Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/94 tsamba 8
  • Itanirani Ena Kudzatsatira Munthu Wamkulu Koposa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Itanirani Ena Kudzatsatira Munthu Wamkulu Koposa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 3 Kapena munganene zonga izi:
  • 4 Nali lingaliro lina:
  • 5 Mwina mungafune kugwiritsira ntchito zonga izi:
  • Zitsanzo za Maulaliki a Utumiki wa Kumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Asonkhezereni Kukhala Otsatira Ake
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Kuchitira Umboni kwa “Anthu Onse”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
km 12/94 tsamba 8

Itanirani Ena Kudzatsatira Munthu Wamkulu Koposa

1 Monga momwe kwalembedwera pa Mateyu 5:14, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi.” Otsatira a Yesu anafunikira kuuza anthu kulikonse za Ufumu wa Yehova ndi makonzedwe Ake achikondi a chipulumutso mwa Yesu. Ndi ntchito imeneyo m’maganizo, tikuyembekezera mwachidwi kugaŵira buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako m’mwezi wa December. Nawa malingaliro ena amene mungafune kugwiritsira ntchito.

2 Mutatchula dzina lanu, mukhoza kunena zotsatirazi m’mawu anu:

◼ “Anthu ambiri afuna kudziŵa kuti Yesu anali wotani pamene anali ndi moyo padziko lapansi monga munthu. Kodi muganiza kuti iye anali wosiyana motani ndi ena? [Yembekezerani yankho.] Buku lochititsa chidwi limeneli, la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, likusimba zochitika zazikulu za moyo ndi utumiki wake, ndipo limasonyeza umunthu umene iye anali nawo. Ena ataliŵerenga, amaona ngati kuti anali ndi mpata wa kuyanjana naye mwaumwini, kuvutika naye, ndi kudzionera okha utumiki wake.” Sonyezani chithunzi choyamba m’bukulo, chimene chikusonyeza mutu wake. Ndiyeno tsegulani pa mawu oyamba, ndi kuŵerenga ndime yachiŵiri pakamutu kakuti “Pindulani mwa Kuphunzira za Iye.” Gaŵirani bukulo pachopereka cha K15.00.

3 Kapena munganene zonga izi:

◼ “Nthaŵi ino anthu akuganiza za Yesu. Komabe, popeza kuti padziko lapansi pakuchitika zinthu zambiri zoipa, anthu ena angakayikire ngati Yesu amatisamaliradi. Muganiza bwanji?” Yembekezerani yankho. Tsegulani pa mutu 24 m’buku la Munthu Wamkulu, ndipo fotokozani mwachidule chifukwa chake Yesu anadza padziko lapansi. Ndiyeno ŵerengani Yohane 15:13, kugogomezera chikondi chochokera mumtima chimene Yesu ali nacho kwa ena. Musaiŵale kunyamula magazini atsopano, brosha, kapena trakiti loyenera zimene muyenera kukhala nazo kuti mugaŵire ngati bukulo silinatengedwe.

4 Nali lingaliro lina:

◼ “Achichepere ambiri akufunafuna anthu akuti atengere chitsanzo chawo, koma anthu a chitsanzo chabwino ngovuta kupeza. Yesu Kristu anaika chitsanzo changwiro kaamba ka aliyense. [Ŵerengani 1 Petro 2:21.] Iye anasumika moyo wake wonse pa kulambira Atate wake wakumwamba. Kodi muganiza kuti zikanakhala bwanji ngati anthu ambiri akanayesayesa kumtsanzira?” Yembekezerani yankho. Sonyani ku ndime yachitatu patsamba lachiŵiri kuchokera kumapeto a bukulo, imene ikulongosola mikhalidwe yake yapadera. Fotokozani mmene buku la Munthu Wamkulu lingathandizire tonsefe kukhala Akristu abwinopo.

5 Mwina mungafune kugwiritsira ntchito zonga izi:

◼ “Pamene wina wangotchula Yesu Kristu, anthu ambiri amaganiza za iye monga khanda kapena monga munthu womavutika amene ali pafupi kufa. Zimene iwo adziŵa ponena za Yesu ndizo kubadwa kwake ndi imfa yake basi. Kaŵirikaŵiri zinthu zodabwitsa zimene iye ananena ndi kuchita samazizindikira. Zimene anakwaniritsa zimayambukira munthu aliyense amene wakhalapo padziko lapansi. Chifukwa chake kuli kofunika kwa ife kuchita zimene tingathe kuphunzira zochuluka ponena za zinthu zabwino kwambiri zimene anatichitira.” Ŵerengani Yohane 17:3. Tsegulani patsamba loyamba la mawu oyamba a buku la Munthu Wamkulu, ndipo ŵerengani ndime yachinayi. Muuzeni mmene angapezere bukulo ndi mmene angaligwiritsirire ntchito pa phunziro laumwini.

6 Musaiŵale kukhala ndi cholembapo anthu osonyeza chikondwerero ndi zimene mwagaŵira kotero kuti mudzakhoze kubwererako pamaulendo obwereza. Pamene kukali nthaŵi, tiyeni mwachangu tifunefune anthu oona mtima ndi kuwathandiza kukhala otsatira a Mpulumutsi wathu, Yesu Kristu.—Mat. 16:24.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena