Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/96 tsamba 3
  • Kodi ndi Motani Mmene Ndingapezere Khutu Lomvetsera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi ndi Motani Mmene Ndingapezere Khutu Lomvetsera?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Luso Lomvetsera Ena Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Lidiya—Wopembedza Mulungu Ndiponso Wochereza Alendo
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Chitsanzo Chabwino—Lidiya
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Khalani Mmvetseri Wabwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 2/96 tsamba 3

Kodi ndi Motani Mmene Ndingapezere Khutu Lomvetsera?

1 M’mzinda wa Filipi, “mkazi wina dzina lake Lidiya, wakugulitsa chibakuwa, . . . mtima wake Ambuye anatsegula, kuti amvere zimene anazinena Paulo.” (Mac. 16:14) Kodi nkhaniyi imatiphunzitsanji? Kumvetsera nkumene kumatsegulira munthu njira ya kuphunzira choonadi. Chipambano chathu pa kufalitsa uthenga wa Ufumu kwakukulukulu chimadalira pa kufunitsitsa kwa mwini nyumba kuti amvetsere. Pamene tipeza khutu lomvetsera, nkosavuta kupereka uthenga wathu. Koma kuchititsa munthu kuti amvetsere kungakhale kovuta. Kodi tingachitenji?

2 Tisanapite mu utumiki, tiyenera kudziona mmene tikuonekera ndi mmene ziŵiya zimene tidzagwiritsira ntchito zikuonekera. Chifukwa ninji? Anthu amakonda kumvetsera kwa amene akuoneka mwaulemu. Kodi tavala bwino ndi mwaulemu? Ngakhale kuti kuvala mosasamala nkofala ku dziko, ife timapeŵa kusasamala kumeneko chifukwa chakuti ndife atumiki oimira Ufumu wa Mulungu. Maonekedwe athu oyera ndi audongo amawonjezera umboni wabwino wa uthenga wa Ufumu umene timalalikira.

3 Khalani Waubwenzi ndi Waulemu: Mosasamala kanthu za kusintha kwa malingaliro kwa masiku ano, anthu ambiri amachitira ulemu Baibulo ndipo amamvetsera mokondwera makambitsirano aulemu ndi aubwenzi a zimene Baibulo limanena. Kumwetulira kwachikondi, ndi kochokera pansi pamtima kungachititse mwini nyumba kumasuka ndi kutsegula njira ya makambitsirano okondweretsa. Kuona mtima kwathu ndi makhalidwe athu abwino ziyeneranso kuonekera m’malankhulidwe athu ndi kakhalidwe, zimene zimaphatikizapo kutchera kwathu khutu mwaulemu ku ndemanga za mwini nyumba.

4 Chifuno chathu ndicho cha kugaŵana ndi ena chiyembekezo cha m’Baibulo. Pomakumbukira zimenezi, tiyenera kutsimikizira kuti makambitsirano athu ngokopa, osati audani kapena otsutsa. Palibe chifukwa chotayira nthaŵi kutsutsana ndi munthu amene akuonekeratu kuti ngwotsutsa. (2 Tim. 2:23-25) Tingasankhepo umodzi wa maulaliki ambiri olimbikitsa ndi apanthaŵi yake operekedwa kwa ife mu Utumiki Wathu Waufumu ndi m’buku la Kukambitsirana. Komabe, tiyenera kuwakonzekera bwino kotero kuti tilankhule mogwira mtima ndi chikhutiro.—1 Pet. 3:15.

5 Ndi eni nyumba ochepa amene amakumbukira bwinobwino zimene tanena pambuyo pa ulendo wathu woyamba. Komabe, mwachionekere onse amakumbukira njira mmene tinalankhulira. Tisachepetse konse mphamvu ya ubwino ndi chifundo. Ndithudi, m’gawo lathu muli anthu ambiri onga nkhosa amene adzatchera khutu ku choonadi monga mmene Lidiya anachitira m’zaka za zana loyamba. Kupereka chisamaliro chapadera ku maonekedwe athu ndi malankhulidwe athu kungalimbikitse anthu oona mtima kumvetsera Mawu a Mulungu ndi kuwalandira moyanja.—Marko 4:20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena