Kodi Mumakumbukira?
Kodi mwapeza makope a posachedwapa a Nsanja ya Olonda a phindu logwira ntchito kwa inu? Chotero bwanji osayesa kukumbukira kwanu ndi zotsatirazi:
◻ Nchifukwa ninji Timoteo anali chitsanzo chabwino chotere kaamba ka achichepere kuti atsatire?
Timoteo anapereka womwe ukutchedwa umoyo wabwino panyumba kuti akhale mnzake wodalirika, ndi wokhulupirika wa Paulo. Iye anamamatira kwa Paulo kupyola m’mavuto, kumchirikiza iye mu ntchito yolalikira ndi kukhala wofunitsitsa kutumikira kulikonse kumene anatumizidwako. (Afilipi 2:19, 20)—8/15, tsamba 14.
◻ Kodi ndi ziti zomwe ziri ziyeneretso kaamba ka kubatizidwa?
Wophunzira wopita ku ubatizo afunikira kuzindikira chimene chikuphatikizidwamo. Iye afunikira mowonadi kufuna kutumikira Yehova chifukwa chakuti amamkonda Iye. Iye amasonyeza ichi mwakumamatira ku zofunika za makhalidwe abwino a Mulungu ndi kugawana chikhulupiriro chake ndi ena. Iye afunikiranso kupanga kudzipereka kwaumwini kwa Yehova m’pemphero.—8/15, tsamba 16.
◻ Nchifukwa ninji chiri cholakwa kufufuzafufuza kukhulupirira mizimu?
Kufufuzafufuza kukhulupirira mizimu kumafikira ku kukonda zimene Yehova amada. (Miyambo 6:16-19) M’chenicheni, chiri monga kukana Yehova ndi kukhala kumbali ya mdani wamkulu wa Mulungu ndi achirikizi ake.—9/1, tsamba 5.
◻ Kodi nchiyani chimene chiri “bukhu la chikumbutso” lonenedwa pa Malaki 3:16?
Kuchokera ku nthaŵi ya Abele kunka mtsogolo, Yehova wakhala akudziŵa, monga ngati ‘kulemba mu bukhu,’ awo a mtundu wa anthu operekeredwa dipo omwe ali oyenera kukumbukiridwa kaamba ka moyo wosatha. “Bukhu la chikumbutso limeneli” liri lofanana ndi “bukhu la moyo” ndi “mpukutu wa moyo.” (Chivumbulutso 3:5; 17:8; Mateyu 23:35)—9/1, tsamba 29.
◻ Kodi nchiyani chimene chimapanga bwenzi lowona kukhala la mtengo wapatali?
Inu nthaŵi zonse mungatembenukire kwa bwenzi lowona kaamba ka thandizo, chiweruzo, chitonthozo, ndi ubwenzi wathithithi.—9/15, tsamba 3, 4.
◻ Kodi nchiyani chimene chiri “mpweya” wodzetsa imfa wadzikoli?
Iwo uli mzimu wachisawawa, kapena mkhalidwe wolamulira wadyera ndi kusamvera, wosonyezedwa ndi anthu otalikira kwa Mulungu. (Aefeso 2:2; 1 Akorinto 2:12)—9/15, tsamba 11.
◻ Kuti chipembedzo chikhale cha phindu logwira ntchito, kodi nchiyani chimene icho chiyenera kuchita?
Icho chiyenera kukhala ndi chipatso chabwino. Chiyenera kutulutsa anthu abwino. Chiyenera kukhala chokhoza kulongosola chifukwa chimene zinthu ziri mmene ziriri padziko lapansi lerolino. Ndipo chiyenera kuika m’malingaliro ndim’mitima ya anthu chiyembekezo chotsimikizirika kaamba ka mtsogolo. (Mateyu 7:17-20)—10/1, tsamba 7.
◻ Kodi nchiyani chimene kukonzanso kunalephera kukwaniritsa?
Okonzanso ena oyambirira analota za kubwerera ku malamulo a Baibulo, ku Chikristu chenicheni. Loto limeneli silinazindikiridwe nkomwe. Ndi kupita kwa nthaŵi, ziphunzitso zenizeni za matchalitchi a Chiprotestanti, kaya zinali za utundu kapena zosiyanako, zinagwera kwakukulukulu mumzera umodzi ndi zija za tchalitchi cha Roma Katolika.—10/1, tsamba 25.
◻ Kodi nchiyani chomwe chinatsogolera ku chiweruzo choipa cha Mose ndi Aroni kutsatira chochitika cha pa Kadesi-barnea?
Masalmo 106:32, 33 amapereka chidziŵitso m’chochitikachi, kusonyeza kuti Mose anachita mwa mzimu waukali ‘kulankhula mwasontho ndi milomo yake.’ Ndi mawu aukali, iye anaitanira chisamaliro pa iyemwini ndi Aroni kuposa kwa Yehova, amene kwenikweni akanapereka madzi mozizwitsa. Mwanjirayi Mose analephera ‘kulemekeza Mulungu pamaso pa anthuwo.’ (Numeri 27:12-14)—10/15, tsamba 31.
◻ Kodi ndi chifuno chamtengo wapatali chotani chimene chinatumikiridwa ndi Lamulo la Mulungu loperekedwa kwa Israyeli?
Lamulo linaperekedwa kwa Israyeli m’malo mwakufuna kusunga mtunduwo kukhala waukhondo mwakuthupi, mwauzimu, mwamalingaliro, ndi mwamakhalidwe.—11/1, tsamba 12.
◻ Kodi ndi zothandiza zotani zomwe ziripo za kusungirira kuyera kwa umbeta?
Pempherani mokhazikika kaamba ka mzimu wa Mulungu ndi thandizo lake kusonyeza chipatso chake. Mwerekerani ndi kugwiritsira ntchito uphungu wopezeka m’Mawu a Mulungu. Pewani zithunzi zosonyeza umaliseke ndi zosangalatsa za chisembwere. Chenjerani ndi mayanjano anu. Pewani malankhulidwe oipa onse ndi kuseka koipa.—11/15, tsamba 20.
◻ Kodi ndi kusiyana kwakukulu kotani kumene kulipo pakati pa ochiritsa osimbidwa mu Baibulo ndi aja osimbidwa ndi ochiritsa mwachikhulupiriro lerolino?
Yesu ndi ophunzira ake sanalipiritse nkomwe kaamba ka kuchiritsa kwawo. Kuchiritsa kochitidwa m’nthaŵi za Baibulo kunali kaya kochiritsa pa nthaŵi yomweyo kapena kofikiritsidwa mkati mwa nyengo yochepa ya nthaŵi.—12/1, tsamba 4, 5.
◻ Kodi ndi ati amene ali ena a mapindu a kuimba mofuula m’kulambira kowona?
Kudzilowetsa kwathu kwaumwini m’kulambira kwapoyera kumakhala kwa mphamvu. Kuimba kumapereka umboni wabwino kwa achatsopano. Chofunika koposa, chilemekezo chokulira chimabweretsedwa kwa Yehova.—12/1, tsamba 27.