Sanaleke Kuchitira Umboni
1 Dzina lathulo, Mboni za Yehova, limatidziŵikitsa ndi kufotokoza zimene timachita. Timachitira umboni zoposa za Mulungu wathu, Yehova. (Yes. 43:10, 12) Aliyense ayenera kukhala ndi phande m’kupereka umboni umenewu ngati ati akhale chiŵalo cha mpingo. Kwakukulukulu umboni umachitidwa mwa utumiki wathu wapoyera, umene umaphatikizapo kufikira nyumba ndi nyumba, kuchita ntchito ya m’khwalala, kupanga maulendo obwereza, ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo. Tonsefe tikufulumizidwa moyenerera kukalimira kukhala ndi phande lokwanira.—1 Akor. 15:58.
2 Komabe, ziŵalo zina za mpingo nzosakhoza kuchita zambiri. Matenda aakulu kapena thanzi lofooka lingawachititse kukhala obindikiritsidwa. Achibale otsutsa angadzetse zopinga zazikulu. Wachichepere angaletsedwe ndi kholo losakhulupirira. Anthu okhala kumadera akutali kopanda zoyendera angakhale osoŵa chochita. Manyazi achibadwa angachititse anthu amantha kuwopa. Ofalitsa ena amene amapezeka m’mikhalidwe imeneyi kapena yofanana nayo angalingalire kuti sakuyenerera kukhala Akristu chifukwa chakuti zimene ali okhoza kuchita nzochepa kwambiri koposa zimene ena akuchita ndiponso nzochepa kwambiri koposa zimene akufunadi kuchita. Palibe chifukwa chakuti iwo achepse zoyesayesa zawozo. (Agal. 6:4) Iwo angatonthozedwe podziŵa kuti Yehova amakondwera pamene apereka zawo zonse zimene angathe mu mkhalidwe uliwonse umene alimo.—Luka 21:1-4.
3 Kupeza Njira ya Kugaŵana ndi Ena: Zokumana nazo zambirimbiri zasimbidwa zosonyeza mmene anthu ena okhala ndi mikhalidwe yovuta sanalolere zopinga kuwaletsa kuchitira umboni. Pogwiritsira ntchito luso lawo, iwo alinganiza njira zambiri zosiyanasiyana zochitira umboni wamwamwaŵi. Awo obindikiritsidwa panyumba agwiritsira ntchito telefoni kutsegula khomo lalikulu la kuchitira umboni. Wodzawaona aliyense amaonedwa monga munthu amene akhoza kumvetsera. Ngakhale kuti mkazi wokhala ndi banja lotsutsa sangakhale wokhoza kuchitira umboni panyumba, iye amagwiritsira ntchito mipata ya kukambitsirana ndi anansi kapena ndi ena amene amakumana nawo m’zochita zake zatsiku ndi tsiku.
4 Munthu wachichepere angaletsedwe ndi kholo losakhulupirira kukhala ndi phande m’kuchitira umboni kwathu kwapoyera. Mmalo mwa kungovomereza zimenezo kukhala chopinga chachikulu, iye angaone anzake a m’kalasi ndi aphunzitsi monga “gawo” lake ndipo akhoza kupereka umboni wabwino kwambiri ndipo mwinamwake kuchititsadi maphunziro a Baibulo. Ambiri a amene amakhala kumadera akutali akhoza kukhala ndi phande mwa kulemba makalata. Awo amene amasonkhezeredwa ndi changu Chachikristu nthaŵi zonse adzapeza njira ina yopeŵera kukhala “aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye wathu Yesu Kristu.”—2 Pet. 1:8.
5 Ponena za kukhala ndi phande kwathu mu ntchito yochitira umboni, Yehova waika muyezo wofanana kwa onse, ndiko kuti, tiyenera kukhala “amtima wonse.” (Akol. 3:23, NW) Ngakhale kuli kwakuti kuchuluka kwa nthaŵi imene timatha ndi zimene timakwaniritsa zidzasiyana, chisonkhezero chake nchofanana—chikondi chenicheni chimene chimachokera mu “mtima wangwiro.” (1 Mbiri 28:9; 1 Akor. 16:14) Ngati tikupereka zimene tingathe, sitidzakhala ndi chifukwa cholingalirira kuti tilibe chikhulupiriro kapena kuti tili opanda ntchito monga ziŵalo za mpingo chifukwa chakuti zinthu zimene tikuchita nzochepa. Mofanana ndi Paulo, ife moonadi tinganene kuti ‘sitinabise zinthu zopindulira, osazilalikira ndi kuphunzitsa pabwalo.’—Mac. 20:20.