Bwerani Mudzamve Nkhani Yapoyera Yakuti—“Chikhulupiriro ndi Mtsogolo Mwanu”
Kodi mungadziŵe bwino za mtsogolo mwanu? Kodi pali zomwe mungachite kuti mukonze mmene mudzakhalira?
Nkhani yapoyera, yomwe ndi mbali ya Msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova wakuti “Kukhulupirira Mawu a Mulungu,” idzasonyeza chifukwa chake tiyenera kuyembekezera kuti mtsogolo mudzakhaladi mwabwino. Popeza kuyambira mwezi uno nkhaniyi idzakambidwa pamisonkhano yambiri kuzungulira dziko lonse lapansi, mungathe kukamverako pafupi ndi kwanuko.
Funsani Mboni za Yehova za kwanuko kapena lemberani afalitsi a magazini ano za malo a msonkhano pafupi ndi kwanuko.