Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 5/1 tsamba 4-7
  • Kodi Zili Nkanthu ndi Mmene Mumapembedzera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zili Nkanthu ndi Mmene Mumapembedzera?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chipembedzo Chilichonse Chimakondweretsa Mulungu?
  • Miyezo ya Mlengi ya Kulambira
  • Chithandizo Chilipo
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kulondola Chipembedzo Choyera Kaamba ka Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mmene Mungacidziwire Cipembedzo Coona
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 5/1 tsamba 4-7

Kodi Zili Nkanthu ndi Mmene Mumapembedzera?

DZUŴA lili pamutu, kunja kukutentha kwambiri m’mudzi wina waung’ono wa mu Afirika. Kuchigwa chapafupipo kukumveka ng’oma zoliritsa, kuimba, ndi kuwomba m’manja kwachisangalalo. Komatu chimenechi sichochitika cha macheza. Ndiko kulambira kwamwambo kwa mu Afirika. Komabe, mamvekedwewo akupikisana ndi mawu ofuula kwambiri ochokera patchalitchi china chochiritsa. Pamenepo olambira otengeka maganizo amachita “machiritso” ozizwitsa ndi kulankhula m’malirime. Kumbali ina kwa tauniyo kulinso mtundu wina wa kulambira. Liwu lofuula lomvekera pamwambamwamba la mmwezini loitana alambiri anzake Achisilamu kumapemphero.

Inde, kudzipereka kwachipembedzo kosiyanasiyana kwambiri kungaonedwe m’mizinda ndi matauni ambiri a mu Afirika. M’mibadwo yawo yambiri anthu a mu Afirika anali okhutira kutsatira miyambo yachipembedzo yawoyawo. Komano panadza amishonale a Dziko Lachikristu, motsatira magulu ankhondo a mitundu yosiyanasiyana ya Azungu, ndipo anayesayesa mwankhanza “kupangitsa aliyense kukhala Mkristu”​—ngakhale kusintha maina awo.

Chotulukapo chake? Mtundu wa chipembedzo umene unasanganiza zikhulupiriro zamwambo ndi machitachita a mu Afirika ndi ziphunzitso zachipembedzo zochokera kwina. Kufikira lerolino “Akristu” ambiri olambira amagwiritsira ntchito njirisi ndi mazango amwambo. Komabe, amishonale a Dziko Lachikristu anaimira molakwa kwambiri Chikristu chowona, ndipo anasiya chilema cha kuipidwa nacho. Mokulira, iwo ali ndi thayo la kuchititsa mkhalidwe wamaganizo wa anthu kukhala wotsekeka kulinga ku Baibulo limene lili pakati pa anthu ena a mu Afirika lerolino.

Mosasamala kanthu za zimenezo, mipangidwe yambiri ya “Chikristu” idakagwiritsidwabe ntchito mofala. M’zaka zaposachedwapa timagulu tachipembedzo tochiritsa takhala totchuka kwambiri; matchalitchi ochiritsa afalikira. Wolemba nkhani za m’nyuzipepala wina anafotokoza za chikoka cha matchalitchi ameneŵa mwa kunena kuti ‘lingaliro la munthu wa mu Afirika la chipembedzo kwakukulukulu ndilo la kupezerapo thandizo. M’maganizo a munthu wa mu Afirika, chipembedzo chiyenera kukhala chokhoza kupereka mwachindunji zinthu zakuthupi zokhutiritsa kwa munthu. Chifukwa chake, kwa munthu wa mu Afirika amene amakhulupirira kuti mizimu ili yofunika pafupifupi m’kanthu kalikonse, njira ya kachitidwe ka zinthu ya matchalitchi auzimu [kapena ochiritsa mwa chikhulupiriro] imatsatira zofuna za moyo wake.’ Komabe, mwachisoni, matchalitchi ambiri ochiritsa mwachionekere angokhazikitsidwa monga mabizinesi opezerapo ndalama.

Lerolino, timagulu tachipembedzo toposa 6,000 timapezeka mu Afirika. Mwinamwake inu mwalingalira kuti zipembedzo zonsezi ndi timagulu tazipembedzo zili ndi njira ya ku chipulumutso. Koma funso lofunika nlakuti, Kodi Mulungu amalingalira motani?

Kodi Chipembedzo Chilichonse Chimakondweretsa Mulungu?

Ndithudi, Mlengi wa chilengedwe chonse sangatisiye popanda chitsogozo ponena za nkhaniyi. (Amosi 3:7; Machitidwe 17:26, 27) Ndipo umboni wakuti chitsogozo cha Mulungu chingapezeke m’Baibulo n’ngwochuluka. Ayi, Baibulo siliri buku la azungu, monga momwe ena amalitchera. Kwenikweni, palibe munthu​—wakuda kapena wachiyera​—amene anganenedwe kukhala lake. “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu,” limatero lemba la 2 Timoteo 3:16. Kuwona kwa Baibulo, ziphunzitso zake zothandiza kwambiri, kukhalapo kwake kwanthaŵi yaitali, kupulumuka kwake kuukiridwa kwankhanza, maulosi ake olondola ndi kufalitsidwa kwake kosafanana ndi kwina kulikonse padziko lonse​—ameneŵa ali maumboni omvekera bwino a kulembedwa kwake ndi Mulungu.

Kodi bukulo limatiphunzitsanji? Choyamba, limatiuza kuti pali “Mulungu wowona” mmodzi yekha. (Yohane 17:3) Popeza kuti zimenezo zili choncho, kodi ndimotani mmene m’zipembedzo zonse mungakhalire chowonadi? Kodi magulu achipembedzo samatsutsana pamene afika pankhani ya kudziŵika kwa Mulungu ndi chimene ali? Wolemba Baibulo Yakobo analankhula za “chipembedzo choyera ndi chowona.” (Yakobo 1:27, Today’s English Version) Ngati kuli kofunika kudziŵa chipembedzo chowona, payeneranso kukhala chipembedzo chonama kapena chonyenga. Zimenezi zikatsutsana ndi lingaliro lakuti zipembedzo zonse zangokhala njira zosiyanasiyana zofikira kwa Mulungu.

Miyezo ya Mlengi ya Kulambira

Kodi ndi iti imene ili njira yoyenera yolambirira Mulungu? Baibulo limatiphunzitsa kuti kulambira kowona kwazikidwa pa chidziŵitso cholongosoka. Mneneri wamkulu Yesu Kristu panthaŵi ina anauza mkazi wina Wachisamariya kuti: “Inu mulambira chimene simuchidziŵa.” (Yohane 4:22) Kodi mwinamwake zimenezi zingakhale choncho kwa inunso? Kodi mwaphunzitsidwa kuti Mulungu Wamphamvuyonse ali ndi dzina lake, Yehova? (Salmo 83:18) Kodi mumadziŵa zimene zili zifuno zake ponena za munthu ndi dziko lapansi? (Mateyu 6:9, 10; Aefeso 1:9, 10; 3:11) Kodi chipembedzo chanu chimakupatsani chiyembekezo chotsimikizirika cha mtsogolo mwabwino kwambiri? Ndipo ngati mudzilingalira inu mwini kukhala Mkristu, kodi mungafotokoze zikhulupiriro zanu kuchokera m’Malemba, kapena kodi munangozilandira popanda kuzipenda?

Ngati mupeza kuti mulibe chidziŵitso cholongosoka, mukhoza kuchipeza kupyolera mwa phunziro la Mawu a Mulungu, Baibulo. Yehova Mulungu amayembekezera kuti olambira ake owona akhale ozoloŵerana ndi zimene Buku Lopatulika limenelo limaphunzitsa. Ndiponso, iye amawayembekezera kuzigwiritsira ntchito m’miyoyo yawo. Mkhalidwe wathu wamaganizo uyenera kukhala ngati uja wa wamasalmo amene anati: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Kodi ndikufikira kumlingo uti kumene chipembedzo chanu chakuthandizani kudziŵa ndi kumvetsetsa Baibulo?

Mbali ina yofunika ya kulambira kowona ndiyo chikhulupiriro mwa Yesu Kristu, osati kokha monga mneneri wamkulu komanso monga Mwana wa Mulungu wobadwa yekha. Malemba amanena momvekera bwino kuti Yesu ndiye “Mkulu wa moyo.” (Machitidwe 3:15; 4:12) Ambiri amanena kuti amakhulupirira mwa Yesu, koma kodi chikhulupiriro chawo chili chenicheni motani? Chikhulupiriro chenicheni mwa Kristu chimafuna kumvera malangizo ake. Mulungu mwiniyo analimbikitsa zimenezi pamene analengeza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani iye.” (Marko 9:7) Motero olambira owona amayesayesa kuyenda m’mapazi a Yesu mosamalitsa monga momwe angathere. (1 Petro 2:21) Njira ina yochitira motero ndiyo mwa kuchita ntchito ya kulalikira poyera imene iye anayambitsa. (Mateyu 4:17, 10:5-7) Kodi chipembedzo chanu chimakulimbikitsani kukhala ndi phande la inu mwini m’ntchito imeneyi?

