Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w11 6/1 tsamba 32
  • “Kodi Anthu Saliwonongeratu Dziko Lapansili?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kodi Anthu Saliwonongeratu Dziko Lapansili?”
  • Nsanja ya Olonda—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Bwerani Mudzamve Nkhani Yapoyera Yakuti—“Chikhulupiriro ndi Mtsogolo Mwanu”
    Galamukani!—1997
  • Webusaiti Yathu Yovomerezeka Yakonzedwa Kuti Izithandiza Ifeyo Komanso Anthu Ena
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Kupulumutsa Dziko Lapansi ku Kuwonongedwa
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Zokumbutsa za Msonkhano Wachigawo wa 1998 Wakuti: “Njira ya Moyo ya Mulungu.”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2011
w11 6/1 tsamba 32

“Kodi Anthu Saliwonongeratu Dziko Lapansili?”

● Kwa munthu amene ali m’mlengalenga, dziko lapansili limaoneka ngati chinthu chokongola kwambiri. Koma mutafufuza bwinobwino mmene zinthu zilili, mupeza kuti dziko lapansili lili pa mavuto oopsa. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti anthu akulephera kuchita zinthu zimene zingathandize kuti dzikoli likhale malo abwino okhalamo. Komanso anthu akuwononga zinthu monga mpweya ndi madzi, akudula mitengo mwachisawawa ndiponso sakugwiritsa ntchito bwino zinthu za m’dzikoli. Iwo akuwononganso dzikoli chifukwa cha makhalidwe awo oipa monga chiwawa, kuphana ndiponso kuchita chiwerewere.

Zinthu zomvetsa chisoni zimenezi zinaloseredwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo m’maulosi ochititsa chidwi a m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:1-5; Chivumbulutso 11:18) Baibulo linaloseranso kuti Mulungu ndi amene adzakonze zinthu padzikoli, osati munthu wina aliyense. Mfundo zofunika kwambiri zimenezi zidzakambidwa mu nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Kodi Anthu Saliwonongeratu Dziko Lapansili?” Nkhani imeneyi idzakambidwa pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa mutu wakuti, “Ufumu wa Mulungu Ubwere.” Msonkhano umenewu udzachitika m’malo osiyanasiyana padziko lonse lapansi.

Tikukuitanani kuti mudzapite ku msonkhano umene udzachitike pafupi ndi kumene mumakhala. Kuti mudziwe madeti, malo ndiponso nthawi imene msonkhanowu udzachitike, funsani a Mboni za Yehova kudera lanulo kapena lemberani amene amafalitsa magazini ino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena