NKHANI YOPHUNZIRA 23
‘Samalani Kuti Wina Angakugwireni’
“Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.”—AKOL. 2:8.
NYIMBO NA. 96 Buku la Mulungu Ndi Chuma
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Malinga ndi Akolose 2:4, 8, kodi Satana amagwiritsa ntchito chiyani pofuna kutipusitsa?
SATANA amafuna kuti tisiye kukonda Yehova. Pofuna kukwaniritsa cholinga chakechi, amayesetsa kusokoneza maganizo athu kuti tiziyendera zofuna zake. Iye amagwiritsa ntchito zimene timalakalaka pofuna kutikopa kuti tizimumvera.—Werengani Akolose 2:4, 8.
2-3. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira chenjezo la pa Akolose 2:8? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Kodi n’zotheka kuti Mkhristu apusitsidwe ndi Satana? Inde. Kumbukirani kuti Paulo sanapereke chenjezo la pa Akolose 2:8 kwa anthu osakhulupirira. Koma analipereka kwa Akhristu odzozedwa ndi mzimu woyera. (Akol. 1:2, 5) Ngati Akhristu akalewo akanatha kupusitsidwa, kuli bwanji ifeyo masiku ano? (1 Akor. 10:12) Paja Satana anaponyedwa padziko lapansi ndipo akuyesetsa kusocheretsa atumiki okhulupirika a Mulungu. (Chiv. 12:9, 12, 17) Komanso tikukhala pa nthawi imene anthu oipa ndiponso onyenga ‘akuipiraipirabe.’—2 Tim. 3:1, 13.
3 Munkhaniyi tikambirana mmene Satana amagwiritsira ntchito “chinyengo chopanda pake” pofuna kutisokoneza maganizo. Tiona zinthu zitatu zachinyengo zimene amagwiritsa ntchito pochita zimenezi. (Aef. 6:11) Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene zingatithandize ngati tasokonezedwa kale ndi maganizo komanso zochita za Satana. Tsopano tiyeni tikambirane zimene Satana anachita kuti apusitse Aisiraeli atalowa m’Dziko Lolonjezedwa komanso zimene tikuphunzirapo.
ANAWAKOPA KUTI AYAMBE KULAMBIRA MAFANO
4-6. Mogwirizana ndi Deuteronomo 11:10-15, kodi Aisiraeli anafunika kusintha chiyani pa nkhani ya ulimi atalowa m’Dziko Lolonjezedwa?
4 Satana anachita zinthu mochenjera pokopa Aisiraeli kuti ayambe kulambira mafano. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iye ankadziwa kuti Aisiraeliwo ankafunikira chakudya ndipo anagwiritsa ntchito zimenezi kuti awakope. Aisiraeli atalowa m’Dziko Lolonjezedwa anafunika kusintha njira zawo zaulimi. Ali ku Iguputo, iwo ankathirira mbewu zawo ndi madzi ochokera mumtsinje wa Nailo. Koma m’Dziko Lolonjezedwa anthu sankathirira mbewu. Iwo ankadalira mvula komanso mame. (Werengani Deuteronomo 11:10-15; Yes. 18:4, 5) Choncho Aisiraeli ankafunika kuphunzira njira zatsopano zaulimi. Koma sizinali zophweka kuphunzira chifukwa anthu ambiri amene ankadziwa zaulimi anali atafa m’chipululu.
Kodi Satana anasokoneza bwanji maganizo a Aisiraeli pa nkhani yaulimi? (Onani ndime 4-6)b
5 Yehova atauza anthu ake kuti zinthu zasintha pa nkhani yaulimi, anawapatsa chenjezo lomwe lingaoneke ngati losagwirizana ndi zaulimizi. Iye anati: “Samalani kuti mitima yanu isakopeke ndipo musapatuke ndi kupembedza milungu ina n’kumaiweramira.” (Deut. 11:16, 17) N’chifukwa chiyani Yehova anachenjeza anthu ake kuti asamalambire milungu yonyenga pa nthawi imene ankawauza zokhudza njira zatsopano zaulimi?
6 Yehova ankadziwa kuti Aisiraeli angafune kuphunzira njira zaulimi kwa anthu osalambira Mulungu omwe ankakhala nawo pafupi. N’zoona kuti anthuwo akanathandiza Aisiraeliwo kuti aphunzire zambiri zokhudza ulimi koma panafunika kusamala. Tikutero chifukwa alimi a ku Kanani anali atasokonezedwa ndi kulambira Baala. Iwo ankaona kuti Baala ndi mwini kumwamba komanso wopereka mvula. Yehova sankafuna kuti anthu ake apusitsidwe ndi zikhulupiriro zabodzazo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri Aisiraeli ankalambira Baala. (Num. 25:3, 5; Ower. 2:13; 1 Maf. 18:18) Apatu Satana anakwanitsa kuwapusitsa.
ZINTHU ZITATU ZIMENE SATANA ANAGWIRITSA NTCHITO POPUSITSA AISIRAELI
7. Kodi Aisiraeli anayesedwa bwanji atafika m’Dziko Lolonjezedwa?
7 Chinthu choyamba chimene Satana anagwiritsa ntchito chinali mtima wofuna kuti mvula igwe, womwe aliyense akhoza kukhala nawo. M’dziko Lolonjezedwa simunkagwa mvula yambiri kuyambira kumapeto kwa April kufika mu September. Anthu ankadalira mvula yomwe inkayamba mu October kuti apeze chakudya komanso kuti zinthu ziziyenda bwino pa moyo wawo. Satana anachititsa Aisiraeli kuganiza kuti zinthu zingawayendere bwino ngati atatengera zimene anthu a m’dzikolo ankachita. Anthuwo ankakhulupirira kuti pamafunika kuchita miyambo ina kuti milungu yawo ibweretse mvula. Aisiraeli amene sankadalira Yehova ankakhulupiriranso kuti kuchita nawo miyambo yolemekeza Baala n’kumene kukanathandiza kuti apewe chilala.
8. Kodi chinthu chachiwiri chimene Satana anagwiritsa ntchito chinali chiyani? Fotokozani.
8 Kodi chinthu chachiwiri chimene Satana anagwiritsa ntchito chinali chiyani? Iye anagwiritsa ntchito chilakolako chawo cha kugonana. Anthu a m’dzikolo ankachita chiwerewere akamalambira milungu yawo. Iwo anafika pokhala ndi mahule aakazi ndi aamuna apakachisi. Sankaona vuto lililonse ndi zinthu zoipa monga kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. (Deut. 23:17, 18; 1 Maf. 14:24) Anthuwo ankaganiza kuti zimenezi zinkathandiza kuti milungu yawo ichititse nthaka kukhala yachonde. Aisiraeli ambiri anakopeka ndi miyambo yachiwerewereyo moti anayamba kulambira milungu yonyenga. Apa tingati Satana anakwanitsa kuwagwira kuti akhale akapolo ake.
9. Malinga ndi Hoseya 2:16, 17, kodi Satana anachititsa bwanji Aisiraeli kuti aziona Yehova molakwika?
9 Kodi chinthu chachitatu chimene Satana anagwiritsa ntchito chinali chiyani? Iye anachititsa Aisiraeli kuti aziona Yehova molakwika. M’masiku a Yeremiya, Yehova ananena kuti aneneri onyenga ankachititsa kuti anthu ake aiwale dzina lake “chifukwa cha Baala.” (Yer. 23:27) Zikuoneka kuti anthu a Mulungu anasiya kugwiritsa ntchito dzina la Yehova n’kuyamba kugwiritsa ntchito dzina loti Baala, lomwe limatanthauza “Mwini wake” kapena “Ambuye.” Izi zinachititsa kuti ziziwavuta kusiyanitsa pakati pa Yehova ndi Baala. Choncho zinali zosavuta kuti azisakaniza kulambira Baala ndi kulambira Yehova.—Werengani Hoseya 2:16, 17 ndiponso mawu am’munsi apalembali.
ZIMENE SATANA AMAGWIRITSA NTCHITO MASIKU ANO
10. Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira ziti masiku ano?
10 Satana akugwiritsabe ntchito njira zomwezi masiku ano. Iye amagwira anthu powakopa ndi zinthu monga zimene aliyense amalakalaka, chiwerewere ndiponso kuchititsa anthu kuti aziona Yehova molakwika. Tiyeni tiyambe ndi kukambirana njira yomalizirayi.
11. Kodi Satana amachititsa bwanji anthu kuti aziona Yehova molakwika?
11 Satana amachititsa anthu kuti aziona Yehova molakwika. Atumwi atamwalira, anthu ena amene ankati ndi Akhristu anayamba kufalitsa zinthu zabodza. (Mac. 20:29, 30; 2 Ates. 2:3) Ampatukowa anachititsa kuti anthu asadziwe bwinobwino za Mulungu woona. Mwachitsanzo, anasiya kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo, n’kuikamo mayina ngati “Ambuye.” Kuchotsa dzina la Mulungu n’kuika mawu akuti “Ambuye” kunasokoneza anthu chifukwa sankaona kusiyana pakati pa Yehova ndi “ambuye” ena otchulidwa m’Baibulo. (1 Akor. 8:5) Iwo ankagwiritsa ntchito mawu oti “Ambuye” ponena za Yehova komanso Yesu. Choncho anthu sankazindikira kuti pali kusiyana pakati pa Yehova ndi Mwana wake ndipo maudindo awo ndi osiyananso. (Yoh. 17:3) Zimenezi zinachititsa anthu kuti ayambe kuphunzitsa mfundo yosemphana ndi Malemba yakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Zotsatira zake n’zakuti anthu amaganiza kuti Mulungu ndi wosamvetsetseka ndipo n’zosatheka kumudziwa. Ilitu ndi bodza lamkunkhuniza.—Mac. 17:27.
Kodi Satana wagwiritsa ntchito bwanji chipembedzo chonyenga kuti anthu azichita chiwerewere? (Onani ndime 12)c
12. Kodi chipembedzo chonyenga chimalimbikitsa chiyani, nanga zotsatira zake n’zotani malinga ndi Aroma 1:28-31?
12 Satana amagwiritsa ntchito chilakolako cha kugonana chimene anthu amakhala nacho. Kale, Satana anagwiritsa ntchito chipembedzo chonyenga pofuna kuti Aisiraeli achite chiwerewere. Izi n’zimene amachitanso masiku ano. Chipembedzo chonyenga chimalekerera khalidwe lachiwerewere komanso kulilimbikitsa. Izi zachititsa kuti anthu amene amati amalambira Mulungu asiye kutsatira mfundo zake za makhalidwe abwino. M’kalata yake yopita kwa Aroma, mtumwi Paulo anafotokoza zotsatira zake. (Werengani Aroma 1:28-31.) Zina mwa ‘zinthu zosayenera’ zimene anthu akuchita ndi zachiwerewere. Mwachitsanzo, iwo amavomereza kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. (Aroma 1:24-27, 32; Chiv. 2:20) Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tizitsatira mfundo zosavuta kumva za m’Baibulo.
13. Kodi Satana amagwiritsanso ntchito njira iti popusitsa anthu?
13 Satana amakopa anthu ndi zinthu zimene aliyense amalakalaka. Mwachibadwa, anthufe timalakalaka kuphunzira zinthu zimene zingatithandize kupeza zofunika pa moyo wathu komanso wa banja lathu. (1 Tim. 5:8) Kuti tiphunzire zinthu zimenezi, timafunika kupita kusukulu komanso kulimbikira maphunziro. Koma tiyenera kusamala pa nkhani imeneyi. M’mayiko ambiri, masukulu amaphunzitsa anthu luso la ntchito komanso nzeru za anthu. Zimene anthu amaphunzitsidwa zimawachititsa kukayikira zoti kuli Mulungu komanso kuti asamatsatire mfundo za m’Baibulo. Amaphunzitsidwa kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. (Aroma 1:21-23) Mfundo zimenezi n’zosemphana kwambiri ndi nzeru yochokera kwa Mulungu.—1 Akor. 1:19-21; 3:18-20.
