Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 1/15 tsamba 19-22
  • Kukonzeratu Tsogolo la Okondedwa Athu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukonzeratu Tsogolo la Okondedwa Athu
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nchifukwa Ninji Tiyenera Kulingalira za Imfa?
  • Kulanda Katundu
  • “Iwo Aŵiri Adzakhala Thupi Limodzi”
  • Miyambo ya Maliro
  • Kuchitapo Kanthu Mwalamulo
  • Kukambirana ndi Achibale
  • Tetezerani Banja Lanu
  • Kaonedwe Kachikristu ka Miyambo ya Maliro
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kupangitsa Moyo Wabanja Kukhala Wabwino
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Mulungu Ali Pamalo Oyamba m’Banja Lanu?
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 1/15 tsamba 19-22

Kukonzeratu Tsogolo la Okondedwa Athu

NKHANI yomvetsa chisoni ya Annie inatuluka m’nyuzipepala yaposachedwapa ya ku Afirika. Mwamuna wa Annie anali wamalonda. Iye anamwalira mu 1995, ndipo anasiya magalimoto 15; mabuku angapo akubanki; ndalama zokwana $4,000 (U.S.) panyumba; sitolo; nyumba yogulitsiramo moŵa; ndi nyumba ya zipinda zitatu zogona. Chimene iye sanasiye chinali chikalata chonena za kagaŵidwe ka katunduyo.

Zinamveka kuti mlamu wake wa Annie analanda katundu ndi ndalamazo ndipo anamkakamiza kuti iye ndi ana ake asanu ndi mmodzi asamuke panyumbapo. Atalandidwa chilichonse, iye ndi ana akewo tsopano akukhala ndi mlongo wake. Anayi mwa ana akewo anasiya sukulu, popeza kuti analibe ndalama zolipirira sukulu kapena kugulira zovala zakusukulu.

Annie anakasuma ku bwalo lalikulu, limene linalamula kuti iye anayenera kupatsidwa wina wa katunduyo, kuwonjezerapo galimoto. Koma palibe nchimodzi chomwe chimene chinabwezedwa. Iye afunikira kupitanso kubwalolo kuti akatenge chikalata cholamula mlamu wakeyo kuti achite monga momwe bwalolo linanenera.

Nchifukwa Ninji Tiyenera Kulingalira za Imfa?

Nkhani ya Annie ikupereka chitsanzo cha zimene zingachitike pamene mutu wa banja alephera kukonzekera za imfa yake. Pa imfa, anthu onse ‘amasiyira ena chuma chawo.’ (Salmo 49:10) Ndiponso, akufa sangathe kunenapo kanthu pa zimene zikuchitikira chuma chawo. (Mlaliki 9:5, 10) Kuti katundu adzagaŵidwe mogwirizana ndi zofuna zake, munthu ayenera kulinganiziratu zonse asanamwalire.

Ngakhale kuti tonsefe timadziŵa kuti tingafe mwadzidzidzi, anthu ambiri amalephera kulinganiziratu zinthu zimene okondedwa awo otsalawo adzatenga. Ngakhale kuti m’nkhani ino tifotokoza kwambiri za miyambo ya m’mitundu ina ya mu Afirika, mavuto ofananawo amapezekanso m’madera ena a dziko lapansi.

Kulingalira za mmene katundu wako adzagaŵidwira pambuyo pa imfa yako ndi nkhani yaumwini. (Agalatiya 6:5) Komabe, wina angafunse kuti, ‘Kodi munthu angakonde bwanji mkazi ndi ana ake ndi kuwasamalira pamene iye akali moyo koma osalinganiziratu zinthu zimene zidzawathandiza pamene iye amwalira?’ Chifukwa chachikulu nchakuti ambiri a ife sitilingalira zakuti tingafe, choncho sitikonzekera kwenikweni za imfa. Ndithudi, sitingathe kudziŵa za tsiku limene tidzafa, monga momwe Baibulo limanenera kuti: “Simudziŵa chimene chidzagwa maŵa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthaŵi, ndi pamenepo ukanganuka.”​—Yakobo 4:14.

Kukonzekera za imfa ndi chinthu chofunika kwambiri. Kumasonyezanso chikondi kwa otsalawo. Ngati sitilinganiziratu zinthu zathu, ena ndiwo amene adzachita zimenezo. Mwinamwake anthu amene sitinali kuwadziŵa nkomwe ndiwo amene adzalinganiza za katundu ndi mwambo wa maliro athu. Pazinthu zoterezi m’maiko ena, Boma ndilo limalinganiza za amene adzatenga ndalama ndi katundu wathu. M’madera ena, achibale ndiwo amalinganiza za kagaŵidwe ka katundu, ndipo zimenezi nthaŵi zambiri zimachititsa mkangano umene umadzetsa njiru m’banjamo. Ndiponso, zimene iwo alinganiza zingakhale zosemphana kwambiri ndi zimene tikanakonda kuti zichitike.

Kulanda Katundu

Mkazi wamasiye ndiye amene amavutika kwambiri pamene mwamuna wake amwalira. Kuwonjezera pa chisoni cha imfa ya mwamuna wake, iye kaŵirikaŵiri amalandidwa katundu. Zimenezi zafotokozedwa poyambirira m’nkhani ya Annie. Chimodzi mwa zifukwa zimene zimapangitsa kuti katundu alandidwe ndi mmene akazi amaonedwera. M’miyambo ina mkazi wa munthu salingaliridwa kukhala mmodzi wa m’banja la mwamuna wakeyo. Kwenikweni iye amaonedwa ngati mlendo amene angabwerere nthaŵi iliyonse kubanja la makolo ake kapena kukwatiwanso m’banja lina. Koma abale ake a mwamunayo, alongo ake, ndi makolo ake sadzamsiya konse, iwo amatero. Ngati iye amwalira, a m’banja lake amakhulupirira kuti zinthu zake zidzakhala zawo, osati za mkazi ndi ana ake.

Amuna amene sadalira akazi awo amachirikiza malingaliro ameneŵa. Mike anali kufotokozera abale ake okha za malonda amene ankachita. Iwo anadziŵa za chuma chake, koma mkazi wake sankadziŵa kalikonse. Pamene iye anamwalira, abale akewo anafikira mkaziyu namfunsa za ndalama zimene mwamuna wakeyo anali kuyembekezera kulandira. Iye sanadziŵe nkomwe za zimenezo. Kenaka, iwo analanda makina ojambulira zinthu zapapepala ndi makina olembera amene mwamuna wake anamgulira. Pomalizira pake, abale akewo anatenga nyumba yake ndi chilichonse chimene chinali m’nyumbamo. Mkazi wamasiye ameneyu ndi mwana wake wamng’ono wamkazi anakakamizidwa kusamuka panyumbapo, anangotenga zovala zawo zokha.

“Iwo Aŵiri Adzakhala Thupi Limodzi”

Amuna achikristu amakonda akazi awo ndipo amaona kuti ayenera kuwadalira. Amuna otere amatsatira uphungu wa m’Malemba wakuti: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha.” Amuna ameneŵa amavomerezanso mawu ouziridwa ndi Mulungu akuti: “Munthu azisiya atate ndi amayi, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo aŵiri adzakhala thupi limodzi.”​—Aefeso 5:28, 31.

Amuna oopa Mulungu amavomerezananso ndi mtumwi Paulo wachikristuyo, amene analemba kuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Mogwirizana ndi pulinsipulo limeneli, ngati mwamuna wachikristu akukonzekera zaulendo wakutali, iye amayenera kulinganiziratu zinthu zimene zidzathandiza banja lakelo pamene iye adzakhala atachokapo. Mofananamo, kodi sikungakhale kwanzeru kuti iye alinganiziretu zinthu zimene zidzathandiza mkazi ndi ana ake pamene iye amwalira? Kukonzekera za imfa ya mwadzidzidzi nkofunika komanso kumasonyeza chikondi.

Miyambo ya Maliro

Amuna achikristu amayeneranso kulingalira mbali ina ya nkhani imeneyi. Kuwonjezera pa chisoni cha imfa ya mwamuna wake, kulandidwa katundu wake, ndiponso mwinamwake ngakhale kulandidwa ana ake, m’mitundu ina mkazi wamasiye amakakamizidwa kutsatira miyambo yakumaloko ya kaliridwe ka maliro. Nyuzipepala ya The Guardian ya ku Nigeria inadandaula kuti m’madera ena, pali mwambo wakuti mkazi amayenera kugona m’nyumba yamdima momwe muli mtembo wa mwamuna wakeyo. M’madera ena, akazi amasiye saloledwa kuchoka panyumbapo nthaŵi yonse yolira malirowo imene imatenga pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi. Panthaŵi imeneyo, iwo saloledwa kusamba m’thupi, ndipo ngakhalenso kusamba m’manja mwawo asanadye kapena atatha kudya chakudya nkoletsedwa.

Miyambo imeneyi imadzetsa mavuto, makamaka kwa akazi amasiye achikristu. Cholinga chawo cha kusangalatsa Mulungu chimawasonkhezera kupeŵa miyambo imene imasemphana ndi ziphunzitso za m’Baibulo. (2 Akorinto 6:14, 17) Komabe, ngati iye alephera kuchita miyambo imeneyi, mkazi wamasiyeyo angazunzidwe. Mwinanso iye angafunikire kuthaŵa kuti apulumutse moyo wake.

Kuchitapo Kanthu Mwalamulo

Baibulo limanena mwanzeru kuti: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu.” (Miyambo 21:5) Kodi mutu wa banja angakonzekere motani? M’madera ambiri munthu amatha kulemba chikalata chofotokoza za kagaŵidwe ka katundu wake ngati amwalira. Chikalatacho chingaphatikizeponso tsatanetsatane wa mmene mwambo wa maliro ake udzayendetsedwera. Chingafotokozenso bwino lomwe zimene mkazi wake ayenera kuchita (kapena zimene sayenera kuchita) mogwirizana ndi miyambo ya malirowo ndi kaliridwe kake.

Mwamuna wa Leah anamwalira mu 1992. Leah anati: “Ndili ndi ana asanu​—ana aakazi anayi ndi mwana wamwamuna mmodzi. Mwamuna wanga anadwala nthaŵi yaitali ndithu asanamwalire. Koma iye asanayambe nkudwala komwe, analemba chikalata chonena kuti anafuna kuti katundu wake yense ndidzatenge ndine ndi ana athu. Izi zinaphatikizapo ndalama za inshuwalansi, munda, ziŵeto, ndi nyumba. Iye anasaina chikalatacho nandipatsa. . . . Mwamuna wangayo atamwalira, abale ake anafuna kuti atengeko katundu wakeyo. Ndinawafotokozera kuti mwamuna wanga anagula mundawo ndi ndalama za m’thumba mwake choncho iwo analibe mphamvu yotenga chilichonse. Pamene iwo anaona chikalatacho, anavomereza.”

Kukambirana ndi Achibale

Mavuto angabuke ngati munthu sakambirana ndi achibale ake ponena za zikhulupiriro ndi zofuna zake. Talingalirani za nkhani ya mwamuna wina amene achibale ake analimbikitsa kuti maliro ake akaikidwe kumudzi mogwirizana ndi mwambo wakwawoko. Pamene iwo anaona kuti anali pangozi yoti angaphedwe, mkazi wake wamasiyeyo ndi ana ake anasiya mtembowo ndi achibale a mwamuna wake nathaŵa. Iye anadandaula kuti: “Mwamuna wanga akanauza ngakhale mmodzi wa atsibweni kapena asuwani ake za mmene akanafunira kuikidwira, achibale akewo sakanalimbikira kuti malirowo aikidwe motsatira miyambo yawo.”

M’mitundu ina kungofotokoza mawu apakamwa kumakhala kothandiza mofanana ndi kulemba chikalata. Zimenezi nzimene zimachitika m’madera ena a ku Swaziland, kumene ambiri amalimbikitsa zikhulupiriro za miyambo yakumaloko ya maliro ndi kaliridwe kake. Pozindikira zimenezi, mwamuna wachikristu wotchedwa Isaac anasonkhanitsa achibale ake, amene sanali Mboni za Yehova, ndipo anakambirana nawo za zomwe adzachite iye akadzafa. Iye anawauza amene anali kudzatenga katundu wakutiwakuti, ndipo anafotokozanso mwatsatanetsatane za kayendetsedwe ka mwambo wa malirowo. Iye atamwalira, zinthu zinayenda mogwirizana ndi zofuna zake. Isaac anaikidwa mwachikristu, ndipo mkazi wake anasamaliridwa bwino.

Tetezerani Banja Lanu

Kulingalira za zimene munthu adzachita pofuna kutetezera banja lake pambuyo pa imfa yake ndi nkhani yaumwini, koma Mkristu wotchedwa Edward anati: “Ndili ndi inshuwalansi yoti ine ndikadzafa, apabanja langa asanu ndi atatu akapeze thandizo. Mkazi wanga ndiye anasaina kuti ndiye azidzayendetsa za ndalama zanga zakubanki. Choncho, ngati ndimwalira, iye angathe kukatapako ndalama kubankiko. . . . Ndili ndi chikalata chothandiza banja langa ponena za katundu. Ndikadzamwalira, chilichonse chimene ndidzasiya chidzakhala cha mkazi ndi ana anga. Ndinalemba chikalatacho zaka zisanu zapitazo. Chinakonzedwa ndi loya, ndipo mkazi wanga ndi mwana wanga wamwamuna ali ndi kope lake. M’chikalata chimenechi, ndinafotokoza momveka bwino kuti achibale anga asadzayendetse nawo mwambo wa maliro anga. Ndine wa m’gulu la Yehova. Choncho, ngakhale patadzakhala Mboni imodzi kapena ziŵiri zodzayendetsa mwambo wamalirowo, omwewo adzakwanira. Ndafotokoza zimenezi kwa achibale anga onse.”

Kunena zoona, kupanga makonzedwe amenewo ndi mphatso yaikulu ku banja lanu. Inde, kukonzekera za imfa sikungafanane ndi kupereka mphatso wamba. Komabe, zimenezi zimasonyeza chikondi chanu. Zimatsimikizira kuti inuyo mumafunadi ‘kusunga a m’banja lanu’ ngakhale pamene mumwalira.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 21]

Yesu Anapezeratu Wodzathandiza Amayi Wake

“Koma pamtanda [“pamtengo wozunzirapo,” NW] wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Mariya, mkazi wa Kleopa, ndi Mariya wa Magadala. Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu! Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amayi wako. Ndipo kuyambira ola lomweli wophunzirayo [Yohane] anamka naye kwawo.”​—Yohane 19:25-27.

[Chithunzi patsamba 22]

Akristu ambiri amalingalira mozama ndi kuchitapo kanthu mwalamulo pofuna kutetezera mabanja awo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena