndi chisungiko chimene iwo ali nacho? Inu mungathe.

Chimene Mungachite

42. Mwa kupita ku King’idomu Holo ya Mboni za Yehova, kodi mudzakhala okhoza kudzionera chiyani?

42 Limodzi la masitepe oyamba ndiro kusonkhana ndi anthu amene akusangalala ndi chisungiko chotero’cho. M’njira imene’yi mungadziwonere nokha kaya ngati ichi ndicho chimene kweni-kweni mwakhala mukufuna-funa. Mboni za Yehova zikukubvomerani mokondwera kudza kumisonkhano yawo pa King’idomu Holo m’dera lanu. Mudzapeza kuti misonkhano yawo sinadzazidwe ndi miyambo yochitira, ndipo palibe mbale ya zopereka imene imayendetsedwa. M’malo mwake, mumakhala kukambitsiridwa kwatanthauzo kwa Mawu a Mulungu ndi m’mene amakhudzira miyoyo yathu. Baibulo limalangiza kuti: “Tiyeni tilingalirane kuti tifulumizane kuchikondi ndi nchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga momwe ena aliri ndi chizolowezi, koma kulimbikitsana.” (Ahebri 10:24, 25, NW) Ndiwo mkhalidwe umene’wu umene mudzaupeza pa pa King’idomu Holo.

43. (a) Ngati inu eni muti mukhale ndi chisungiko chimene mukuchiwona m’miyoyo ya ena pa King’idomu Holo, kodi mufunikira chiani? (b) Kodi n’chifukwa ninji palibe ali yense wa ife angayerekezere unansi wotero’wo kukhala womuyenerera, koma kodi uwo ungapezedwe motani?

43 Kufika pamisonkhano yotero’yo kudzakukhozetsani kuwona chisungiko chimene ena akusangalala nacho, ndipo mosakaikira inu mudzasangalala ndi utsamwali. Koma kanthu kena’nso kakufunika ngati inu eni muti mukhale ndi chisungiko chotero’cho. Chosowa chanu chachikulu koposa ndicho unansi wobvomerezedwa ndi Yehova Mulungu. Iye ndiye Amene moyo wanu watsopano lino ndi ziyembekezo zanu zonse za mtsogolo zomwe zimadalira. Unansi wotero’wo suli kanthu kena kamene ali yense wa ife angayerekezere kukhala komuyenerera. Ife sitinabadwe nawo. Tonsefe ndife mbadwa za Adamu wochimwa, chifukwa cha chimene’cho tinabadwira m’banja laumunthu limene liri lotalikirana ndi Mulungu. Kuti tipeze chiyanjo cha Yehova, tifunikira kukhala oyanjana naye, ndipo kumene’ku nkothekera kokha pamaziko a chikhulupiriro m’makonzedwe achikondi amene iye wapereka kupyolera mwa nsembe ya Mwana wake. Monga momwe Yesu iye mwini ananenera kuti: “Ine ndine njira choonadi ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate kusiyapo kudzera mwa ine.”—Yohane 14:6, NW.

44. (a) Kodi n’chiani chimene tifunikira kuchizindikira choyamba ponena za moyo ndi m’mene miyoyo yathu iyenera kugwiritsidwira ntchito? (Chivumbulutso 4:11) (b) Kuti tikondweretse Yehova, kodi ife enife tiyenera kum’lingalira motani? (c) Kodi nchifukwa ninji ubatizo wa m’madzi uli wofunika, ndipo kodi n’chiyani chimene chiri chofunika munthu asanakonzekere kubatizidwa?

