Limbikitsani Chidwi Chokopedwa ndi Uthenga wa Ufumu Na. 36
1 Kodi mwamaliza kugaŵira mtokoma wanu wa Uthenga wa Ufumu Na. 36? Umenewo uli ndi funso lapanthaŵi yake lofuna kuti onse aliganizire mofatsa: “Zaka 1,000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu ndi Lotani?” Poyandikira zaka za m’ma 2000, anthu anali ndi ziyembekezo zosiyanasiyana ponena za meleniyamu yatsopano. Uthenga wa Ufumu Na. 36 ukufotokoza zina mwa ziyembekezo zimenezo ndipo umatikumbutsanso kuti mikhalidwe ya padziko siikupereka umboni wa chiyembekezo chodalirika. Meleniyamu yokhayo imene idzabweretse mtendere ndi bata zimene anthu ambiri akuzifunafuna ndiyo Ulamuliro wa Yesu Kristu wa Zaka 1,000. Chidaliro chathu chakuti Ufumuwo udzafikadi chatilimbikitsa kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36 kwa aliyense amene tatha kum’gaŵira.
2 Mmene Anthu Alabadirira Uthenga wa Ufumu: Kugaŵira Mauthenga a Ufumu kumene tachita m’mbuyomu kwatilimbikitsa kwambiri m’ntchito yathu. Ponena za Uthenga wa Ufumu Na. 35, ofesi yanthambi ya ku Canada inalemba kuti: “Ofalitsa ndi apainiya anachirikiza mwachisangalalo ndawala yapadera imeneyi m’munda, ndipo anakhala ndi zokumana nazo zambiri zolimbikitsa.” Ndithudi, inunso mwasonyeza chisangalalo chofanana pogaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36.
3 Ndawala ya Uthenga wa Ufumu imene tili nayoyi idzatha pa November 17, 2000. Kodi gawo la mpingo wanu lafoledwa lonse? Ngati ayi, akulu akupemphani kuti mupitirize ndawalayo mpaka kumapeto a November.
4 Kodi kwanuko anthu alabadira motani pamene m’magaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36? Anthu angapo ndiwo angalembe timapepala tija toitanitsira bulosha la Mulungu Amafunanji kapena kupempha phunziro la Baibulo lapanyumba. Komabe, ambiri amene amasonyeza chidwi poyamba pa nkhani ya meleniyamu sachitapo kanthu kwenikweni kufikira mmodzi wa Mboni za Yehova atawachezeranso. Onse amene anasonyeza chidwi tiyenera kuwayenderanso. Kodi nthaŵi yabwino yowayendera ingakhale liti? Tiyenera kubwererako mwamsanga mmene tingathere.
5 Tamverani zokumana nazo zimene zinaoneka pobwerera kumene anagaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 35. Mpainiya wina ku dziko la Ireland anagaŵira Uthenga wa Ufumu kwa mwini malo odyera. Mayiyo anasangalala ndi uthengawo ndipo anapempha mlongoyo kuti akabwerenso. Mlongoyo anabwererako patapita masiku aŵiri, ndipo anayambitsa phunziro la Baibulo. Ku dziko la Denmark, kope la Uthenga wa Ufumu linasiyidwa panyumba imene sanapezepo munthu. Tsiku lomwelo mayi amene amakhala m’nyumbayo anatumiza kapepala [koitanitsira bulosha kapena kupempha phunziro] ku ofesi yanthambi kudzera ku mpingo wapafupi. Mlunguwo usanathe, alongo aŵiri anafika, anapangana zomaphunzira naye, ndipo mayiyo anapita kumsonkhano kwa nthaŵi yoyamba ku Nyumba ya Ufumu!
6 Zimene Muyenera Kunena Mukabwererako: Kupanga maulendo obwereza kumene munagaŵirako Uthenga wa Ufumu n’kosavuta ndipo ndi mbali yosangalatsa ya utumiki wathu. Pamene mubwerera, ndi bwino kunyamula kope lina la Uthenga wa Ufumu Na. 36, kuti mwina mwininyumbayo alibe kope lake. Mungayese njira izi.
7 Mutam’kumbutsa mwininyumbayo kuti inuyo ndinu ndani, munganene kuti:
◼ “Ndinasiya kabuku ka mutu wakuti ‘Zaka 1,000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu N’lotani?’ Kodi sikunali kolimbikitsa kuŵerenga kuti posachedwa Ulamuliro wa Kristu Yesu wa Zaka 1,000 udzayamba, ndipo udzabweretsa Paradaiso padziko lapansi? [Sonyezani zithunzi za Paradaiso mu Uthenga wa Ufumu Na. 36.] Kumbuyoku, akukulangizani kuti mutha kuitanitsa kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?” Muonetseni buloshalo, tsegulani patsamba 5, ŵerengani funso loyamba komanso ndime 1 ndi 2, kenako funsani mwininyumbayo kukambapo. Ŵerengani ndi kukambirana lemba limodzi kapena aŵiri. Ngati kuli kotheka, kambirananinso funso lina ndi ndime yake, kenako panganani zoti mukabwerenso kudzapitiriza makambiranowo.
8 Pakuti chogaŵira chotsatira cha November chidzakhala bulosha la “Mulungu Amafunanji” kapena buku la “Chidziŵitso,” munganene kuti:
◼ “N’tabwera tsiku lija, n’nakusiyirani kabuku konena kuti ‘Zaka 1,000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu N’lotani?’ Kameneko kamapereka mwayi kwa ofuna kumaphunzira Baibulo panyumba kwaulere. Ndabwera kuti ndikusonyezeni buku limene timagwiritsa ntchito pophunzira. [Muonetseni bulosha la Mulungu Amafunanji, ndipo tembenuzirani kuchikuto chakumbuyo; kapena m’sonyezeni buku la Chidziŵitso, ndipo tsegulani pamasamba 188-9.] Zaka chikwi [1,000] zimene Baibulo limatchula zidzabweretsa mikhalidwe ngati imene mukuiona pachithunzipa. Kuti tikalandire nawo moyo m’Paradaiso, tifunikira kumaphunzira kuti tidziŵe zoona zake ponena za Mulungu. Lekani ndikuonetseni mwachidule mmene timaphunzirira Baibulo.”
9 Kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36 kwatisonkhezera kuchita mbali yokulirapo mu utumiki, tikumapereka umboni waukulu kwambiri. Mwachidziŵikire, izi zalimbikitsanso chidwi cha anthu ambiri m’gawo. Mothandizidwa ndi Yehova, kuyesetsa kwathu mogwirizana kudzatheketsa kupeza onga nkhosa owonjezereka.—Mat. 10:11; Mac. 13:48, 49, 52.