Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 11/1 tsamba 29
  • Amene Anali Wotsutsa Aphunzira Choonadi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amene Anali Wotsutsa Aphunzira Choonadi
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Mng’ono Wake wa Yesu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kodi Muli ndi Oda Yokhazikika ya Magazini?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Magazini Amalengeza Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Nsanja ya Olonda—1998
w98 11/1 tsamba 29

Olengeza Ufumu Akusimba

Amene Anali Wotsutsa Aphunzira Choonadi

NKHANI zambiri zasimbidwa ponena za nkhondo yachiweniweni ku Liberia. Anthu zikwi makumi ambiri anataya miyoyo yawo, ndipo ambiri anathaŵa m’dzikomo. Mosasamala kanthu za kuvutikaku, anthu oona mtima akupezabe choonadi, monga mmene chokumana nacho chotsatirachi chikusonyezera.

Kuyambira ali ndi zaka khumi, James ankaphunzitsidwa ndi Tchalitchi cha Lutheran. Atakhala mkonzi wa nyuzipepala ya tchalitchi, iye anagwiritsa ntchito malo akewo kulemba nkhani zotsutsa Mboni za Yehova. Mosasamala kuti anali asanakumanepo ndi mmodzi wa iwo.

M’kupita kwa nthaŵi, James anasiya ntchito ku nyuzipepala ya tchalitchiyo nakhala ndi motela yakeyake yapamwamba. Tsiku lina atakhala pofikira alendo m’motela yakeyo, alongo ena ovala bwino kwambiri aŵiri anamfikira. Poona kuvala kwawo kwaudongoko anawauza kuti aloŵe. Koma pamene anafotokoza chifukwa chimene anafikira, iye anati, “Ndilibe mpata woti tikambirane.” Mbonizo zinamgaŵira sabusikiripishoni ya magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndipo anangolandirira kuti Mbonizo zichoke. Kwa miyezi 12 magaziniwo anabwera kunyumba kwake, koma anangowaika m’chikwama chapulasitiki osawachotsa zikutiro zake.

Nkhondo yachiweniweni ikadali mkati, James analongedza ndalama ndi zinthu zamtengo wapatali m’chikwama kuti athaŵe nazo nkhondo ikangofika. Tsiku lina mmawa, bomba linaphulika pafupi ndi khomo lakuseri kwa nyumba yake, chipolowe chili choncho, anatenga chikwama chake nathaŵa kupulumutsa moyo wake. Atakumana ndi khamu la anthu wamba othaŵa, iye anadutsa malo ofufuzira angapo. Pamalopo, anthu wamba osalakwa anali kulandidwa katundu ndi kuphedwa popanda chifukwa chenicheni.

Atafika pamalo ofufuzira oyamba, James anafunsidwa mafunso ochepa ndipo anauzidwa kutsegula chikwama chake. Atatero, anayang’ana m’chikwamamo ndipo sanakhulupirire. Anazizwa poona kuti chikwama chimene ananyamula sichinali chija chimene chinali ndi zinthu zamtengo wapatali. Chifukwa chosokonezeka, ananyamula chikwama chokhala ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! onse osatsegula. Komabe, pamene msilikali anaona magaziniwo ndi kuŵerenga dzina lake pazikutozo, anati: “O! Ndiwe wa Mboni za Yehova. Sitikufufuza anthu inu, tikudziŵa simunama.” Atatenga magazini angapo m’chikwamamo, msilikaliyo anauza James kudutsa.

Zofananazo zinachitika m’malo asanu ndi anayi ofufuzira, popeza akazembe onse anaganiza kuti James anali wa Mboni za Yehova ndipo anamlola kudutsa popanda kumvulaza. Tsopano James anazindikira kuti anachita bwino kusatenga zinthu zamtengo wapatali zija popeza malinga ndi zimene anaona, pang’onong’ono anakaphedwa chifukwa cha katundu wakeyo.

Pamene anafika pofufuzira pomaliza komanso poopsa kwambiri, anagwidwa nthumanzi kuona mitembo yambirimbiri itangogonagona. Kenako iye anaitanira padzina la Yehova. Anapemphera kuti ngati Mulungu amthandiza kudutsa malo ophera anthuwo, adzamtumikira kwa moyo wake wonse.

James anapereka chikwama chake kwa asilikali, kachiŵirinso anati: “Sitikufufuza anthu inu.” Anatembenukira kwa iye, ndi kumuuzanso kuti: “Mmodzi wa abale ako amakhala mmunsi mwa chitundachi. Pita ukakhale naye.” Panthaŵi imeneyi malingaliro a James kulinga kwa Mboni anali atasinthiratu. Nthaŵi yomweyo anakaonana ndi mbaleyo, ndipo makonzedwe a phunziro la Baibulo anapangidwa m’buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.a

Masiku angapo pambuyo pake, nkhondo inamkakamiza kuthaŵa kumalowo. Tsopano, James anathaŵira kutchire atatenga buku lake la Kukhala ndi Moyo Kosatha lokha! Kwa miyezi 11 yolekanitsidwa ndi Mboni, iye anaŵerenga buku lonse nthaŵi zisanu. Pamene anabwereranso mu mzinda, anapitirizanso kuphunzira Baibulo ndi Mboni ndipo anapita patsogolo kwambiri. Patapita nthaŵi pang’ono, iye anabatizidwa, ndipo tsopano akutumikira mokhulupirika ndi abale ake auzimu.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena