Pindulani ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996—Mbali 2
1 Sukulu Yautumiki Wateokratiki itangoyamba mu 1943, nthambi ina ya Sosaite inasimba kuti: “Makonzedwe abwino ameneŵa akhala opambana m’nyengo yaifupi pothandiza abale ambiri amene ankalingalira kuti sadzakhala konse alankhuli apoyera kukhala olankhula mogwira mtima kwambiri pa pulatifomu ndi ogwira mtima kwambiri m’munda.” Sukuluyo ikupitiriza kupereka maphunziro abwino kwambiri, amene ife tonse timafuna.
2 Kuŵerenga Baibulo: Awo amene amapatsidwa nkhani zoti akambe si iwo okha amene amapindula ndi sukuluyi. Kwenikweni, tonsefe timagaŵiridwa zochita—kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu. Ndandanda ya sukulu imasonyeza machaputala a Baibulo amene tiyenera kuŵerenga mlungu uliwonse. Pali zikumbutso zambiri za m’Malemba zimene zimagogomezera kufunika kwa kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. (Yos. 1:8; Sal. 1:2; Mac. 17:11) Kuŵerenga Baibulo kuli kofunika pa thanzi labwino lauzimu; kumamanga maganizo ndi mtima. Ngati tiŵerenga Baibulo mosachepera pa mphindi zisanu patsiku, tidzakhala okhoza kuyenderana ndi kuŵerengedwa kwake. Pamapeto a chaka, tidzakhala titaŵerenga machaputala oposa 150 a Mawu a Mulungu. Ngati tikhala ndi Baibulo pafupi, tidzakhala okhoza kuŵerenga mbali yake ina tsiku lililonse.
3 Nkhani Yolangiza: Kuti asonkhezere abale kuchita utumiki wokhulupirika ndi wachangu, mlankhuli amene amapereka nkhani yolangiza afunikira kugwiritsira ntchito njira zabwino zophunzitsira, kuti awazindikiritse, ndi kukulitsa chiyamikiro pa Yehova, Mawu ake, ndi gulu lake. Akulu ndi atumiki otumikira angachite zimenezi mwa kukonzekera bwino, akumagogomezera nkhani yawo pa mutu wake, kulankhula mokhutira, ndi kuchititsa nkhaniyo kukhala yaumoyo. (Aheb. 4:12) Nkofunika kuti mlankhuli asunge nthaŵi yake. Buku la “Ogwirizana m’Kulambiridwa” nlodzala malemba a m’Baibulo ndipo limapereka mpambo wa nkhani za m’Malemba zokondweretsa zimene tingapindule nazo mwauzimu. Buku la Olinganizidwa limatisonyeza mathayo athu aakulu a m’Malemba ndipo limafotokoza chidziŵitso chofunika kwa onse chonena za ntchito ya akulu ndi atumiki otumikira, ndi mbali zosiyanasiyana za dongosolo la Mpingo. Pali zambiri zoti tiphunzire.
4 Mfundo Zazikulu za Baibulo: Abale opatsidwa gawoli ayenera kusankha mavesi apadera amene angagwiritsiridwe ntchito mothandiza kuti apindulitse mpingo. Zimenezi zimafuna kuti aŵerenge machaputala ake, kusinkhasinkhapo, ndi kufufuza pamavesi osankhidwa kuti apeze mfundo zimene zidzafotokoza tanthauzo la malemba amenewo. Kumapeto kwa Watch Tower Publications Index, kuli “Scripture Index,” imene ingakhale yothandiza popeza chidziŵitso cha mavesi ena a Baibulo. Abale osamalira mbali imeneyi ayenera kusonyeza luntha ndi kupeŵa kuloŵetsa nkhani zina zosafunika. Sayenera kukonza mfundo zochuluka kuposa zimene angafotokoze m’mphindi zisanu ndi imodzi.
5 Ife tonse tingapindule ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Ingatithandize kuwongolera kalankhulidwe kathu ndi luso la kuphunzitsa. Kugwiritsira ntchito mwaŵi wonse wa makonzedwe ameneŵa kudzatithandizadi kuchititsa ‘kupita kwathu patsogolo kuonekera kwa anthu onse.’—1 Tim. 4:15, NW.