Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kn36 tsamba 1-3
  • Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?
  • Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwononga Zinthu Zachilengedwe
  • Matenda
  • Umphaŵi
  • Nkhondo
  • Zaka 1000 Zimene Zidzadalitsa Mtundu wa Anthu
  • Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo!
  • Zaka Chikwi Zopambana Zikuyandikira
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi N’kupupuluma Kapena Kuzengereza?
    Galamukani!—1999
  • Kodi Zaka za Chikwi Chachitatu Zidzayamba Liti?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Limbikitsani Chidwi Chokopedwa ndi Uthenga wa Ufumu Na. 36
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Onani Zambiri
Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?
kn36 tsamba 1-3

Uthenga wa Ufuma Na. 36

Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?

ZAKA 1000 Zatsopano—Kodi N’chiyambi cha Nyengo Yatsopanodi?

PAKATI pa usiku wa December 31, 1999, zaka za ma 1900 zinatha.a Zaka 100 zimenezo zinali nthaŵi yachipwirikiti chokhachokha. Komanso inali nthaŵi imene kunayambika maluso atsopano opanga zinthu, kutsogola kwadzaoneni m’zamankhwala, kuchuluka kwa chidziŵitso, ndi kutukuka msanga kwa chuma cha padziko lonse. N’chifukwa chake anthu ambiri akuganiza kuti zaka 1000 zatsopanozi zikutipatsa chiyembekezo komanso kuti zidzasintha zinthu. Kodi mwina nkhondo, umphaŵi, kuwononga chilengedwe, ndi matenda zidzatha m’nyengo imeneyi?

Ambiri akuganiza choncho. Koma kodi n’zothekadi kuti zaka 1000 zatsopano zidzasintha zinthu moti inu n’kupindula—kusintha kumene kudzapangitsa moyo wanu komanso wa banja lanu kukhala wotetezeka komanso wamtendere? Talingalirani za kuopsa kwake kwa oŵerengeka chabe mwa mavuto omwe tikukumana nawo.

Kuwononga Zinthu Zachilengedwe

Mayiko otukuka “akuwononga chilengedwe padziko lonse ndi kuipitsa malo kwambiri komanso kusokoneza zamoyo ndi chikhalidwe chawo.” Ngati zimenezi zipitiriza, “chilengedwe chidzawonongekeratu.”—“Global Environment Outlook—2000,” United Nations Environment Programme.

Matenda

“Pofika m’chaka cha 2020, matenda osapatsirana akuyembekezeka kumapha anthu asanu ndi aŵiri mwa anthu khumi alionse amene azifa m’madera omwe akutukuka, poyerekeza ndi anthu osakwana theka la chiŵerengero chimenecho amene akufa ndi matendawo lerolino.”—“The Global Burden of Disease,” Harvard University Press, 1996.

Akatswiri ena akuti “pofika m’chaka cha 2010, chiŵerengero cha anthu chidzatsika ndi 66 miliyoni m’mayiko 23 kumene kuli mliri woopsa wa [AIDS].”—“Confronting AIDS: Evidence From the Developing World,” lipoti la European Commission and the World Bank.

Umphaŵi

“Anthu pafupifupi [1,300,000,000] amadya ndalama zosakwana dola imodzi patsiku, ndipo pafupifupi [1,000,000,000] satha kupeza chakudya chofunikira.”—“Human Development Report 1999,” United Nations Development Programme.

Nkhondo

“Chiwawa [m’mayiko ambiri] chingafike posalamulirika kuposa ndi kale lonse. Posonkhezeredwa ndi [kugaŵikana] kwa mafuko, mitundu, komanso zipembedzo, . . . chiwawa choterocho chidzakhala . . . mtundu wofala kwambiri wa nkhondo m’zaka [25] zikudzazi . . . , ndipo izidzapha anthu zikwi mazana ambiri chaka chilichonse.”—“New World Coming: American Security in the 21st Century,” U.S. Commission on National Security/21st Century.

Choncho chikondwerero chomwe chakhalapo chifukwa cha zaka 1000 zatsopano chikungophimba zenizeni zakuti kuwononga zinthu zachilengedwe, matenda, umphaŵi, ndi nkhondo zikuwonjezeka kuposa kale lonse. Gwero la mavuto onseŵa ndi umbombo, kusakhulupirirana, ndi dyera—mikhalidwe imene siingathetsedwe ndi kafukufuku wa sayansi, luso lopanga zinthu, kapena ndale.

Zaka 1000 Zimene Zidzadalitsa Mtundu wa Anthu

MLEMBI wina wakale panthaŵi inayake anati: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Munthu alibe nzeru zolamulira nazo dziko lapansi komanso alibe ulamuliro wotero. Mpangi wathu, Yehova Mulungu, ndi yekhayo amene ali ndi ulamuliro umenewo komanso nzeru yothetsera mavuto a mtundu wa anthu.—Aroma 11:33-36; Chivumbulutso 4:11.

Koma adzachita liti zimenezo? Ndipo motani? Umboni wakuti tafika pafupi ndi mapeto a “masiku otsiriza” uli paliponse. Tatsegulani Baibulo lanu tiŵerenge 2 Timoteo 3:1-5. Lemba limeneli likufotokoza bwino lomwe maumunthu amene anthu ali nawo “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino. Mateyu 24:3-14 ndi Luka 21:10, 11 akufotokozanso za “masiku otsiriza.” Malembaŵa makamaka akunena za zochitika zimene zakhalako chiyambireni chaka cha 1914, monga nkhondo padziko lonse, miliri, ndi njala yaikulu.

Posachedwa pompa, “masiku otsiriza” adzatha. Danieli 2:44 amati: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse . . . Udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [apadziko lapansi]. Nudzakhala chikhalire.” Ndi mawu amenewo, iye analosera kuti Mulungu adzakhazikitsa Ufumu, kapena boma, limene lidzalamulira dziko lapansi. Malinga ndi Chivumbulutso 20:4, boma limeneli lidzalamulira zaka 1000! Talingalirani njira zina zimene moyo wa mtundu wa anthu udzakhalire wabwino m’zaka 1000 zaulemerero zimenezo:

Zachuma. “Adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.”—Yesaya 65:21, 22.

Zaumoyo. “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.” “Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.

Zachilengedwe. Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’—Chivumbulutso 11:18.

Ubale wa Anthu. ‘Sadzaipitsa, sadzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’—Yesaya 11:9.

Anthu mamiliyoni ambiri amakhulupirira malonjezo ameneŵa a m’Baibulo ndipo n’chifukwa chake ali ndi chiyembekezo cha tsogolo labwino. Chotero, amatha kupirira zovuta pamoyo wawo komanso zothetsa nzeru. Koma ndi motani mmene Baibulo lingakhalire ndi mphamvu yokutsogolerani pamoyo wanu?

Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo!

SAYANSI limodzi ndi luso lake lopanga zinthu nthaŵi zina imachititsa chidwi kwambiri! Ngakhale zili choncho, nzeru yaumunthu imeneyo sinachititse moyo wa anthu ambiri kukhala wamtendere ndi wosangalatsa. Chidziŵitso chokha chimene chingachite zimenezi chikufotokozedwa mu Baibulo pa Yohane 17:3, pamene pamati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”

Chidziŵitso chimenechi chikupezeka m’Baibulo. Ngakhale kuti anthu ambiri amanena zotsutsa buku lopatulika limenelo, ali oŵerengeka okha amene aliŵerengapo. Nanga inu bwanji? Zoona, kuŵerenga Baibulo kumafuna khama. Komatu m’pake. Baibulo ndi buku lokhalo limene “adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.”—2 Timoteo 3:16.

Nanga mungatani kuti muyambe kulidziŵa Baibulo? Bwanji osapempha Mboni za Yehova kuti zikuthandizeni? Izo zikuphunzitsa anthu mamiliyoni m’nyumba zawo kwaulere. Pofuna kukuthandizani pankhaniyi, zimagwiritsa ntchito mabuku osiyanasiyana ofotokoza za m’Baibulo, monga kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Kali ndi mayankho achidule pamafunso ambiri amene mungakhale nawo okhudzana ndi Baibulo. Mafunso onga aŵa: Kodi Mulungu ndani? Kodi chifuno cha Mulungu cha dziko lapansi n’chiyani? Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Kodi Baibulo lingaongole motani moyo wanu wa banja?

Ngati mukufuna kuti wa Mboni za Yehova adzakuchezereni kunyumba kwanu, chonde talembani kafomu kali munsimu. Adzasangalala kukuuzani zambiri zokhudza Ulamuliro wa Zaka 1000 wa Ufumu wa Mulungu!

□ Ndikufuna kulandira kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

□ Chonde nditumizireni munthu wodzaphunzira nane Baibulo panyumba kwaulere

[Mawu a M’munsi]

a Panopa tikunena za malingaliro omwe anthu ambiri kumayiko a Azungu ali nawo ponena za zaka 1000 zatsopano. Malinga ndi kuŵerengera kolondola, zaka 1000 zatsopano zidzayamba pa January 1, 2001.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena