Bwererani kwa Amene Anachita Chidwi ndi Uthenga Wa Ufumu
1 Pamilungu Ingapo Yapitayo, Takhala Tikusangalala Ndi Mwaŵi Wogaŵira Uthenga Wa Ufumu Na. 35, Mutu Wake Wakuti, “Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?” Konsekonse Ofalitsa Akuyesetsa Kugaŵira Kope Limeneli La Uthenga Wa Ufumu Kwa Anthu Ambiri Oyenera. (Mat. 10:11) Ngakhale Kuti Mkupitiwu Udzatha Lamlungu, Pa November 16, Ngati Gawo Lilipobe Lofuna Kufoledwa, Akulu Angakupempheni Kugaŵirabe Uthenga Wa Ufumu Na. 35, Malinga Ngati Mukali Nawo.
2 Kope Limeneli La Uthenga Wa Ufumu Lachititsa Chidwi Anthu Ambiri. Amaona Kuti Anthu Ochuluka Alibe Chikondi Chachibadwidwe Ndiye Sakudziŵa Kuti Kutsogoloku Kulinji. (2 Tim. 3:3) Tikufuna Kubwererako Kuti Tikakulitse Chidwi Chimene Tinadzutsa.
3 Uthenga wa Ufumu Ubala Zipatso: Pamkupiti wina wa Uthenga wa Ufumu, mu 1995, mlongo wina wachikulire anatumiza papositi makope ena. Ndiye mkazi wina yemwe analandira limodzi anafika pamsonkhano pa Nyumba ya Ufumu chifukwa anafuna kudziŵa zambiri zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira. Pamsonkhano umenewo anavomereza phunziro la Baibulo nthaŵi yomweyo, ndipo kuyambira pamenepo sanaphonyephonye misonkhano. Pasanapite nthaŵi, analembera kalata a kutchalitchi chake chakale, kuwauza kuti salinso mmodzi wa iwo!
4 Pakali pano, anthu mazana ambiri aŵerenga Uthenga wa Ufumu Na. 35. Koma kodi anachitapo chiyani? Ngakhale kuti zimene anaŵerenga zinawachititsadi chidwi, ambiri sangachitepo kanthu mpaka Mboni za Yehova zitawachezeranso. Kodi mukukonzekera kubwererako? Kudera nkhaŵa mwachikondi anthu anzathu kutisonkhezere kutero. Onse amene anachita chidwi ndi Uthenga wa Ufumu tikawachezerenso.
5 Kodi Mudzati Chiyani Mutabwererako? Munganene mawu angapo onena za Uthenga wa Ufumu kuti ngwapanthaŵi yake, ndiyeno nkufunsa funso lochititsa chidwi. Mvetserani mosamalitsa pamene mwini nyumbayo akuyankha kuti mudziŵe zimene zili m’maganizo mwake. Kenako msonyezeni mfundo yoyenera mu brosha lakuti Mulungu Amafunanji, yomwe inatchulidwa mu Uthenga wa Ufumu. Ngati mwaona kuti zamsangalatsa, yesani kuyamba phunziro la Baibulo nthaŵi yomweyo.
6 Nazi zitsanzo zina za maulaliki amene mungayese pamene mwabwerera kwa amene anachita chidwi ndi “Uthenga wa Ufumu” Na. 35:
◼ “Ndiyesa mukukumbukira trakiti lija ndinakusiyirani posachedwa? Uthenga wake wapangitsa anthu ambiri zedi mwathu muno kukambitsirana zimene limanena, popeza limakhudza nkhani yaikulu yomwe ikugaŵa mtundu wa anthu lero—kusakonda ena.” Msonyezeni chithunzi chili patsamba 2 la Uthenga wa Ufumu pa kamutu kakuti “Chikondi cha Mnansi Chazirala.” Ndiyeno mfunseni kuti, “Kodi mukuganiza kuti Mulungu akufunadi kuti anthu azikhala motere?” Yembekezerani yankho. Pitani paphunziro 5 m’brosha lakuti Mulungu Amafunanji, ndipo yesani kuyamba phunziro la Baibulo.
◼ “Pamene tinakumana nthaŵi yoyamba, ndinakusiyirani nkhani ina yonena zakuti ‘Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?’ Mukuganiza kuti dziko loterolo lingakhalepo?” Yembekezerani yankho. Pitani paphunziro 6 m’brosha lakuti Mulungu Amafunanji, ndipo ŵerengani ndime 6. Kenako ŵerengani lonjezo la Mulungu pa Mika 4:3, 4. Ngati mwini nyumbayo akuoneka kuti zamsangalatsa, mgaŵireni broshalo ndikumpempha kuchita naye phunziro.
◼ “Pamene ndinakuchezerani poyamba, ndinakusiyirani nkhani yakuti ‘Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?’ Ikupereka mwaŵi kwa munthu aliyense amene angafune phunziro la Baibulo laulere lapanyumba. Ndabweranso kudzakusonyezani buku lothandizira kuphunzira lomwe timagwiritsira ntchito. [Msonyezeni buku la Chidziŵitso.] Buku limeneli limafotokoza bwino nthaŵi imene anthu onse adzakondana wina ndi mnzake, ndipo limayankha mafunso ena amene angakhale akukuvutani, monga: Kodi nchifukwa ninji timakalamba ndi kufa? Kodi Mulungu waloleranji kuvutika? Kodi nchiyani chimachitika kwa okondedwa athu akufa? Kodi mungakonde kuti ndikusonyezeni mmene timaphunzirira?” Ngati mwini nyumbayo wakana, mfunseni ngati angakonde kuliŵerenga bukulo payekha. Ngati walola, mgaŵireni bukulo pa chopereka cha nthaŵi zonse. Konzani kudzabwererakonso.
7 Titalifola bwinobwino gawo lonse ndi Uthenga wa Ufumu Na. 35, tingagaŵire buku la Chidziŵitso pamasiku otsala a mweziwo. Zitsanzo zabwino pakugaŵira bukuli zili patsamba lakumbuyo la makope a Utumiki Wathu Waufumu wa December 1995; March, June, ndi November 1996; ndi June 1997.
8 Mkupiti wapadera umenewu wogaŵira Uthenga wa Ufumu uyenera kutisonkhezera tonsefe kuwonjezera khama lathu pantchito yolalikira. Ndi thandizo la Yehova, tingadalire kuti mkupiti umenewu uyendadi bwino, kotero kuti anthu kulikonse adzaona kuti chifuno cha Mulungu nchakuti mtundu wonse wa anthu azikondana wina ndi mnzake. Yehova apitirizetu kudalitsa kuyesetsa kwathu pamene tikubwerera kwa amene anachita chidwi ndi Uthenga wa Ufumu.