Pezekani ku Msonkhano Wachigawo wa “Okonda Ufulu”!
MASIKU atatu ofupa a chilangizo cha Baibulo akukuyembekezerani. Dzapezekenipo pa 10:20 Lachisanu m’maŵa pamene msonkhano udzayamba ndi nyimbo. Dzasangalaleni ndi nkhani yotsegulira yakuti, “Kodi Nkusuzumiriramonji m’Lamulo Langwiro la Ufulu?,” ndipo mbali yomalizira ya gawo lam’maŵa idzakhala ndi nkhani yaikulu yakuti: “Chifuno ndi Ntchito ya Ufulu Wathu Wopatsidwa ndi Mulungu.”
Pa Lachisanu masana, chenjezo lidzaperekedwa kwa Akristu la kukwaniritsa ntchito yawo monga aminisitala a Mulungu. “Otanganitsidwa—m’Ntchito Zakufa Kapena Muutumiki wa Yehova?” ndi “Anthu Omasuka Koma Oŵerengeredwa” iri iŵiri ya mitu imene idzafutukulidwa. Chilimbikitso chogwiritsira ntchito ufulu wathu kutumikira Yehova chidzaperekedwa m’drama yeniyeni yovala malaya apadera. Idzazikidwa pa zokumana nazo za Ezara ndi anzake omwe anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babulo mu 468 B.C.E. kukakometsera kachisi wa Mulungu.
Gawo lam’maŵa pa Loŵeruka lidzakhala ndi nkhani yosiirana ya mbali zitatu yakuti, “Ufulu Wokhala ndi Thayo m’Banja.” Yotsatira nkhani yofufuza moyo yakuti “Dzisungeni Inumwini Womasuka Kutumikira Yehova” idzakhala nkhani ya kudzipereka Kwachikristu ndi ubatizo. Ambiri masana adzayembekezera mwachidwi mbali yakuti “Kodi Ukwati Ndiwo Mfungulo Kuchimwemwe?” Gawolo lidzamaliza ndi chigogomezero chomwe mosakaikira chidzadzetsa chimwemwe chachikulu kwa onse okonda ufulu.
Mudzafunikira kukhalapo pa Sande m’maŵa kumvetsera nkhani yosiirana ya mbali zitatu yakuti “Kutumikira Monga Asodzi a Anthu.” Imeneyi idzafotokoza fanizo la Yesu la khoka ndi nsomba ndipo idzalongosola mbali imene tingakhale nayo m’kukwaniritsidwa kwake. Gawo lam’maŵa lidzamaliza ndi nkhani zofunika zakuti “Kukhala Ogalamuka ‘m’Nthaŵi Yamapeto’” ndi “Kodi Ndani Adzapulumuka ‘Nthaŵi ya Tsoka’?” Kenaka, masana, simudzafunikira kuphonya nkhani yabaibulo yakuti, “Kulengeza Dziko Latsopano la Mulungu la Ufulu.” Nkhani yomalizira yochititsa nthumanzi isanakambidwe, padzakhala kukambitsirana phunziro la Nsanja ya Olonda la mlunguwo. Bweretsani kope lanu la magazini yophunziridwa mlunguwo.
Mkati mwa August ndi September, misonkhano 46 yandandalitsidwa kuzungulira Zambia yonse, chotero padzakhala umodzi wosakhala kutali kwambiri ndi kwanuko. Funsani kwa Mboni za Yehova kumaloko kaamba ka nthaŵi ndi malo kumene kudzakhala wapafupi kwambiri ndi kwanuko.