Kodi Ndikati Chiyani?
Tikakumana ndi anthu mu utumiki amene amavomereza, timafuna kubwererakonso kuti tikawachitire umboni wina. Komabe, mwina sitingadziŵe chokanena kuti tiyambe kukambitsirana. Mungayese njira iyi: Funsani funso lochititsa chidwi, kenako pitani m’buku la Kukambitsirana kuti musonyeze yankho la m’Malemba. Zingakuthandizeni mutakhala ndi mpambo wa mafunso amene mungasankhepo limodzi limene mukuganiza kuti ndilo lingachititse chidwi kwambiri pakhomo limenelo. Mpambo uli pansiwu, tautenga m’buku la Kukambitsirana, ukusonyeza nambala ya tsamba pamene yankho lililonse likupezeka:
◼ Kodi nchifukwa ninji timakalamba ndi kufa? (151)
◼ Kodi pali zifukwa zabwino zokhulupirira Mulungu? (307)
◼ Kodi Mulungu amasamaladi zimene zimachitika kwa anthufe? (308)
◼ Kodi munthu ayenera kupita kumwamba kuti akhale ndi mtsogolo mwachimwemwe? (204)
◼ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kudziŵa ndi kugwiritsira ntchito dzina lake la Mulungu? (420)
◼ Kodi Ufumu wa Mulungu udzachitanji? (376)
◼ Kodi nchiyani chimene chili cholinga cha moyo wamunthu? (290)
◼ Kodi nchifukwa ninji pali zipembedzo zambiri chonchi? (83)
◼ Kodi munthu angadziŵe motani chimene chili chipembedzo choona? (89)
◼ Kodi Satana ali munthu wamphamvu motani m’dziko lamakono? (355)
◼ Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola kuvutika? (222)
◼ Kodi nchifukwa ninji pali kuipa kochuluka chonchi? (183)
Mungasunge mpambo wa mafunso ameneŵa m’Baibulo kapena m’buku lanu la Kukambitsirana kuti muziwaona msanga. Kukumbukira mawu ena otsimikizika okanena pamaulendo obwereza kudzakulimbikitsani kukhala wokhulupirika pakukulitsa chidwi cha anthu amene munapeza.