Musaphonye Msonkhano Wachigawo wa “Chinenero Choyera”!
Masiku anayi ofupa a chilangizo cha Baibulo akukuyembekezerani. Dzapezekenipo pamene programu idzayamba pa 1:30 mmadzulo Lachinayi. Dzasangalaleni ndi nkhani yodzutsa maganizo yakuti “Kodi Mabwenzi Anu Ndiwo Mabwenzi a Yehova?” limodzinso ndi nkhani yaikulu yakuti, “Chinenero Choyera cha Mitundu Yonse.” Nkhani yamasana yomalizira iyi, “Kupulumutsa Moyo Wanu Ndi Mwazi—Motani?,” idzayankha funso lakuti: Kodi mwazi umafunikiradi kupulumutsa moyo?
Gawo lam’mawa pa Lachisanu lidzayamba pa 9:30. Mukapezekeko kuti mukapindule ndi nkhani yosanthula yakuti, “Kristu ‘Anada Kusayeruzika’—Kodi Inu Mumatero?” ndiponso nkhani yogwira mtima yakuti “Kanani Maloto Audziko, Londolani Zenizeni za Ufumu.” Pamasana, malingaliro opindulitsa onena za momwe mungakhalire ndi moyo ndi chuma chomwe muli nacho adzaperekedwa. Makolo adzasonyezedwa mmene angakwaniritsire mathayo awo mokhutiritsa, ndipo drama yamakono idzapereka chitsogozo chabwino koposa kwa achichepere ponena za kutengamo mbali m’maseŵera akusukulu.
Gawo lam’mawa pa Loŵeruka lidzakhala ndi nkhani ya kudzipereka ndi ubatizo, limodzinso ndi kulingalira pa kufunika kwa kudzimana kotero kuti mukhale ndi phunziro Labaibulo laumwini. “Gareta la Yehova Lakumwamba Likuyenda” idzakhala nkhani yochititsa chidwi pa programu yamasana. Ndiponso, padzakhala zokumbutsa zamphamvu zonena za thayo lathu Lachikristu la kuthandiza ochititsidwa khungu ndi chipembedzo chonyenga, ndipo thandizo lopindulitsa la kukwaniritsa thayo limeneli lidzaperekedwa.
Mudzafunikira kukhalapo pa Sande m’mawa kumvetsera ku uthenga wamphamvu umene udzaperekedwa motsutsana ndi Chikristu Chadziko ndi atsogoleri ake achipembedzo. Ichi chidzatsatiridwa ndi drama yamakedzana yovala malaya apadera yozikidwa pa zochitika zokhudza miyoyo ya Yehu ndi Yonadabu. Kenaka, masana, khalani otsimikizira kukamvetsera ku nkhani yapoyera yakuti, “Khalani Ogwirizana mwa Chinenero Choyera.”
Mkati mwa August ndi September, misonkhano 33 yandandalitsidwa kuzungulira Zambia yonse, chotero padzakhala umodzi wosakhala kutali kwambiri ndi kwanuko. Funsani kwa Mboni za Yehova kumaloko kaamba ka nthaŵi ndi malo kumene kudzakhala wapafupi kwambiri ndi kwanuko.