Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 4 tsamba 4
  • Baibulo Linasungidwa Bwino Kuti Lisawole

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Baibulo Linasungidwa Bwino Kuti Lisawole
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Timafunikiradi Oyambirirawo?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Umboni wa Kusungidwa kwa Umulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Bukulo Linapulumuka Bwanji?
    Buku la Anthu Onse
  • Baibulo Linapulumuka Modabwitsa
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 4 tsamba 4

NKHANI YA PACHIKUTO | BAIBULO​—BUKU LOMWE LINAPULUMUKA M’ZAMBIRI

Baibulo Linasungidwa Bwino Kuti Lisawole

VUTO LIMENE LINALIPO: Anthu omwe ankalemba komanso kukopera mipukutu ya Baibulo ankagwiritsa ntchito gumbwa komanso zikopa. (2 Timoteyo 4:13) Komatu zimenezi zikanachititsa kuti mipukutuyi iwonongeke mosavuta. N’chifukwa chiyani tikutero?

Gumbwa amang’ambika, kusuluka komanso kutha mosavuta. Richard Parkinson ndi Stephen Quirke, anaphunzira zinthu zosiyanasiyana za ku Egypt ndipo anati: “Gumbwa akhoza kuwola n’kutsala ulusi kapenanso fumbi lokhalokha. Mpukutu ukakhala nthawi yaitali umachita nkhungu kapenanso kuwola chifukwa cha chinyezi ndipo akaukwirira umadyedwa ndi chiswe.” Komanso mipukutu ina ya gumbwa itapezeka, sinasungidwe bwino ndipo inawonongeka chifukwa cha chinyezi komanso kuwala.

Mipukutu ya chikopa imakhala yolimba kusiyana ndi ya gumbwa. Koma nayonso imawonongeka ikasungidwa pamalo otentha, achinyezi kapenanso owala kwambiri.a Mipukutuyi imadyedwanso ndi tizilombo. Buku lina linanena kuti: “Kawirikawiri mipukutu yakale siikhalitsa.” (Everyday Writing in the Graeco-Roman East) Choncho zikanakhala kuti mipukutu ya Baibulo inawola, uthenga wake ukanatheranso pomwepo.

ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE: Lamulo lachiyuda linkalimbikitsa mfumu iliyonse kuti izikopera “buku lakelake la chilamulo” lomwe ndi mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo. (Deuteronomo 17:18) Komanso pofika chakumapeto kwa nthawi ya atumwi n’kuti akatswiri okopera malemba atakopera mipukutu yambiri. Zimenezi zinathandiza kuti malemba azipezeka m’masunagoge a ku Isiraeli ngakhalenso kumadera akutali monga ku Makedoniya. (Luka 4:16, 17; Machitidwe 17:11) Komano zinatheka bwanji kuti mipukutuyi isungidwe mpaka pano?

1. Mtsuko; 2. Chidutswa cha mpukutu wa ku nyanja yakufa

Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inasungidwa kwa zaka zambiri m’mitsuko yomwe inaikidwa m’mapanga, m’madera ouma

Phanga lomwe kunapezeka mipukutu ina ya Baibulo

Katswiri wina wa Chipangano Chatsopano dzina lake Philip W. Comfort ananena kuti: “Ayuda ankakonda kusunga mipukutu m’mitsuko n’cholinga choti isawonongeke.” Ndipo zikuoneka kuti Akhristu nawonso ankachita zomwezo chifukwa mipukutu ina yoyambirira ya Baibulo inapezeka m’mitsuko, m’zipinda zamdima ndi m’mapanga a m’madera otentha kwambiri.

ZOTSATIRA ZAKE: Mipukutu yambiri ya Baibulo idakalipo ndipo yakhalapo kwa zaka zoposa 2,000. Kunena zoona palibenso mipukutu ya mabuku ena akale yomwe yakhalapo kwa nthawi yaitali chonchi.

a Mwachitsanzo, chikalata cholengeza kuti dziko la United States ndi lodziimira palokha (U.S. Declaration of Independence), chinalembedwa pachikopa. Panopa padutsa zaka zosapitirira 250 kuchokera nthawi yomwe chikalatachi chinalembedwa, koma zilembo zake zimavuta kuwerenga chifukwa zinafufutika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena