Futukulani Chuma Chanu cha Utumiki wa Ufumu
1 Yesu anayerekezera chiyembekezo cha Ufumu ndi chuma chamtengo wapatali. (Mat. 13:44-46) Kodi ife tili ngati amuna a m’mafanizo a Yesu amene anagulitsa chuma chawo chonse kuti agule kanthu kena kofunika koposa? Ngati tili otero, tidzaika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba, ngakhale kuti zimenezi zingaloŵetsemo mavuto ndi kudzimana.—Mat. 6:19-22.
2 Popeza kuti utumiki wathu wa Ufumu ndiwo chuma, chikhumbo chathu chiyenera kukhala cha kuufutukula. Kodi njira yathu m’moyo imasonyezanji? Kodi tikufutukula ntchito yathu ya Ufumu? Tingatero mwa kukhala ndi phande m’mbali zosiyanasiyana za utumiki, kuphatikizapo ntchito ya kunyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza, kuchititsa maphunziro a Baibulo, ndi kuchitira umboni wamwamwaŵi.
3 ‘Kodi Ndingafutukule Bwanji Mbali Yanga?’ Popeza kuti chaka chatsopano chautumiki chayamba, ndi bwino kuti aliyense wa ife apende ntchito ya iyemwini kuona zimene angachite kuti awonjezere nthaŵi yotheredwa mu utumiki wakumunda ndi kufunsa kuti: ‘Kodi ndingathe kulinganiza zochita zanga kotero kuti ndidzilembetsa monga mpainiya wothandiza panthaŵi ndi nthaŵi kapena ngakhale mopitiriza? Nditapanga kusintha kungapo, kodi ndingaloŵe mu utumiki wa upainiya wokhazikika?’ Apainiya atsopano amene amalembetsa podzafika September 1 amayenerera kuloŵa Sukulu Yautumiki Waupainiya chaka chotsatira.
4 Ofalitsa ena aika chonulirapo chaumwini cha kuchita zowonjezereka m’kuchitira umboni kwamwamwaŵi. Kaŵirikaŵiri ntchito imeneyi imabala zipatso zabwino kwambiri. Ena angalingalire zowongolera mmene angapangire maulendo obwereza ogwira mtima kapena kuyambitsa maphunziro a Baibulo atsopano.
5 Ngati tilingalira kuti utumiki wathu ngwochepa m’njira ina, kodi tingachitenji kuti tiufutukule? Awo amene afikira zonulirapo zapamwamba mwachipambano akupereka lingaliro lakuti ife choyamba tiyenera kutsimikiza kuika zinthu za Ufumu poyamba, zivute zitani. (Mat. 6:33) Chikhulupiriro ndi chidaliro cholimba pa Yehova nzofunika. (2 Akor. 4:7) Pemphani thandizo lake kupyolera m’pemphero loona mtima ndi lakhama. (Luka 11:8, 9) Tingakhale ndi chidaliro chakuti Yehova adzadalitsa zoyesayesa zathu zoona mtima za kuwonjezera phande lathu mu utumiki wake.—1 Yoh. 5:14.
6 Kambitsiranani ndi abale ndi alongo ena amene afutukula utumiki wawo mwachipambano. Afunseni mmene anakhozera kugonjetsa zopinga popanda kulefuka. Zokumana nazo zawo zingakhaledi zimene zikufunika kukukhutiritsani kuti utumiki wofutukuka ungathe kufikiridwa.
7 Pamene muŵerenga nkhani za mu Nsanja ya Olonda kapena za mu Utumiki Wathu Waufumu zonena za utumiki wakumunda, lingalirani mwapemphero za mmene mungagwiritsirire ntchito malingalirowo mu utumiki wanu. Chitani chimodzimodzinso pamene muli pa misonkhano ya mpingo kapena pa misonkhano yadera. Malingaliro operekedwa mu nkhani ino achokera m’nkhani imene inali mbali ya programu ya msonkhano wadera wa chaka chatha. Ndiyo yoyamba mu mpambo wa nkhani zolinganizidwira kutithandiza kutsatira ndi kugwiritsira ntchito chilimbikitso choperekedwa m’programuyo.
8 Yesu anaona mwamphamvu kwambiri utumiki wake, akumaupanga kukhala nkhaŵa yake yaikulu. Iye analengeza kuti: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.” (Yoh. 4:34) Kodi timalingalira mofananamo? Ngati timatero, ndithudi ife tidzapeza njira zofutukulira ntchito yathu ndi kuuza ena “zabwino” zochokera mosungiramo chuma chathu.—Mat. 12:35; Luka 6:45.