Bwererani Kuti Mukapulumutse Ena
1 Chili chifuniro cha Mulungu kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Tim. 2:4) Kodi tingachitenji kuti tiwathandize? Pangani maulendo obwereza ndi cholinga cha kukaphunzitsa choonadi. Kodi mudzanenanji? Malingaliro otsatirawa angakuthandizeni.
2 Pamene mwafikira munthu amene anaombola buku la “Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?” mungatsegulenso pachithunzithunzi cha patsamba 4 ndi kufunsa mwini nyumbayo kuti:
◼ “Pamene munapenda mowonjezereka buku limene ndinakusiyirani ndi kusinkhasinkha pa lonjezo la Mulungu la dziko laparadaiso, kodi mukulingalira bwanji ponena za malonjezo abwino kwambiri ameneŵa amene Mulungu wapereka kwa anthu?” Mutayamikira yankho la mwini nyumbayo ndi kuthirirapo ndemanga mwachidule, mungatsegule pa mitu 2 ndi 3 ndi kupereka lingaliro lakuti mukambitsirane za chifukwa chake zoyesayesa za anthu kuti abweretse mtendere ndi chisungiko, kuphatikizapo zija zachipembedzo, zalephera.
3 Ngati munasiya mwini nyumba akudabwa chifukwa chake Mulungu akulekerera kuipa mungapitirize kukambitsiranako mwa kunena kuti:
◼ “Ndinasangalala pa kukambitsirana kwathu pamene tinakumana poyamba paja, ndipo ndabweranso kuti ndidzaone zimene mukulingalira ponena za chifukwa chimene Mulungu walekerera mavuto ndi chiwawa kuchitika m’dziko lerolino. [Yembekezerani yankho. Tsegulani ndi kuŵerenga ndime 25 patsamba 54 m’buku la Mtendere Weniweni, kuphatikizapo mawu ogwidwa pa 2 Petro 3:8, 9.] Onani kuti mutu wotsatira m’bukulo ukufunsa kuti, ‘Kodi Mulungu Wakhala Akuchitanji?’ Mwinamwake tingakambitsirane za yankho la funso limenelo paulendo wanga wotsatira.”
4 Mungabwererenso kwa munthu amene munamgaŵira buku la “Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe” ndi kafikidwe aka:
◼ “Pamene ndinakufikirani nthaŵi yoyamba, ndinachita chidwi ndi nkhaŵa yanu kaamba ka banja lanu. Popeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza a dongosolo loipa la zinthu, nkofunika kuti mabanja akonzekere zamtsogolo. Ndi cholinga chimenecho, buku limene ndinakusiyirani, lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe, limalimbikitsa kwambiri za kukambitsirana Baibulo panyumba nthaŵi zonse. [Ŵerengani ndime 10 pamasamba 185-6.] Ngati mungandilole, ndingakonde kutenga mphindi zoŵerengeka chabe kuti ndikusonyezeni mmene anthu a m’maiko oposa 200 amakambitsirana za Baibulo panyumba monga banja.” Ngati nthaŵi ilola, fotokozani mfundo zimene zili pakamutu kamene kali patsamba 70 kuti musonyeze mmene phunzirolo limachitidwira.
5 Mukhoza kubwerera kwa munthu amene munamgaŵira buku la “Chisungiko cha Padziko Lonse” mwa kunena kuti:
◼ “Ndafikanso kuti ndidzakusonyezeni zambiri ponena za chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansili.” Tsegulani pachithunzithunzi cha patsamba 172-3, ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4, ndiyeno fotokozani mwachidule mmene Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsira lonjezo limeneli. Mpempheni kuchita naye phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.
6 Kumbukirani kuti chonulirapo cha kupanga maulendo obwereza ndicho kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Buku latsopano lakuti, Knowledge That Leads to Everlasting Life, lalinganizidwa makamaka kuchititsira maphunziro. Pamene tibwerera kwa amene tinawagaŵira mabuku akale ndi kuyambadi kuphunzira nawo, ndi bwino kuwasonyeza buku latsopano limeneli. Tidzapeza chisangalalo chambiri pamene awo amene akuphunzira adziŵa kuitana pa dzina la Yehova kaamba ka chipulumutso.—Mac. 2:21.