Samalirani Chiphunzitso Chanu Nthaŵi Zonse
1 Programu yatsopano ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki idzayamba m’January 1995. M’chaka chimenecho mabuku a Ogwirizana m’Kulambiridwa kapena Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu ndiwo adzagwiritsiridwa ntchito m’nkhani yachilangizo. Popeza kuti sikudzakhala mafunso openda pambuyo pa nkhani yachilangizo yotengedwa m’buku la Uminisitala Wathu, kodi nchiyani chimene tingachite kuti tisamalire chiphunzitso chathu ndi kupeza mapindu ochuluka?—1 Tim. 4:16, NW.
2 Ngakhale kuti ambiri anaŵerenga kale mabuku a Uminisitala Wathu ndi Ogwirizana m’Kulambiridwa, kupenda nkhani zake zosonyezedwa m’ndandanda ya sukulu kudzathandiza onse kuzindikira kwambiri choloŵa chawo cha teokrase. (Sal. 71:17, 18) Bwanji osapatula nthaŵi mlungu uliwonse ya kupenda zigawo zogaŵiridwa m’mabuku ameneŵa?
3 Nkhani Zachilangizo Zaumoyo ndi Zokondweretsa: Nkhani zachilangizo zotengedwa m’mabuku a Uminisitala Wathu ndi Ogwirizana m’Kulambiridwa ziyenera kukambidwa mwaumoyo ndi mokondweretsa. Ziyeneranso kusonyeza phindu lake la chidziŵitso chimenecho, kuzigwiritsira ntchito kuzamitsa kumvetsetsa kwathu Mawu a Mulungu ndi kuwagwiritsira ntchito kwambiri m’miyoyo yathu. Tidzathandizidwanso kukhala ndi chithunzi chokwana bwino cha mmene mpingo Wachikristu ukugwirira ntchito lerolino. Ngati banja lililonse limene lipezeka pa Sukulu libwera ndi mabuku ameneŵa ku msonkhano, ziŵalo za banja zikhoza kuitsatira bwino kwambiri nkhani yachilangizo ndi kupindula ndi mfundo zimene zikukambidwa.
4 Kuŵerenga Baibulo Kosonkhezera Maganizo: Kuŵerenga kwabwino, limodzi ndi kugogomezera ganizo koyenera ndi kusonyeza mzimu wake, kuli mbali yofunika ya kuphunzitsa kogwira mtima. Ndiponso, chigawo choŵerengedwa m’Nkhani Na. 2 sichachikulu kwambiri, ndipo nthaŵi zonse padzakhala nthaŵi yokwanira yolola mlankhuli kukamba mawu oyamba ndi omaliza. Mawu oyamba ayenera kudzutsa chikondwerero mwa omvetsera pa nkhani yogaŵiridwayo ndi kuwakonzekeretsa kuona phindu lake. Mawu omaliza ayenera kuphatikizapo ndemanga ndi tanthauzo la nkhaniyo, ndipo mlankhuliyo akumagwiritsira ntchito nthaŵi yonse yogaŵiridwa.
5 Chidziŵitso chowonjezera chonena za programu ya sukulu ndi mmene nkhani ziyenera kukambidwira chili mu “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1995.” Timasamalira chiphunzitso chathu mwa kupenda malangizo a m’ndandandayo, mwa kukonzekera bwino nkhani zathu, ndi mwa kugwiritsira ntchito uphungu umene timapatsidwa, kuti tiwongolere luso lathu la kulankhula ndi kuphunzitsa. Amene sanalembetsebe sukulu akupemphedwa mokoma mtima kuchita zimenezo.