Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 4 tsamba 5
  • Baibulo Linasungidwa Ngakhale Kuti Ena Ankalitsutsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Baibulo Linasungidwa Ngakhale Kuti Ena Ankalitsutsa
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Nkhani Yofanana
  • William Tyndale—Munthu Woona Patali
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mmene Baibulo Linadzafikira kwa Ife—Mbali Yachiŵiri
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Baibulo Linatsutsidwa Kwambiri
    Galamukani!—2011
  • Baibulo la William Tyndale la Anthu
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 4 tsamba 5

NKHANI YA PACHIKUTO | BAIBULO​—BUKU LOMWE LINAPULUMUKA M’ZAMBIRI

Baibulo Linapulumuka Ngakhale Kuti Ena Sankalifuna

VUTO LIMENE LINALIPO: Atsogoleri ambiri andale komanso azipembedzo sankafuna kuti anthu adziwe uthenga wa m’Baibulo. Choncho iwo ankagwiritsa ntchito udindo wawo poletsa anthu kumasulira, kusindikiza ngakhalenso kukhala ndi Baibulo. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri:

  • Cha m’ma 167 B.C.E.: Mfumu Antiyokasi Epifanasi yemwe ankafuna kukakamiza Ayuda kuti azitsatira chipembedzo chachigiriki, analamula kuti Malemba onse Achiheberi awonongedwe. Wolemba mbiri wina dzina lake Heinrich Graetz, ananena kuti nduna za mfumuyi “zikapeza mipukutu ya Chilamulo, zinkaing’amba ndiponso kuitentha nthawi yomweyo. Komanso zinkapha aliyense amene wapezeka akuwerenga Baibulo pofuna kulimbikitsidwa ndiponso kutonthozedwa.”

  • Zaka za m’ma 500 mpaka 1500: Atsogoleri ena achikatolika ankakhumudwa chifukwa choti anthu a m’chipembedzochi ankalimbikitsa ena kutsatira mfundo za m’Baibulo m’malo mwa zikhulupiriro zachikatolika. Iwo ankafuna kuti anthu aziwerenga buku la Masalimo la m’Chilatini basi. Ndipo anthu wamba omwe anali ndi mabuku ena a m’Baibulo, ankawanena kuti ndi ampatuko. Pamsonkhano wina wa tchalitchichi anasankha anthu oti “azifufuza mwakhama anthu ampatuko . . . m’nyumba ndiponso m’zipinda zonse zapansi, zomwe ankazikayikira kuti akusungirako mabuku a m’Baibulo. . . . Ndipo nyumba iliyonse yomwe apezako wampatuko, aziigwetsa.”

Anthuwa akanakwanitsadi kuwononga Baibulo, ndiye kuti uthenga wake ukanatheranso pomwepo.

Tsamba la m’Baibulo lachingelezi lomasuliridwa ndi William Tyndale

Baibulo lachingelezi lomasuliridwa ndi William Tyndale, linapulumuka ngakhale kuti pa nthawiyi Mabaibulo ena analetsedwa komanso kuwotchedwa. William anaphedwa mu 1536.

ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE: Ngakhale kuti Mfumu Antiyokasi inkafuna kuti Baibulo lisapezekenso ku Isiraeli, Ayuda ambiri anali atasamukira m’mayiko osiyanasiyana. Ndipotu akatswiri amanena kuti pomwe inkafika nthawi ya Yesu, n’kuti Ayuda oposa 60 pa 100 alionse akukhala m’madera a kunja kwa dziko la Isiraeli. Ayudawa ankasunga mipukutu ya Malemba m’masunagoge awo ndipo ndi yomwenso anthu ena kuphatikizapo Akhristu, ankaigwiritsa ntchito.​—Machitidwe 15:21.

M’zaka za m’ma 500 mpaka 1500, anthu ena analimba mtima n’kulolera kuzunzidwa ndipo anapitiriza kumasulira ndi kukopera Baibulo pamanja. Zikuoneka kuti pofika cha m’ma 1400, mabuku ena a m’Baibulo ankapezeka m’zinenero pafupifupi 33, ngakhale kuti pa nthawiyi kunalibe makina osindikizira mabuku. Patapita nthawi, anthu anayamba kumasulira komanso kusindikiza Mabaibulo m’zinenero zinanso zambiri.

ZOTSATIRA ZAKE: M’nkhaniyi taona kuti atsogoleri ena andale komanso azipembedzo ankafuna kuwononga Baibulo, koma sizinatheke. Baibulo lamasuliridwa komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse. Lathandizanso mayiko ambiri pa nkhani zokhudza malamulo ndi zinenero. Komanso lathandiza anthu ambiri kusiya makhalidwe oipa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena