Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/95 tsamba 1
  • Kristu Monga Chitsanzo cha Achichepere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kristu Monga Chitsanzo cha Achichepere
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Utumiki wa Nthaŵi Zonse Umasangalatsa
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Utumiki Waupainiya—Kodi Ngoyenera Inu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 6/95 tsamba 1

Kristu Monga Chitsanzo cha Achichepere

1 Pambuyo pa kukambitsirana Baibulo kwanthaŵi yaitali, wachichepere wina anati: “Ndinachita chidwi ndi umunthu wamphamvu wa Yesu Kristu. Ameneyu ndiye mtsogoleri amene ndingamdalire.” Mawu amenewo sanganenedwe ponena za mtsogoleri aliyense wa dziko kapena ngwazi zamaseŵero ndi zosangulutsa. Akristu enieni samalingalira anthu amenewo amene poyera amalandira miyezo yadziko ndi moyo wotsutsana ndi Chikristu kukhala zitsanzo zabwino.—Sal. 146:3, 4.

2 Achichepere angatsimikizire kuti pamene asonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Kristu, amadzisonyeza kukhala nkhosa za Mulungu ndipo amadziŵidwa ndi Yesu. Mbusa Wabwinoyo amawasamalira. (Yoh. 10:14, 15, 27) Achichepere amene amatsatira Kristu monga Chitsanzo chawo ngodala.

3 Mbale wina amene pakali pano akutumikira pa Beteli ya Brooklyn anali ndi chonulirapo cha mwaŵi wa utumiki umenewu kuyambira pamene anali ndi zaka zisanu ndi zitatu. Analimbikitsidwa kulingalira utumiki wa pa Beteli kukhala njira yogwira ntchito ya kutsatira chitsanzo cha Kristu atasinkhuka. Makolo ake, ndiponso oyang’anira oyendayenda, anamthandiza kuika chonulirapo chimenechi patsogolo pake. Kuti amthandize kukonzekera, anamlimbikitsa kuchita zinthu mwakhama monga chiŵalo cha banja la Beteli, kumagwira ntchito zapanyumba, kuthandiza kukonza Nyumba Yaufumu, ndi kukulitsa maluso osiyanasiyana mu utumiki. Pambuyo pa kusangalala ndi utumiki wa pa Beteli kwa zaka zambiri tsopano, iyeyo ngwothokoza kuti pamene anali kukula, anayesayesa kutsanzira chitsanzo cha Kristu.

4 Yesu sanalondole ntchito ya kudziko; anasankha utumiki. Mlongo wina wachichepere anafuna kuchita upainiya pamene anamaliza sukulu komano anazengereza chifukwa cha kusapeza ntchito yoyenera ya maola ochepa. Iye ankangolingalira kuti: ‘Ndipeze ntchito choyamba, ndiyeno ndidzapereka fomu yanga yaupainiya.’ Mkulu wina anamsonyeza kuti pamene ayembekezera kwanthaŵi yaitali, mpamenenso adzakhumba kuloŵa ntchito ya maola atsiku lonse, popeza kuti sipadzakhala chilichonse chomletsa kuivomera. Mlongoyo anasimba kuti: “Ndinapempha Yehova mzimu wake kuti unditsogolere.” Nthaŵi yomweyo analembetsa kukhala mpainiya wothandiza ndipo pambuyo pake anakhala mpainiya wokhazikika. Posapita nthaŵi, iyeyo anapeza ntchito yoyenera imene inaloleza mndandanda wake wa upainiya.

5 Yesu analengeza molimbika za uthenga wa Ufumu kwa aliyense. (Mat. 4:23) Akristu achichepere angaphunzirenso kukhala olimbika polalikira, osaopsezedwa ndi ena. Mboni ina yazaka 14 inasimba kuti: “Aliyense kusukulu amadziŵa za kaimidwe kanga monga Mkristu. . . . Amadziŵa bwino kwambiri kwakuti ngati ndikumana ndi wa m’kalasi mnzanga pamene ndili mu utumiki, sindimachita manyazi. Kaŵirikaŵiri ophunzira anzanga amamvetsera, ndipo nthaŵi zambiri amalandira mabuku.”

6 Kulingalira za chitsanzo cha Kristu kungathandize achichepere kupanga zosankha zanzeru ponena za mtsogolo mwawo. M’malo mwa kukhala otanganitsidwa ndi kulondola zadziko, iwo ‘amakumbukira Mlengi wawo’ mwa kusonyeza changu mu utumiki wa Yehova. (Mlal. 12:1) Monga Kristu Yesu, akukulitsa “chikondi cha Atate,” chimene chimadzetsa madalitso abwino kwambiri kuposa chilichonse chimene dziko lingapereke. M’malo mwa ‘kupita’ ndi dziko lakale, iwo angayembekezere ‘kukhalako ku nthaŵi zonse.’—1 Yoh. 2:15-17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena