Pindulani ndi Pologalamu ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 1999
1 Yesu anali Mphunzitsi Wamkulu. Anthu “anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Marko 1:22) Ngakhale kuti palibe aliyense wa ife amene angalankhule ndi kuphunzitsa ngati mmene anachitira Yesu, tingayesetse kumtsanzira. (Mac. 4:13) Motero, tidzathandizidwa kupitirizabe kukulitsa maluso athu a kulankhula ndi kuphunzitsa pamene tikhala pa pologalamu ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase.
2 Mu 1999, Nkhani Na. 1 idzatengedwa makamaka m’nkhani za m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 1997. Tidzamvetsetsa zinthu zauzimu bwino kwambiri ngati tiŵerengeratu nkhanizi pasadakhale ndiyeno nkukazimvetsera pa pologalamu ya sukulu. Amene agaŵiridwa nkhani zachilangizo zimenezi ayenera kusonyeza mmene nkhaniyo ingagwiritsidwire ntchito, akumaikamba mosangalatsa ndi mogwira mtima. Nkhani Na. 3 idzachokera m’buku la Chimwemwe cha Banja ndipo Nkhani Na. 4 idzachokera m’buku la Munthu Wamkulu, ngakhale kuti Nkhani Na. 3 ingatengedwenso m’buku la Munthu Wamkulu ndiponso Nkhani Na. 4 ingatengedwenso m’buku la Chimwemwe cha Banja. Woyang’anira sukulu ayenera kulingalira mosamalitsa pa nkhani iliyonse asanaigaŵire kwa munthu. Ophunzira onse amene akupatsidwa nkhani zochokera m’buku la Chimwemwe cha Banja ayenera kukhala opereka chitsanzo chabwino pamoyo wawo wabanja.
3 Gwiritsani Ntchito Uphungu, Ndipo Konzekerani Bwino: Aliyense angawongolere luso lake la kulankhula ndi kuphunzitsa. (1 Tim. 4:13) Motero tizifunafuna uphungu ndipo tisamauone ngati chinthu chofunika kuchizemba. (Miy. 12:15; 19:20) Kulongosola choonadi mogwira mtima pamisonkhano kapena mu utumiki wakumunda kumafuna zoposa kungofotokoza mfundo kapena kungoŵerenga malemba chabe. Timafunika kufika pamtima ndi kusonkhezera omvetsera athu. Tingachite zimenezi mwa kulankhula choonadi mokhutiritsa kuchokera mumtima mwathu. (Yerekezerani ndi Machitidwe 2:37.) Uphungu umene timalandira m’sukulu udzatithandiza kukwaniritsa zimenezi.
4 Mutangopatsidwa nkhani, ganizirani za uphungu wakulankhula umene mudzagwirirapo ntchito monga mmene walongosoledwera mu Bukhu Lolangiza la Sukulu. Ganizirani zimene muyenera kuchita kuti mugwiritse ntchito uphungu umene munalandirapo kale. Sinkhasinkhani za mutu wankhani yanu, za mmene mungakakhalire pa pulatifomu, ndi mmene mudzagwiritsira ntchito malemba amene ali m’nkhani yanu. Lingalirani mmene mungagwiritsire ntchito bwino kwambiri chidziŵitsocho kuti muphunzitse ndi kusonkhezera ena.—1 Tim. 4:15, 16.
5 Ngati mukuchita mantha kulembetsa sukulu, pemphererani nkhaniyo ndiyeno mfotokozereni maganizo anu wochititsa sukuluyo. Aliyense angapindule mwa kupezerapo mwayi pa pologalamu ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase imene idzachitidwa mu 1999.