Chikondi nachonso chili chofunika cha kulambira kowona. Yehova Mulungu amafotokozedwa kukhala chitsanzo changwiro chenichenicho cha chikondi, ndipo Yesu anauza otsatira ake kuti akadziŵidwa ndi chikondi chimene akasonyeza pakati pawo. (Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 4:8) Polingalira za mamiliyoni ambiri a anthu lerolino amene amanena kuti ali Akristu, kodi dzikoli siliyenera kudzazidwa kotheratu ndi chikondi? Komabe, m’chenicheni, dziko lathuli lakhaladi malo opandiratu chikondi. Nkhondo zapha miyoyo mamiliyoni ambiri m’zaka za zana lino lokha. Upandu ndi chiwawa zikupitirizabe kufalikira. Chotero dzifunseni kuti, ‘Ngati aliyense akanakhala wa chipembedzo changa, kodi dzikoli likanakhala malo a anthu achikondi?’

Potsirizira pake, Baibulo limasonyeza kuti olambira owona ayenera kulekana ndi dziko limene silidziŵa Mulungu. Pamene Mulungu anapatula mtundu wakale wa Israyeli monga wosunga kulambira koyera, anachenjeza anthu ake kupeŵa mayanjano apafupi ndi mitundu yoluluzika yowazinga. (Deuteronomo 7:1-6) Pa Yohane 17:16, Kristu Yesu mofananamo anati ponena za ophunzira ake: “Siali a dziko lapansi monga ine sindili wa dziko lapansi.” Olambira owona a Mulungu samatenga mbali m’ndale za dziko, m’makhalidwe oipa, m’malonda aumbombo, kapena m’nthanthi zina zilizonse zonyoza Mulungu. (Yohane 18:36; 1 Yohane 2:15-17) Amamvera lamulo lolembedwa pa Aroma 12:2 lakuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano.” Kodi zimenezo nzimene chipembedzo chanu chimakulimbikitsani kuchita?

Chithandizo Chilipo

Inde, njira imene mumalambirira ilidi nkanthu kwa Mulungu. Malinga ndi mmene amafunira, pali chipembedzo chimodzi chokha chowona. (Aefeso 4:4-6) Kukambitsirana kwathu kwakufupiku kwakhudza zina za mfundo zazikulu za chiphunzitso cha Baibulo. Bwanji osayesayesa kuphunzira zambiri?

Mosasamala kanthu za kuleredwera kwanu m’chipembedzo, Mboni za Yehova zingathe kukuthandizani ponena za nkhaniyi. Izo nzodziŵika padziko lonse chifukwa cha ntchito yawo yaikulu ya maphunziro a Baibulo. Zimaona kuti ziri ndi thayo la kuthandiza anthu a mafuko onse ndi zipembedzo kupeza tanthauzo lakuya la Baibulo. (Miyambo 2:1-6) Zimafalitsa mabuku ofufuzidwa bwino kwambiri ofotokoza Baibulo.a Kwenikweni, zidzafika kwanu kwaulere kudzakuphunzitsani Baibulo mwachindunji. Mamiliyoni a anthu kuzungulira dziko lonse pakali pano akupindula ndi programu imeneyi ya maphunziro a Baibulo. Bwanji osachita motero inu mwini? Ndithudi, nkofunika kuti inu mutero chifukwa chakuti zilidi nkanthu ndi mmene mumalambirira.

[Mawu a M’munsi]

a Chimodzi cha zofalitsidwa zimenezo ndicho buku lakuti Mankind’s Search for God, lofalitsidwa mu 1990 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. Anthu ambiri ayamikira mafotokozedwe ake anzeru ndi aukatswiri a zipembedzo zazikulu za m’dziko.

[Chithunzi patsamba 5]

Amishonale a Dziko Lachikristu anaimira molakwa kwambiri Chikristu chowona

[Chithunzi patsamba 5]

Matchalitchi ambiri ochiritsa ndiwo mabizinesi opezera ndalama

[Chithunzi patsamba 6]

Chikhulupiriro mwa Yesu chili mbali yofunika ya kulambira kowona

[Chithunzi patsamba 7]

Mboni za Yehova zimathandiza mamiliyoni kupeza chidziŵitso cholongosoka mwanjira ya maphunziro a Baibulo apanyumba aulere

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena