Yehova Amanga Nyumba
LOŴERUKA, March 21, 1987, linali tsiku limene ziwalo za malikulu a ku South Africa za Watch Tower Society sizidzaiwala nkomwe. Inali nthaŵi ya m’mbiri. Chimango chatsopano pa Roodekrans chinaperekedwa—kutsirizidwa kwa zaka zisanu ndi chimodzi za kugwira ntchito kwa kalavulagaga. Koma ulemerero upita kwa Yehova. Monga mmene Solomo anachilongosolera: “Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.”—Masalmo 127:1.
Tiyeni mwachidule tifufuze kakulidwe ka Mboni za Yehova mu South Africa. Mu 1902 anthu aŵiri oyambirira akumaloko anayamba kuphunzira zofalitsidwa za Sosaite ndi kulengeza kwa ena. Mu 1910 Will Johnston anatsogozedwa ndi Mbale Russell kutsegula ofesi ya nthambi ya munthu mmodzi mu Durban. Chaka chotsatira umodzi wa mipingo ya mu Africa unalinganizidwa mu Ndwedwe pafupipo. Mkati mwa chaka chovuta cha 1914, msonkhano wachigawo woyambirira unachitika mu Durban ndipo unali ndi opezekapo 50. Nthambi inasinthidwira ku Cape Town mu 1923, ndipo chaka chotsatira makina osindikizira ang’ono anagwiritsiridwa ntchito. Nthambi inasinthidwira ku malo a akulu mu 1933, koma panalibe Nyumba ya Beteli.
Chikhalirechobe kusintha kwina kofunika kunachitika mu 1952, kupita ku Elandsfontein—makilomita 1,500 cha kumpoto kwa Cape Town ndipo chifupifupi makilomita 20 cha kum’mawa kwa Johannesburg. Inali yoyambirira ya nyumba mu South Africa imene kwenikweni inalinganizidwa ndi Sosaite, chotero inaphatikizapo malo okulira kaamba ka kusindikiza limodzinso ndi Nyumba ya Beteli, kapena kogona. Panthaŵiyo, ntchito ya Ufumu inkatsegulidwa m’maiko osiyanasiyana osamaliridwa ndi nthambi ya South Africa. Chotero nthambi inafunikira kukulitsidwa mu 1959, kachiŵirinso mu 1971, ndipo kachiŵirinso mu 1978. Kenaka panalibe malo kaamba ka kufutukuka kotsatirapo pa malowo.
Ofalitsa aŵiri oyambirira mu South Africa anawonjezeka ku chifupifupi 28,000. Inali nthaŵi ya kufunafuna malo atsopano, amene anaphatikizapo kufufuza kwa nthaŵi yaitali. Potsirizira pake munda wabwino wa 87 hectares unapezedwa pa Roodekrans yomwe iri pa mtunda wa makilomita 60 kuchokera ku Elandsfontein. Chitsogozo cha Yehova ndi chithandizo chinawonekera kwenikweni m’kupezedwa ndi kugulidwa kwa malo okondedwawa.
Kulaka Mavuto
Komabe, mavuto okulira anafunikira kulakidwa. Mtengo woyambirira unawonekera kukhala waukulu, ndipo zilolezo zapadera zinafunikira kumanga fakitare, maofesi, ndi malo ogona m’malo okhala. Vuto lowonjezereka linali kufunitsitsa kwa kukhala ndi Mboni zakuda kumeneko omwe anali otembenuza. Chinawonekera kukhala chozizwitsa mmene mavutowa anagonjetsedwera, kupereka umboni wakuti Yehova ankamanga nyumbayo. Vuto lina linali kusowa kwakukulu kwa antchito aluso. Koma antchito aufulu anali ofulumira kuphunzira maluso osiyanasiyana. Ichi chinaphatikizapo alongo. Woyang’anira m’modzi anachitira ndemanga kuti: “Atsikana achichepere oyengedwa omwe sakuyenera pa malo omangawa anakhala akatswiri oyala zinthu zoika pansi. Sindinawonepo ndi kale lonse ubwino wotere.”
Ntchito yomanga inayenda pang’onopang’ono poyambirira. Kenaka antchito aufulu ambiri anapita ku Roodekrans—akuda, achiyera, Akaladi, ndi Amwenye. Abale anakhoza ngakhale kubwera kuchokera ku maiko ena, onga ngati New Zealand ndi United States. Ichi chinali chachilendo mu South Africa. “Chiri chabwino kuwona abale ndi alongo akugwira ntchito pamodzi, a mitundu yosiyanasiyana ndi mafuko ochokera ku mayambidwe osiyanasiyana,” anatero wogwira ntchito m’modzi waufulu. Ambiri anasiya ntchito zawo zabwino kapena kutenga matchuthi a atali kukathandiza ndi kumangako pa Roodekrans. Iwo anaphatikizapo akatswiri okonza magalimoto okhala ndi chidziŵitso, akatswiri a zomangamanga, katswiri wokonza makina, odziŵa kulemba mmene kamangidwe kadzawonekera oyeneretsedwa, ndi oyang’anira a kumangako. Makina amtengo wapatali anaperekedwa monga chopereka kapena kugwiritsiridwa ntchito pa ngongole.
Bwanji ponena za zowonongedwa zazikulu zophatikizidwapo? Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linapanga makonzedwe kaamba ka ngongole ya ndalama zambiri, ndipo Mboni za kumaloko za mafuko onse ndi misinkhu yonse zinathandizira mooloŵa manja. Mtsikana wa zaka zisanu ndi chimodzi analemba kuti: “Ndinali kusunga ndalamayi kuti ndigule chidoli, koma ndikuitumiza iyo kwa inu. Ndikungoyembekeza kuti inu mungakhoze kutsiriza Roodekrans ndi ndalamayi. Pamene ndakula, ndidzafunanso kupita ku Roodekrans kukagwira ntchito kumeneko.” Mnyamata wachimwenye wa zaka zisanu zakubadwa anapereka ndalama zake zodyera kuchokera ku miyezi isanu ndi umodzi yapita!
Kothera kwa mlungu mazana angapo a Mboni zowonjezereka zinadza kudzagawanamo mu ntchito yofunika kwambiriyi. Ogwira ntchito aufulu ena anabwera pa maziko a tsiku ndi tsiku, kaŵirikaŵiri akumapanga kudzipereka kwenikweni ndi kuika kuyesayesa kwamphamvu kwa kuchita tero. Odzacheza osakhala Mboni anangogwedeza mitu yawo m’kusakhulupirira pa kuwona unyinji, wa kuchirikiza kotenthedwa maganizo. Anthu ambiri okhala pafupi anakondweretsedwa kwenikweni. Makampani a zamalonda akumaloko analimbirana kaamba ka kuchita malonda pa Roodekrans, ndipo oimira awo kaŵirikaŵiri anachitira ndemanga pa mkhalidwe wa mtendere ndi umodzi.
Nyumba Yaikulu Mkakonzedwe Kokongola
Mapiri atanthwe kumbali ya kum’mwera kwa malo omangawo amaloza ku chigwa chosangalatsa ndi mtsinje. Ngakhale kuti malowo ali pafupi ndi malo ochewutsa kunja kwa mzinda, kukali nyama zina kumeneko, zonga ngati nkhanga ndi akafumbwe. Nkhwazi ndi nkhandwe kaŵirikaŵiri zimadzachezera nazonso. Nyumba yogonako, iri kumbali yopendekeka pang’ono ya mapiri kwa mamita 360, ndipo iri yomangidwa ndi njerwa zofiira. Iri ndi nyumba zitatu zosanjikana, yokhala ndi kawonekedwe kokongola. Pakati pake pali malo antchito okhala ndi chipinda chodyera, chophikira, chochapira, ndi kosamalira okalamba. Chapafupi pali mbali ya ofesi ndi chipinda chosindikizira chachikulu, chomwe chiri mongoyerekezera cha ukulu wa chingalawa cha Nowa. Mkati mwake chiri ndi makina osindikiza mitundu inayi otchedwa TKS offset.
Chakumadzulo kwa nyumba yogonayo kuli malo a munda ndi chipinda choikamo zinthu chachikulu, chomwe chinkagwiritsiridwa ntchito monga chipinda chodyera ndi mophikira mkati mwa kumangako. Minda ya udzu ndi alfalfa imapereka chakudya kaamba ka ng’ombe zambiri za mkaka. Pali mazana angapo a zitsamba za protea pa mapiri kumbuyo kwa malo ogona. Kuwonjezera pa mitengo yomwe iripo yaitali ya eucalyptus, mitengo yambiri yatsopano, maluwa okongola, ndi malo a kapinga okulira abzyalidwa.
Progamu Yopereka
Khamu la chifupifupi 4,000 linasonkhana pabwalo pafupi ndi nyumba yogonako kaamba ka kupereka pa Loŵeruka masana, March 21, 1987. Pulatifomu yosakhalitsa inaloza kumapiri, ikumapereka kawonekedwe konga bwalo lamaseŵera. Tcheyamani, Mbale R. F. Stow, anaŵerenga mauthenga ochirikiza ochokera ku maiko 17. Womwe unadzutsa mitima kwambiri pakati pa awa unali wochokera kwa Maud Johnston, mkazi wa woyang’anira wa nthambi woyambirira mu Durban. Pa zaka zakubadwa 92, iye adakali kutumikirabe mu Beteli ya ku Australia.
P. J. Wentzel, woyang’anira wa Depatimenti ya Utumiki, anali mlankhuli woyambirira, ndipo anapereka chidule cha mbiri ya ntchito ya Ufumu mu South Africa. Iye anayerekeza chiŵerengero cha opezekapo 50 pa msonkhano woyamba mu 1914 ndi chiŵerengero cha opezekapo 99,000 pa misonkhano ya chigawo mu 1986. Wotsatira, J. R. Kikot, woyang’anira fakitare, analongosola kusindikiza kwa mabukhu mu zinenero zambiri ndi ntchito ya otembenuza oposa 50. Iye anatchulanso kuti mu 1979 makina osindikizira otchedwa TKS, mphatso yochokera ku nthambi ya ku Japan, anakhazikitsidwa, koma iwo anasindikiza kokha mu mitundu iŵiri. Posachedwapa, mbali ziŵiri zowonjezereka, mphatso inanso yochokera ku Japan, zinawonjezeredwa ku makinawo. Monga chotulukapo, Nsanja ya Olonda ya April 1, 1987, inasindikizidwa mu mitundu yonse, ku chikondwerero cha onse.
C. F. Muller, m’gwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi, analongosola mmene Yehova anathandizira kupereka malowo, ndalama, akatswiri, ndi antchito ofikapo. Mzimu wa Yehova unatulutsanso kugwirizana kwabwino pakati pa mafuko osiyanasiyana. Ngakhale kuti pa nthaŵi imodzi chinawonekera kukhala chosatheka kumanga fakitare mu malo akulu ogona ndi kwa akuda kuti akhale kumeneko, Yehova anatsegula njira, chotero iye anali m’Mangi Wamkulu!
Mlankhuli wotsatira anali Carey Barber, chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Nkhani yake yabwino inazikidwa pa Yesaya 65:17-19, pamene pamaneneratu mmene anthu a Yehova “adzasangalala . . . ndi kukondwa kosatha.” Mlankhuliyo analongosola kuti “kusangalala” kumatanthauza “kudumpha kaamba ka chisangalalo” ndipo kuti uli mkhalidwe waukulu wa chimwemwe. Ilo ndithudi linali tsiku lachimwemwe kwa opezekapo. Nkhani yopereka inaperekedwa ndi Milton Henschel, nayenso wa Bungwe Lolamulira. Iye anapereka pemphero lapadera kwa Yehova, akumapereka chiyamikiro kaamba ka kutipatsa nyumbayo, yomwe tsopano inaperekedwa kwa Iye.
Tsiku lotsatira Mboni 28,250 ndi anthu okondwerera anasonkhana mu Rand Stadium, Johannesburg, kumene anamvetsera chidule cha programu ya pa Roodekrans. M’nkhani yotembenuzidwira mu Chizulu, Henschel anasonyeza mmene Mboni za Yehova, zotsogozedwa ndi Yehova ndi Yesu, ziriri zachipambano kulikonse ndi kufalitsa “fungo labwino la Kristu” ndi chidziŵitso china cha Baibulo. (2 Akorinto 2:14-17) Iye anatsiriza ndi zokumana nazo zolimbikitsa zambiri zomwe zinasangalatsa opezekapo ochuluka.
Mkati mwa masiku angapo otsatira, kusonkhana kofananako kunachitika mu Durban ndi Cape Town. Izi zinali nthaŵi zimene sizidzakhoza kuiwalidwa ndi Mboni za Yehova mu South Africa. Banja la Beteli pa Roodekrans ndithudi lidzakumbukira kwa nthaŵi yaitali tsiku la kupereka kaamba ka mudzi wawo watsopano. Ndi Mboni zoposa 40,000 m’malo mwa 28,000 pamene ntchito inayambika pa Roodekrans, ‘nyumba imene Yehova waimanga’ ikukwaniritsa chifuno chofulumira ndi choyenera.