44 Tifunikira kuzindikira kuti miyoyo yathu tinailandira kuchokera kwa Mulungu ndi kuti kulephera kuli konse kugwiritsira ntchito miyoyo yathu momvera Mulungu n’kulakwa. Ngati ife moona mtima tikumva chisoni ndi kulephera kuli konse kwa nthawi yapita’yo kugwiritsira ntchito miyoyo yathu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu tidzakana njira yolakwa imene’yo ndi kupotoloka kotheratu, tikumagwirizanitsa miyoyo yathu ndi chifuniro cha Mulungu. Ichi chikuphatikizapo kuchita chimene Yesu anati ophunzira ake ayenera kuchita, ndiko kuti, ‘kudzikana.’ (Mateyu 16:24) Munthu amene akuchita chimene’chi samanena’nso kuti iye ali ndi “kuyenera” kwa kukhala ndi moyo wake kuti angokhutiritsa zikhumbo zake za iyemwini, osadera nkhawa iriyonse ndi chifuniro cha Mulungu. M’malo mwake, iye amadzipereka kotheratu ku kuchita chifuniro cha Mulungu monga momwe chasonyezedwera ndi Mwana wake. Ndipo iye amachita chimene’chi chifukwa chakuti icho n’choyenera ndi chifukwa chakuti iye wakhutiritsidwa maganizo kuti chirichonse chimene Yehova amachita chiri ndi chifuno chabwino ndi cholungama, ndi kuti chimene Mulungu amachita chimachititsa madalitso kwa ife ngati tikukonda chilungamo. Iye amakonda Yehova moonadi ‘ndi mtima wake wonse, maganizo, moyo ndi nyonga.’ (Marko 12:29, 30) Atapanga chowinda chotero’cho mu mtima mwake, iye amakhala wokonzeka kudzionetsera kaamba ka ubatizo wa m’madzi wapoyera, motsanzira Yesu Kristu ndi momvera malangizo amene iye anapereka kwa ophunzira ake. Munthu angalowe muunansi wovomerezedwa ndi Mulungu woona ndi kukhala ndi chisungiko chimene atumiki woona ndi kukhala ndi chisungiko chimene atumiki ake akusangalala nacho, kokha mwa njira yosonyezedwa m’Mawu a Mulungu imeneyi.

45. Kodi timasonyeza motani kuti tikufuna’di Yehova kukhala Wolamulira wathu?

45 Pambuyo pake, n’kofunika kwambiri kupitiriza kusonyeza kuti inu mwakana’di njira yanuyanu yochirikizidwa ndi Satana; kuti simukukhazikitsa muyezo wanu wa inu mwini wa chabwino ndi choipa; kuti mukufuna kweni-kweni Yehova kukhala Wolamulira wanu. Mudzafunikira kuchita monga kwafotokozedwera pa Miyambo 3:5, 6, kuti: Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” Inde, adzaongola mayendedwe anu m’njira ya chisungiko cheni-cheni ndi chosatha.

46. Kodi ndi chisungiko chotani chimene chimadza kwa awo amene amalandira moonadi makonzedwe achikondi a Yehova?

46 Ha, ndi madalitso akulu chotani nanga amene amadza kwa onse amene moonadi akulandira makonzedwe achikondi amene Yehova walinganizira mtundu wa anthu! Poima zolimba pansi pa ulamuliro wake, iwo akutetezeredwa tsopano, ndipo ali ndi ziyembekezo zotsimikizirika za m’tsogolo. Chifukwa cha kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova ndi kunena kwake zowona, iwo adzalandira chisungiko chokhutiritsa kwambiri chimene chidzadza kwa mtundu wa anthu pansi pa Ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Mwana wake Yesu Kristu.

[Mawu a M’munsi]

a Kusiyapo ngati kwasonyezedwa mwanjira ina, mau ogwidwa a Malemba m’kabukhu’ka ngochokera m’Baibulo Lachicnyanja (Revised Union Nyanja Version ndi New World Translation of the Holy Scriptures, (NW) akumakhala chidule chake.

[Chithunzi patsamba 4]

Anthu okhala ndi moyo tsopano adzaona tsiku pamene njala sidzakhalako’nso

[Chithunzi patsamba 7]

Ziyembekezo zathu zamtsogolo zimadalira pa Uyo amene analenga miyamba ndi dziko lapansi

[Chithunzi patsamba 13]

Mbiri yolembedwa ya Baibulo yonena za makolo athu oyamba imasonyeza chifukwa chake kupanda chisungiko kumaipitsira moyo wa anthu lerolino

[Chithunzi patsamba 21]

Pansi pa Ufumu wa Mulungu padzakhala mapeto a kuswa lamulo, mapeto a upandu ku chuma cha munthu ndi munthu mwini’yo

[Chithunzi patsamba 24]

Mawu a Mulungu amalonjeza kuti matenda ndi imfa zidzachotsedwa—inde, ngakhale okondedwa amene amwalira adzaukitsidwa kudzakhala’nso ndi moyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena