Misonkhano Yautumiki ya February
Mlungu Woyambira February 5
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Mbiri Yateokrase.
Mph. 15: “Kulengeza Choonadi Tsiku ndi Tsiku Motsanzira Yesu.” Mafunso ndi mayankho. Fotokozani mwachidule za lipoti la utumiki la Malaŵi. Omvetsera athirire ndemanga pa avareji ya maola—Kodi ikupereka lingaliro lakuti tikulengeza choonadi tsiku ndi tsiku? Perekani chilimbikitso choyenera. Ŵerengani ndime 5.
Mph. 20: “Kupeza Mfungulo ya Chimwemwe cha Banja.” Fotokozani maulaliki osonyezedwawo, ndipo sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri.
Nyimbo Na. 14 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 12
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Lengezani za makonzedwe apadera a utumiki wakumunda a kutha kwa mlungu.
Mph. 13: “Konzekerani Ntchito ya Sabusikripishoni mu April.” Fotokozani kufunika kwa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! podziŵikitsa uthenga wabwino. Ŵerengani nkhani ya ndime ziŵiriyo, ndi kulongosola zimene mpingo wanu udzachita kuti upangitse April kukhala mwezi wapadera wa kugaŵira masabusikripishoni.
Mph. 22: “Kodi ndi Motani Mmene Ndingapezere Khutu Lomvetsera?” Mafunso ndi mayankho. Itanani ofalitsa aŵiri kuti adzakambitsirane mmene adzayesera kusonyeza kutentha polankhula pamakomo, akumagwiritsira ntchito malingaliro ena operekedwa mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, masamba 165-7, ndime 10-21.
Nyimbo Na. 133 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 19
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 15: “Pindulani ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996—Mbali 2.” Nkhani yoperekedwa ndi woyang’anira sukulu. Gogomezerani kufunika kwa kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku.
Mph. 20: “Thandizani Mwachikondi Awo Amene Amasonyeza Chikondwerero.” Fotokozani maulaliki a maulendo obwereza osonyezedwa. Mkulu akambitsirana ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu za mbali zina za buku la Moyo wa Banja ndi mmene zimenezi zingasonyezedwere. Sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri. Perekani malingaliro ena onena za mmene tingakulitsire chidwi kufikira pa kuyambitsa phunziro m’buku la Knowledge That Leads to Everlasting Life.
Nyimbo Na. 53 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 26
Mph.10: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 15: Kukonzekera Maulaliki Okopa. Woyang’anira utumiki kapena mkulu wina akambitsirana ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu za mapindu a kukhala ndi maulaliki a kukhomo ndi khomo amene akusonyeza kanthu kena kamene kali kokopa kumaloko. Mwachitsanzo, nkhani zakumaloko zonena za kuyesayesa kuwongolera kakhalidwe; kuwonjezereka kwa mavuto a m’banja, ana opulupudza, kapena kusoŵa kwa ntchito; kapena nkhani zimene zikusonyeza chifukwa chake anthu akukhala okayikira mowonjezereka ponena za njira zothetsera mavuto za andale ndi atsogoleri achipembedzo. Tchulani nkhani zina zaposachedwapa zochitika kwanuko, ndipo kambitsiranani mmene zingagwiritsiridwire ntchito kuyambitsira makambitsirano.
Mph. 20: Kugaŵira Buku la Knowledge That Leads to Everlasting Life m’March. Sonyezani mbali zina zokondweretsa za bukulo zimene zingagwiritsidwe ntchito kuyambitsira makambitsirano. (1) Sonyezani zithunzithunzi zochititsa chidwi, monga zimene zasonyezedwa pamasamba 4-5, 86, 124-5, 188-9. (2) Sonyezani mmene mutu uliwonse umathera ndi mpambo wa mafunso openda, ndipo fotokozani mmene ameneŵa angagwiritsiridwe ntchito monga maziko a maulaliki. Mwini nyumba angafunsidwe ngati angafune kudziŵa mayankho ake. Sankhani mafunso ena a pampambo wa pamasamba 11, 22, 61, 149. (3) Tsegulani pa bokosi la patsamba 102, ndipo perekani njira zosonyeza mmene mawu akuti “Some Feature of the Last Days” angagwiritsiridwe ntchito kusonkhezera chidwi. (4) Gogomezerani za mmene bukulo lilili lokonzedwa mwapadera kaamba ka kuchititsira maphunziro opita patsogolo. Mitu yake njaifupi, nkhani zake nzosavuta kuzimva, malemba osonyeza mfundo zamphamvu aikidwamo, ndipo mafunso ofufuza mtima amasumika maganizo pa mfundo zazikulu. Limbikitsani onse kugaŵira bukulo ndi chonulirapo chakuyambitsa maphunziro.
Nyimbo Na. 151 ndi pemphero lomaliza.