Chifukwa Chimene Muyenera Kupezeka pa Msonkhano Wachigawo wa “Kudzipereka Kwaumulungu”
Masiku atatu odzetsa mfupo a chilangizo cha Baibulo akukudikirani pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa “Kudzipereka Kwaumulungu” wodzayamba mu August. Kupyolera mu nkhani zolangiza ndi kufunsana ndi drama, chitsogozo chofunika cha Baibulo chidzaperekedwa. Khalanipo pa 9:00 Lachisanu m’mawa pamene msonkhano udzayamba ndi kuperekedwa kwa nyimbo.
Programu ya Lachisanu m’mawa idzapereka nkhani yakuti “Kupeŵa Milomo Yolakwa” ndi nkhani yofunika koposa ya chiyambi cha chipunzitso cha Utatu. M’masana, makolo adzachenjezedwa kulandira thayo lawo la makhalidwe kupereka kwa ana awo choloŵa chauzimu. Chotsatira, achichepere adzalimbikitsidwa kupanga Kristu kukhala chitsanzo chawo ndi kupanga chowonadi kukhala chawochawo. Programu ya tsikulo idzamaliza ndi kukambitsirana kwa makonzedwe aakulu amene akupangidwa mwapadera kuthandiza achichepere.
Loŵeruka lidzakhala tsiku lina lathunthu la chilangizo lomwe lidzapereka ubatizo m’mawa ndipo masana nkhani zofunika koposa zonena za Bungwe Lolamulira Lachikristu ndi mmene tingagwirizanirane nalo lerolino. Magawo a masana adzamaliza ndi nkhani yofunika koposa yakuti “Baibulo—Mawu a Mulungu kapena a Munthu?”
Sande m’mawa, chilangizo chapanthaŵi yake chidzachenjeza motsutsana ndi “munthu wosayeruzika” ndipo motsutsana ndi kusochera mu nkhani za chakudya ndi chakumwa, kapesedwe, ndi zosangulutsa. (2 Atesalonika 2:3) Ichi chidzatsatiridwa ndi drama yamakono yogogomezera kufunika kwa kudzigonjetsera ife eni kwa Mulungu. Kenaka, simudzafunikira kuphonya nkhani ya Baibulo, “Chipulumutso Chiri Pafupi kaamba ka Anthu a Kudzipereka Kwaumulungu!”
Mkati mwa August, ndi September, misonkhano 37 yandandalitsidwa mkati mwa Zambia mokha, chotero padzakhala umodzi osati kutali ndi kwanu. Fufuzani ndi Mboni za Yehova kumaloko kaamba ka nthaŵi ndi malo a umene uli kufupi kwambiri ndi inu.
[Chithunzi patsamba 32]
Msonkhano wachigawo mu Verona, Italy