Asonkhezereni Kukhala Otsatira Ake
1 Pa 1 Akorinto 3:6, Paulo analemba kuti: “Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa.” Paulo anagwiritsira ntchito ganizo limeneli kuthandiza abale ake kuona kufunika kwa kugwira ntchito mogwirizana pansi pa umutu wa Kristu. Mwa njira imeneyi anawathandizanso kuzindikira mbali yaikulu imene iwo anali nayo m’ntchito ya kuoka ndi kuthirira.
2 Ntchito yopulumutsa moyo imeneyo ifunika kumalizidwa m’tsiku lathuli. Pokhala Akristu odzipatulira, tili ndi thayo lalikulu la kuthandiza ena kukhala otsatira a Yesu. (Mac. 13:48) Kodi ndimotani mmene mudzatsatirira chikondwerero chimene munadzutsa mwa kugwiritsira ntchito buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako?
3 Ngati mwabwerera kukacheza ndi munthu amene analandira bukulo, mukhoza kunena kuti:
◼ “Nthaŵi ija pamene tinakambitsirana, tinakambitsirana zakuti kodi Yesu Kristu anali munthu wotani. Ndinakondwera kwambiri kukusiyirani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Kodi ndi mbali ziti ponena za kuphunzitsa kwa Yesu ndi umunthu wake zimene zakukhudzani mtima kwambiri?” Yembekezerani yankho. Tsegulani pa mutu 113, ndipo kambitsiranani chitsanzo chabwino koposa cha kudzichepetsa chimene Yesu anapereka. Ŵerengani Afilipi 2:8 kuti musonyeze mmene mtumwi Paulo anaonera mkhalidwe wa maganizo wa kudzichepetsa umene Yesu anali nawo. Ndiyeno mukhoza kufotokoza mmene angaphunzirire zambiri kupyolera m’phunziro la Baibulo la nthaŵi zonse.
4 Mwina mungakonde mawu oyamba otsatirawa:
◼ “Tinakambitsirana zimene Yesu anachita pamene anali padziko lapansi zimenenso zimasonyeza kuti iye amatisamaliradi. Kodi muganiza adzachita chiyani potsiriza pake kuti athandize awo amene akuvutika kwambiri?” Yembekezerani yankho. Tsegulani pa mutu 133, ndipo pendani ndemanga zimene zili m’ndime yachisanu. Sonyezani chithunzi chimene chili patsamba lotsatira, ndipo fotokozani mmene zinthu zidzakhalira pamene chifuniro cha Mulungu chidzachitidwa padziko lapansi pano monga kumwamba. Tchulani mapindu amene angapezedwe mwa kuphunzira zambiri.
5 Ngati paulendo woyamba simunagaŵire bukulo chifukwa chakuti munthuyo sanasonyeze chikondwerero chokwanira, mwinamwake mungayambe kukambitsirana motere:
◼ “Ndikhulupirira kuti inuyo ndi ine tikuvomereza kuti anthu ambiri lerolino amatsanzira munthu wina amene amamuyesa kukhala chitsanzo chawo. Yesu Kristu ndiye chitsanzo chabwino kwambiri kuposa chilichonse chimene wina angakhale nacho. Lolani ndikuuzeni phunziro lofunika kwambiri limene ndaliphunzira mwa kupenda chitsanzo chimene Yesu anatiikira. [Tsegulani pa mutu 40 m’buku la Munthu Wamkulu, ndipo sonyezani phunziro labwino la chifundo limene Yesu anapereka.] Limeneli linandikumbutsa kwambiri zimene ndifunikira kuti ndisonyeze mkhalidwe umenewu kwa ena.” Ŵerengani Mateyu 5:7. Gaŵirani bukulo kapena brosha la Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
6 Kapena mungafune kuyesa kafikidwe kolunjika kotsatiraka:
◼ “Pamene ndinali kuno tsiku lija, tinakambitsirana za kufunika kwa kupeza chidziŵitso ponena za Yesu. Yohane 17:3 amanena kuti kupeza chidziŵitso chotero ‘ndiko moyo wosatha.’ Kodi tingachipeze motani?” Yembekezerani yankho. Pitirizani mwa kufotokoza makonzedwe athu a phunziro la Baibulo ndi mmene angapindulire nawo.
7 Paulo akunena kuti wogwira ntchito ya kututa “adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.” (1 Akor. 3:8) Ngati tiyesetsa zolimba pothandiza ena kukhala otsatira a Yesu, mphotho yathu idzakhaladi yaikulu.