Konzekerani Ntchito ya Kugaŵira Sabusikripishoni mu April
Monga momwe taonera mu Kalenda yathu ya 1996, Mgonero wa Ambuye chaka chino udzachitidwa pa April 2. Pokhala olimbikitsidwa ndi chochitika chapadera chimenechi, aliyense adzakhaletu ndi phande mwachangu m’kugaŵira sabusikripishoni mu April yense. Tidzakhala tikugaŵira magazini apanthaŵi yake abwino chotani nanga! Nsanja ya Olonda ya April 1 idzasimba za nkhani yapoyera ya msonkhano wachigawo wa chaka chatha yakuti, “Tamandani Mfumu Yamuyaya!” Nsanja ya Olonda ya April 15 idzakhala ndi mutu wankhani yapoyera yapadera ya April wapita wakuti “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ayandikira.” Nkhani yapadera ya chaka chino pa April 21 yakuti, “Kukhala Opanda Banga Pakati pa Mbadwo Wokhotakhota,” idzatisonkhezera mowonjezereka. Tidzagaŵira Galamukani! wa May 8 wa mutu wakuti “Pamene Sikudzakhalanso Nkhondo.”
Monga chinthu chotsatira pa mkupiti wa Uthenga wa Ufumu wa April wathayo, April yemwe akubwerayo ayenera kukhala mwezi wapadera wa kugaŵira sabusikripishoni. Inoyo ndiyo nthaŵi ya kupanga makonzedwe. Ambiri adzafuna kulembetsa kukhala apainiya othandiza. Makope apadera ofunika kaamba ka magazini a April ayenera kuodedwa. Makonzedwe a Masiku a Magazini angapangidwe, aliyense akumatengamo mbali ngati kuli kotheka—mmaŵa, masana, ndi/kapena madzulo. Tiyeni tonsefe ‘tikhale akuchita mawu.’ Monga momwe kunanenedweratu ponena za Mesiya pa Salmo 69:9, nafenso tikhozetu kunena kuti: “Changu cha pa nyumba yanu chandidya ine.”—Yak. 1:22; Yoh. 2:17.