Kupenda Kolemba m’S̃ukulu Yautumiki Wateokratiki
Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogawiridwa kuyambira mlungu wa May 2 kufikira August 22, 1994. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Tonsefe tingayembekezerebe kuloŵa m’mavuto ovuta kwambiri mkati mwa masiku otsala otsiriza ameneŵa a dongosolo lakale la Satana. [om-CN tsa. 162 ndime 3]
2. Malinga ndi kunena kwa Salmo 15:4, ngati Mkristu adziŵa kuti chinachake chimene analonjeza sichili chogwirizana ndi malemba, ayenera kuchichitabe. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 9/15 mas. 28-9.]
3. Mkati mwa nthaŵi za tsoka monga ngati njala, mtumwi Paulo anali wokhoza kulinganiza mphatso za chithandizo kotero kuti chilichonse chichitidwe molongosoka. [om-CN tsa. 158 ndime 2]
4. Njira ya moyo ya Yesu inatsimikizira kuti Adamu akanasunga umphumphu wangwiro ngati akanafuna kutero ndi kuti panalibe cholakwika ndi ntchito ya kulenga ya Mulungu. [uw-CN tsa. 52 ndime 11]
5. Tauni ya Kana, yokhala m’mapiri pafupi ndi Nazarete, kumene Yesu mwiniyo anakulira, ndiko kunali kwawo kwa Natanayeli. [gt-CN mutu 15]
6. Mwa kugwira ntchito zolimba ndi kudzipereka kotheratu kwa Mulungu, Mkristu woona akhoza kupeza kuyenera kwa moyo wosatha. [uw-CN tsa. 36 ndime 11]
7. Pa 1 Akorinto 2:9 pamanena za dziko lapansi la Paradaiso lamtsogolo. [uw-CN tsa. 26 ndime 12 (3); onani w86-CN 3/1 tsa. 30.]
8. Sitingakhoze kuona mkhalidwe wa kusakhulupirika kukhala wosanunkha kanthu, ngakhale kuti uli wofala m’dziko. [uw-CN tsa. 53 ndime 13]
9. Salmo 49:15 lili mawu osonyeza chikhulupiriro m’chiyembekezo cha chiukiriro. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 3/1 tsa. 22 ndime 13.]
10. Nthaŵi zina chinyengo cha kuloŵa mu mkhalidwe wadziko chimachokera kwa munthu wina amene amadzinenera kuti akutumikira Yehova. [uw-CN tsa. 43 ndime 11]
Yankhani mafunso otsatirawa:
11. Kodi chipiriro nchiyani? [om-CN tsa. 164 ndime 1]
12. Kodi ndi chitsimikizo chabwino chotani chimene Salmo 27:10 limatipatsa? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 3/15 tsa. 22 ndime 17.]
13. Kodi Salmo 10:13 limavumbula lingaliro lolakwika lotani limene ochita zoipa osalapa ali nalo? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 11/1 tsa. 6.]
14. Malinga ndi kunena kwa Eksodo 9:15, 16, kodi nchiyani chimene chinakwaniritsidwa mwa kachitidwe ka Yehova ndi Farao? [uw-CN tsa. 57 ndime 6, 7]
15. Tchulani malingaliro aŵiri amene tingapendere mopindulitsa zimene tikuŵerenga m’Baibulo. [uw-CN tsa. 27]
16. Kodi lamulo lakuti “mpsompsoneni Mwanayo” limatanthauza chiyani, monga momwe lalembedwera pa Salmo 2:12? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 7/1 tsa. 8.]
17. Kodi ndi kumasuka kwamtundu wanji kumene Yesu anali kulongosola pa Yohane 8:32? [uw-CN tsa. 40 ndime 6]
18. Kodi ndani amene akuimiridwa ndi “mkazi” pa Genesis 3:15? [uw-CN tsa. 30 ndime 3]
19. Kodi nchifukwa ninji Davide ananena kwa Yehova pa Salmo 51:4 kuti, “Pa inu, inu nokha, ndinachimwa,” pamene anadziŵa kuti machitidwe ake ochimwa anachitidwa kwa anthu anzake? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 3/15 tsa. 11 ndime 13.]
20. Kodi munthu wochiritsidwayo analephera bwanji kumvera Yesu, ndipo kodi zotulukapo zake zinali zotani? (Luka 5:12-16) [gt-CN mutu 25]
Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Pa Yobu 40:9, “kugunda” kumayenerera bwino ndi ․․․․․․․ aakulu, ndipo pa Yobu 41:29, ‘ziputu’ mwachionekere zimasonya ku ․․․․․․․otsalira m’munda pambuyo pa kukolola. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani it-2 mas. 1040 ndi 1098.]
22. Ponena za kututa ․․․․․․․, Yesu anati: “Kwezani anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta. Wakumweta alandira kulipira, ․․․․․․․ chobala ku moyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.” [gt-CN mutu 19]
23. Mu ․․․․․․․, apongozi a ․․․․․․․ akudwala kwambiri malungo. Chotero Yesu apita pafupi nawo, nawagwira dzanja, nawadzutsa. Pomwepo akuchiritsidwa nayamba kuwakonzera chakudya! [gt-CN mutu 23]
24. Popeza kuti Satana anagwiritsira ntchito bodza kuchititsa makolo athu oyamba kuloŵa m’tchimo, Yesu anamutcha ‘ ․․․․․․․.’ [uw-CN tsa. 53 ndime 13 (1)]
25. Yesu ali Mwana ․․․․․․․ wa Mulungu chifukwa chakuti ali iye yekha amene analengedwa ndi Yehova mwini. [uw-CN tsa. 29 ndime 1]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Yobu anaona Mulungu, monga kwalembedwa pa Yobu 42:5, mwanjira yakuti iye (anali ndi masomphenya a Mulungu mu chimphepo; anaona mngelo amene anamuonekera; anafikira pakudziŵa Yehova mokwanira). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 8/15 tsa. 12 ndime 11.]
27. Yesu anakwapula ogulitsa nyama pa kachisi mu Yerusalemu chifukwa chakuti (anali kugulitsa mkati mwenimweni mwa kachisi ndipo anali kubera anthu mwakuwalipiritsa ndalama zambiri; anali kupereka nsembe za nyama pakachisi; sanafune kumvetsera kwa iye). [gt-CN mutu 16]
28. Maziko amene agwetsedwa, monga kwalembedwa pa Salmo 11:3, akunena za (maziko a kachisi ku Yerusalemu; Yesu Kristu monga Mwala Wapangondya; maziko pamene chitaganya chimaimapo, monga ngati chiweruzo cholungama, chilamulo, ndi malangizo). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 7/1 tsa. 8.]
29. Yesu akutha (masiku 20 usana ndi usiku; masiku 40 usana ndi usiku; mwezi umodzi) m’chipululu ndipo sakudya kanthu mkati mwa nthaŵi imeneyi. [gt-CN mutu 13]
30. Nkhani yaikulu imene Satana anadzutsa pamene anatokosa kuyenera kwa Mulungu kwa kulamulira ndi njira Yake ya kulamulira kwenikweni inaphatikizapo (zoyenerera za anthu; funso lakuti ndani anali wamphamvu koposa; ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Mulungu). [uw-CN tsa. 46 ndime 1]
Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Gen. 3:1-5; Sal. 24:1; Mac. 8:32-38; Aheb. 10:26, 27; 1 Pet. 4:3, 4
31. Kuzindikira kuti munthu ndi dziko lapansi zili zolengedwa za Mulungu ndi kuti zonse nza Yehova kuyenera kutithandiza kukhala odzichepetsa ndi omvera. [uw-CN tsa. 39 ndime 4]
32. Tiyenera kukhala osamala kwambiri kupeŵa kuloŵa m’chizoloŵezi cha kuchita chilichonse chimene tikudziŵa kuti sichimakondweretsa Yehova. [uw-CN tsa. 33 ndime 8 (3) ndi 8 (4)]
33. Chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo ndi chiyamikiro cha uthenga wake chimasonkhezera anthu onga nkhosa kubatizidwa. [uw-CN tsa. 32 ndime 7]
34. Ngakhale kuti mungamagwire ntchito ndi osakhulupirira kapena kupita nawo kusukulu, mumasonyeza kuti simuwasankha monga mabwenzi mwa kupeŵa mayanjano osayenerera ndi iwo. [uw-CN tsa. 44 ndime 13]
35. Nkofunika kuti tipeŵe kulingalira kwadziko kumene kumasonkhezera anthu kukhulupirira kuti akumanidwa kanthu kena ngati sadziikira miyezo yawoyawo m’moyo. [uw-CN tsa. 46 ndime 1]
S-97-CN-ZAM & MAL #283 8/94