14. Kodi nzeru za m’dzikoli zimasokoneza bwanji anthu?
14 Nzeru za anthu zimakhala zosemphana kwambiri ndi mfundo za Mulungu zachilungamo. Sizilimbikitsa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa koma “ntchito zathupi.” (Agal. 5:19-23) Zimachititsa anthu kukhala onyada ndipo zotsatira zake n’zakuti anthu ambiri amakhala “odzikonda.” (2 Tim. 3:2-4) Makhalidwe amenewa ndi osiyana kwambiri ndi makhalidwe amene atumiki a Yehova amalimbikitsidwa kukhala nawo monga kudzichepetsa. (2 Sam. 22:28) Akhristu ena amene anapita kuyunivesite anasokonezedwa kwambiri moti amayendera nzeru za anthu m’malo moyendera maganizo a Mulungu. Tiyeni tingokambirana chitsanzo chimodzi pa nkhaniyi.
Kodi maganizo athu angasokonezedwe bwanji ndi nzeru za m’dzikoli? (Onani ndime 14-16)d
15-16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mlongo wina?
15 Mlongo wina amene wachita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 15 anati: “Ndine Mkhristu wobatizidwa ndipo ndakhala ndikuwerenga za mavuto amene angabwere chifukwa chopita kuyunivesite. Koma ndinanyalanyaza malangizowa poganiza kuti sakundikhudza.” Kodi chinachitika n’chiyani atapita kuyunivesite? Iye anati: “Ndinkatanganidwa kwambiri ndi maphunziro moti sindinkapeza nthawi yokwanira yoti ndipemphere kwa Yehova mmene ndinkachitira kale. Ndinkatopa kwambiri moti zinkandivuta kukambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo kapena kukonzekera misonkhano. Mwamwayi, ndinazindikira kuti kutanganidwa ndi maphunzirowo kunkasokoneza ubwenzi wanga ndi Yehova moti ndinasiya.”
16 Koma kodi maphunziro apamwamba anasokoneza bwanji maganizo ake? Mlongoyu anati: “N’zomvetsa chisoni kuti maphunzirowa anandichititsa kuti ndizingopezera zifukwa abale ndi alongo. Ndinkaona kuti abale ndi alongowo sachita bwino zinthu zambiri komanso ndinkawapewa. Zinanditengera nthawi yaitali kwambiri kuti ndisinthe maganizo amenewa. Zimene zinachitikazi zandithandiza kuzindikira kuti kunyalanyaza malangizo amene Atate wathu wakumwamba amatipatsa kudzera m’gulu lake n’koopsa kwambiri. Yehova amandidziwa bwino kuposa mmene ndimadzidziwira ndekha. Zikanakhala bwino ndikanamvera poyambapo.”
17. (a) Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
17 Tiyeni tizichita zonse zimene tingathe kuti tipewe kutsatira “nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake” zimene zimapezeka m’dziko la Satanali. Nthawi zonse tizikhala osamala kuti Satana asatigwire ngati nyama. (1 Akor. 3:18; 2 Akor. 2:11) Tisalole kuti atichititse kuona Yehova molakwika. Nthawi zonse tizitsatira mfundo zapamwamba za Yehova. Ndipo tisalole kuti Satana atipusitse n’kusiya kutsatira malangizo a Mulungu. Koma kodi mungatani ngati maganizo am’dzikoli akusokonezani kale? Nkhani yotsatira idzatisonyeza mmene Mawu a Mulungu angatithandizire kuti tichotse “zinthu zozikika molimba” zimene zili m’maganizo athu.—2 Akor. 10:4, 5.
NYIMBO NA. 49 Tizikondweretsa Mtima wa Yehova
a Satana ndi katswiri pa nkhani yopusitsa anthu. Iye wapangitsa anthu ambiri kuganiza kuti ali pa ufulu, pomwe ndi akapolo ake. Munkhaniyi tikambirana misampha imene Satana amagwiritsa ntchito kuti apusitse anthu.
b MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Aisiraeli akucheza ndi anthu a ku Kanani ndipo akunyengereredwa kuti ayambe kulambira Baala komanso kuchita chiwerewere.
c MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Chikwangwani chosonyeza tchalitchi chololeza kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.
d MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo wapita kuyunivesite. Iye ndi anzake akopeka ndi maganizo a mphunzitsi wawo oti asayansi akhoza kuthetsa mavuto a m’dzikoli. Kenako wapita ku Nyumba ya Ufumu koma sizikumusangalatsa ndipo akungopezera anthu zifukwa.