Kufunafuna kaamba ka Chowonadi Kufupidwa
MWA kupeza kukhutiritsidwa kochepa monga mlaliki wamba mu tchalitchi cha Chipresbyterian, mwamuna wina anayamba kufunafuna kaamba ka tchalitchi chowona cha Mulungu. Iye anandandalitsa zofunika khumi zomwe iye anadzimva kuti tchalitchi chowona chifunikira kukhala nazo. Iye anali kale ndi kumvetsetsa kolongosoka kwa moto wa helo wosakhala wa m’malemba, kusafa kwa moyo, ndi zina zotero. Iye anachita kufufuzaku kwa zaka 30. Pamene anakumanidwa ndi mmodzi wa Mboni za Yehova, anayamba kufunsa mafunso ake, onga ngati: “Ndani omwe ali kagulu ka nkhosa? Ndani omwe ali a 144,000 ndi nkhosa zina?” Atapeza mayankho okhutiritsa iye anavomereza ku phunziro la Baibulo. Pambuyo pa miyezi itatu iye anati kwa mboniyo: “Chabwino Mbale, tchalitchi chowona cha Mulungu chiri cha Mboni za Yehova.” Iye tsopano ali ndi zaka 71 za kubadwa ndipo wachimwemwe kukhala atapeza tchalitchi chowona pambuyo pa kufunafuna kwa zaka 30!