“Khulupirirani Yehova” Msonkhano wa Chigawo—Musauphonye Iwo!
Masiku atatu, athunthu opatsa mphoto a malangizo a Baibulo ndi mayanjano opiI ndulitsa Achikristu akukudikirani pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa “Khulupirirani Yehova”. Mkati mwa July, ndi August, misonkhano yokwanira 32 yandandalitsidwa kuzungulira mu Zambia mokha, chotero udzakhalapo umodzi osati kutali ndi nyumba yanu. Konzekerani kukapezekapo kuyambira pa gawo lotsegulira loyamba pa 9:20 a. m. Lachisanu, ndi kukhala kufikira gawo lomaliza pa Sande masana.
Gawo lotsegulira lidzasonyeza nkhani yopatsa chidziwitso “Anthu Odzipatula Kuchokera Ku Dziko.” Masana, uphungu wachindunji ndi wowona mtima udzaperekedwa kwa makolo ndipo kenaka kwa achichepere. Achichepere adzathandizidwa kudzichinjiriza kukhala ndi moyo womwe ungatchedwe moyo wapawiri.” Kenaka nkhani imeneyi idzaunikiridwa mu chitsanzo chodzutsa mtima chamakono.
M’mawa wa Loweruka udzasonyeza nkhani pa kudzipereka ndi ubatizo, limodzinso ndi malangizo munjira zimene tingasonyezere kukhulupirira kwathu Yehova, m’chigwirizano ndi mutu wa msonkhano. “Thayo la Kubala Ana Mu Nthawi Ino Ya Mapeto” idzakhala nkhani yaikulu pa programu ya masana, yomwe idzamaliza ndi nkhani zosiirana pa mutu wakuti “Mawu a Mulungu Ngamoyo.”
Programu ya Sande idzawonetsa nkhani “Danani Nayo Kotheratu Njira Yochititsa Manyazi Ya Dziko,“ limodzinso ndi chitsanzo cha Baibulo chokhala ndi anthu ovala zovala zapachitsanzo kuunikira kufulumira kwa nthawi. M’masana, nkhani yaikulu “Mu Nthawi Zathu Zowopsya, Kodi Ndani Amene Ungakhulupirire Kwenikweni?“ Idzakhala mfundo yeniyeni ya msonkhano.
Fufuzani ndi Mboni za Yehova kwanuko kaamba ka nthawi ndi malo a msonkhano kufupi ndi inu